< 耶利米書 4 >

1 耶和華說:以色列啊, 你若回來歸向我, 若從我眼前除掉你可憎的偶像, 你就不被遷移。
“Ngati mukufuna kubwerera, inu Aisraeli, bwererani kwa Ine,” akutero Yehova. “Chotsani mafano anu onyansa pamaso panga ndipo musasocherenso.
2 你必憑誠實、公平、公義, 指着永生的耶和華起誓; 列國必因耶和華稱自己為有福, 也必因他誇耀。
Muzilumbira mokhulupirika ndiponso mwa chilungamo kuti, ‘Pali Yehova wamoyo.’ Mukatero anthu a mitundu ina yonse adzandipempha kuti ndiwadalitse ndipo adzanditamanda.”
3 耶和華對猶大和耶路撒冷人如此說: 要開墾你們的荒地, 不要撒種在荊棘中。
Zimene Yehova akunena kwa anthu a ku Yuda ndi a ku Yerusalemu ndi izi: “Limani masala anu musadzale pakati pa minga.
4 猶大人和耶路撒冷的居民哪, 你們當自行割禮,歸耶和華, 將心裏的污穢除掉; 恐怕我的忿怒因你們的惡行發作, 如火着起, 甚至無人能以熄滅!
Dziperekeni nokha kwa Ine kuti munditumikire ndi mtima wanu wonse, inu anthu a ku Yuda ndi ku Yerusalemu. Muzichita zimenezi kuopa kuti mkwiyo wanga ungabuke ngati moto ndi kukutenthani, chifukwa cha ntchito zanu zoyipazo popanda wina wowuzimitsa.
5 你們當傳揚在猶大, 宣告在耶路撒冷說: 你們當在國中吹角,高聲呼叫說: 你們當聚集! 我們好進入堅固城!
“Lengeza ku Yuda ndi kulalikira mu Yerusalemu kuti, ‘Lizani lipenga mʼdziko lonse!’ Ndipo fuwulani kuti, ‘Sonkhanani! Tiyeni tithawire ku mizinda yotetezedwa!’
6 應當向錫安豎立大旗。 要逃避,不要遲延, 因我必使災禍與大毀滅從北方來到。
Kwezani mbendera kuyangʼana ku Ziyoni! Musachedwe, thawani kuti mupulumuke! Pakuti Ine ndikubweretsa chilango kuchokera kumpoto, kudzakhala chiwonongeko choopsa.”
7 有獅子從密林中上來, 是毀壞列國的。 牠已經動身出離本處, 要使你的地荒涼, 使你的城邑變為荒場無人居住。
Monga mkango umatulukira mʼngaka yake momwemonso wowononga mayiko wanyamuka ndi kutuluka ku mbuto yake. Watero kuti awononge dziko lanu. Mizinda yanu idzakhala mabwinja popanda wokhalamo.
8 因此,你們當腰束麻布,大聲哀號, 因為耶和華的烈怒沒有向我們轉消。
Choncho valani ziguduli, lirani ndi kubuwula, pakuti mkwiyo waukulu wa Yehova sunatichokere.
9 耶和華說:「到那時,君王和首領的心都要消滅;祭司都要驚奇,先知都要詫異。」
“Pa tsiku limenelo, mfumu ndi nduna zake adzataya mtima, ansembe adzachita mantha kwambiri, ndipo aneneri adzathedwa nzeru,” akutero Yehova.
10 我說:「哀哉!主耶和華啊,你真是大大地欺哄這百姓和耶路撒冷,說:『你們必得平安。』其實刀劍害及性命了。」
Ndipo ine ndinati, “Haa, Ambuye Yehova, ndithu munawanyenga anthu awa pamodzi ndi Yerusalemu pamene munanena kuti, ‘Mudzakhala pa mtendere,’ chonsecho lupanga lili pakhosi pathu.”
11 那時,必有話對這百姓和耶路撒冷說:「有一陣熱風從曠野淨光的高處向我的眾民颳來,不是為簸揚,也不是為揚淨。
Nthawi imeneyo anthu awa ndi Yerusalemu adzawawuza kuti, “Mphepo yotentha yochokera ku magomo a mʼchipululu ikuwomba pa anthu anga, osati mphepo yopeta kapena yoyeretsa;
12 必有一陣更大的風從這些地方為我颳來;現在我又必發出判語,攻擊他們。」
koma mphepo yamphamvu kwambiri yochokera kwa Ine. Tsono ndi Ineyo amene ndikuwaweruza.”
13 看哪,仇敵必如雲上來; 他的戰車如旋風, 他的馬匹比鷹更快。 我們有禍了! 我們敗落了!
Taonani, adani akubwera ngati mitambo, magaleta awo akubwera ngati kamvuluvulu, akavalo awo ndi aliwiro kupambana chiwombankhanga. Tsoka ilo! Tawonongeka!
14 耶路撒冷啊,你當洗去心中的惡, 使你可以得救。 惡念存在你心裏要到幾時呢?
Iwe Yerusalemu, tsuka mtima wako kuchotsa zoyipa kuti upulumuke. Kodi maganizo ako oyipawo udzakhala nawo mpaka liti?
15 有聲音從但傳揚, 從以法蓮山報禍患。
Pakuti amithenga akulalika mawu mʼdziko la Dani; akulengeza za masautso kuchokera ku mapiri a Efereimu.
16 你們當傳給列國, 報告攻擊耶路撒冷的事說: 有探望的人從遠方來到, 向猶大的城邑大聲吶喊。
Iwo akuti, “Fotokozani zimenezi kwa anthu a mitundu ina, lengezani zimenezi mu Yerusalemu kuti, ‘Ankhondo akubwera kuchokera ku dziko lakutali, akufuwula ndi kudzazinga mizinda ya Yuda.
17 他們周圍攻擊耶路撒冷, 好像看守田園的, 因為她背叛了我。 這是耶和華說的。
Azinga Yerusalemu ngati anthu olondera munda, chifukwa Yerusalemu wandiwukira,’” akutero Yehova.
18 你的行動,你的作為,招惹這事; 這是你罪惡的結果, 實在是苦, 是害及你心了!
“Makhalidwe anu ndi zochita zanu zakubweretserani zimenezi. Chimenechi ndiye chilango chanu. Nʼchowawa kwambiri! Nʼcholasa mpaka mu mtima!”
19 我的肺腑啊,我的肺腑啊,我心疼痛! 我心在我裏面煩躁不安。 我不能靜默不言, 因為我已經聽見角聲和打仗的喊聲。
Mayo, mayo, ndikumva kupweteka! Aa, mtima wanga ukupweteka, ukugunda kuti thi, thi, thi. Sindingathe kukhala chete. Pakuti ndamva kulira kwa lipenga; ndamva mfuwu wankhondo.
20 毀壞的信息連絡不絕, 因為全地荒廢。 我的帳棚忽然毀壞; 我的幔子頃刻破裂。
Tsoka limatsata tsoka linzake; dziko lonse lasanduka bwinja. Mwadzidzidzi matenti athu awonongedwa, mwa kanthawi kochepa nsalu zake zotchinga zagwetsedwa.
21 我看見大旗,聽見角聲, 要到幾時呢?
Kodi ndikhale ndikuona mbendera ya nkhondo, ndi kumva kulira kwa lipenga mpaka liti?
22 耶和華說:我的百姓愚頑,不認識我; 他們是愚昧無知的兒女, 有智慧行惡,沒有知識行善。
Yehova akuti, “Anthu anga ndi zitsiru; iwo sandidziwa. Iwo ndi ana opanda nzeru; samvetsa chilichonse. Ali ndi luso lochita zoyipa, koma sadziwa kuchita zabwino.”
23 先知說:我觀看地, 不料,地是空虛混沌; 我觀看天,天也無光。
Ndinayangʼana dziko lapansi, ndipo linali lopanda anthu ndi lopanda kanthu; ndinayangʼana thambo, koma linalibe kuwala kulikonse.
24 我觀看大山,不料,盡都震動, 小山也都搖來搖去。
Ndinayangʼana mapiri, ndipo ankagwedezeka; magomo onse ankangosunthira uku ndi uku.
25 我觀看,不料,無人; 空中的飛鳥也都躲避。
Ndinayangʼana, ndipo sindinaone anthu; mbalame iliyonse ya mlengalenga inali itathawa.
26 我觀看,不料,肥田變為荒地; 一切城邑在耶和華面前, 因他的烈怒都被拆毀。
Ndinayangʼana, dziko lachonde linali litasanduka chipululu; mizinda yake yonse inali itasanduka bwinja pamaso pa Yehova, chifukwa cha mkwiyo wake.
27 耶和華如此說:全地必然荒涼, 我卻不毀滅淨盡。
Yehova akuti, “Dziko lonse lidzasanduka chipululu komabe sindidzaliwononga kotheratu.
28 因此,地要悲哀, 在上的天也必黑暗; 因為我言已出,我意已定, 必不後悔,也不轉意不做。
Chifukwa chake dziko lapansi lidzalira ndipo thambo lidzachita mdima, pakuti ndayankhula ndipo sindidzafewa mtima, ndatsimikiza ndipo sindidzabwerera mʼmbuyo.”
29 各城的人因馬兵和弓箭手的響聲就都逃跑, 進入密林,爬上磐石; 各城被撇下, 無人住在其中。
Pakumva phokoso la okwera pa akavalo ndi la anthu oponya mivi, anthu a mʼmizinda adzathawa. Ena adzabisala ku nkhalango; ena adzakwera mʼmatanthwe mizinda yonse nʼkuyisiya; popanda munthu wokhalamo.
30 你淒涼的時候要怎樣行呢? 你雖穿上朱紅衣服, 佩戴黃金裝飾, 用顏料修飾眼目, 這樣標緻是枉然的! 戀愛你的藐視你, 並且尋索你的性命。
Iwe Yerusalemu, ndiwe bwinja! Ukutanthauza chiyani kuvala zovala zofiira ndi kuvalanso zokometsera zagolide? Ngakhale udzikonze maso ako powapaka zokometsera, ukungodzivuta chabe. Zibwenzi zako zikukunyoza; zikufuna kuchotsa moyo wako.
31 我聽見有聲音,彷彿婦人產難的聲音, 好像生頭胎疼痛的聲音, 是錫安女子的聲音; 她喘着氣、挓挲手, 說:我有禍了! 在殺人的跟前,我的心發昏了。
Ndikumva kulira ngati kwa mayi pa nthawi yake yobereka, kubuwula ngati kwa mayi amene akubereka mwana wake woyamba. Kuliraku ndi kwa anthu a mu Ziyoni, wefuwefu. Atambalitsa manja awo nʼkumati, “Kalanga ife! Tikukomoka. Moyo wathu waperekedwa kwa anthu otipha.”

< 耶利米書 4 >