< 以賽亞書 33 >

1 禍哉!你這毀滅人的, 自己倒不被毀滅; 行事詭詐的, 人倒不以詭詐待你。 你毀滅罷休了, 自己必被毀滅; 你行完了詭詐, 人必以詭詐待你。
Tsoka kwa iwe, iwe wowonongawe, amene sunawonongedwepo! Tsoka kwa iwe, iwe mthirakuwiri, iwe amene sunanyengedwepo! Iwe ukadzaleka kuwononga, udzawonongedwa, ukadzasiya umʼthirakuwiri, adzakuwononga, ndipo ukadzaleka kuchita zachinyengo adzakunyenga.
2 耶和華啊,求你施恩於我們; 我們等候你。 求你每早晨作我們的膀臂, 遭難的時候為我們的拯救。
Inu Yehova, mutikomere mtima ife; tikulakalaka Inu. Tsiku ndi tsiku mutitchinjirize ndi mkono wanu, ndipo mutipulumutse pa nthawi ya masautso.
3 喧嚷的響聲一發,眾民奔逃; 你一興起,列國四散。
Mukatulutsa liwu lanu longa bingu mitundu ya anthu imathawa; pamene Inu mwadzambatuka mitundu ya anthu imabalalika.
4 你們所擄的必被斂盡, 好像螞蚱吃盡禾稼。 人要蹦在其上,好像蝗蟲一樣。
Zofunkha za ku nkhondo za mitundu ina Aisraeli adzazisonkhanitsa ngati mmene limachitira dzombe. Iwo adzalumphira zofunkhazo monga mmene limachitira dzombe.
5 耶和華被尊崇,因他居在高處; 他以公平公義充滿錫安。
Yehova wakwezeka kwambiri pakuti amakhala pamwamba pa zonse adzadzaza Ziyoni ndi chilungamo ndi chipulumutso.
6 你一生一世必得安穩- 有豐盛的救恩, 並智慧和知識; 你以敬畏耶和華為至寶。
Iye adzakupatsani mtendere pa nthawi yanu, adzakupatsani chipulumutso chochuluka, nzeru zambiri ndi chidziwitso chochuluka; kuopa Yehova ngati madalitso.
7 看哪,他們的豪傑在外頭哀號; 求和的使臣痛痛哭泣。
Taonani, anthu awo amphamvu akulira mofuwula mʼmisewu; akazembe okhazikitsa mtendere akulira kwambiri.
8 大路荒涼,行人止息; 敵人背約, 藐視城邑, 不顧人民。
Mʼmisewu yayikulu mulibe anthu, mʼmisewu mulibe anthu a paulendo. Mdaniyo ndi wosasunga pangano. Iye amanyoza mboni. Palibe kulemekezana.
9 地上悲哀衰殘; 黎巴嫩羞愧枯乾; 沙崙像曠野; 巴珊和迦密的樹林凋殘。
Dziko likulira ndipo likunka likutha. Nkhalango ya Lebanoni ikuchita manyazi, yafota. Chigwa cha chonde cha Saroni chasanduka chachidalala. Masamba a mitengo ya ku Basani ndi Karimeli akuyoyoka.
10 耶和華說: 現在我要起來; 我要興起; 我要勃然而興。
Yehova akunena kuti, “Tsopano ndidzadzambatuka ndipo ndidzaonetsa mphamvu zanga, ndipo ndidzakwezedwa.
11 你們要懷的是糠詷, 要生的是碎稭; 你們的氣就是吞滅自己的火。
Zolingalira zanu nʼzachabechabe ngati udzu wamanyowa. Mpweya wamoto udzakupserezani.
12 列邦必像已燒的石灰, 像已割的荊棘在火中焚燒。
Anthu a mitundu ina adzatenthedwa ngati miyala ya njereza; ndi ngati minga yodulidwa.”
13 你們遠方的人當聽我所行的; 你們近處的人當承認我的大能。
Inu amene muli kutali, imvani zimene ndachita; inu amene muli pafupi, dziwani mphamvu zanga
14 錫安中的罪人都懼怕; 不敬虔的人被戰兢抓住。 我們中間誰能與吞滅的火同住? 我們中間誰能與永火同住呢?
Mu mzinda wa Ziyoni anthu ochimwa agwidwa ndi mantha; anthu osapembedza Mulungu akunjenjemera: Iwo akunena kuti, “Ndani wa ife angathe kukhala mʼmoto wonyeketsa? Ndani wa ife angathe kukhala moto wosatha?”
15 行事公義、說話正直、 憎惡欺壓的財利、 擺手不受賄賂、 塞耳不聽流血的話, 閉眼不看邪惡事的,
Angathe kuti ndi amene amachita zolungama ndi kuyankhula zoona, amene amakana phindu lolipeza monyenga ndipo salola manja ake kulandira ziphuphu, amene amatseka makutu ake kuti angamve mawu opangana kupha anzawo ndipo amatsinzina kuti angaone zoyipa.
16 他必居高處; 他的保障是磐石的堅壘; 他的糧必不缺乏; 他的水必不斷絕。
Munthu wotere ndiye adzakhale pa nsanja, kothawira kwake kudzakhala mʼmalinga a mʼmapiri. Azidzalandira chakudya chake ndipo madzi sadzamusowa.
17 你的眼必見王的榮美, 必見遼闊之地。
Nthawi imeneyo maso a ana adzaona mfumu ya maonekedwe wokongola ndi kuona dziko lotambasukira kutali.
18 你的心必思想那驚嚇的事, 自問說:記數目的在哪裏呢? 平貢銀的在哪裏呢? 數戍樓的在哪裏呢?
Mu mtima mwanu muzidzalingalira zoopsa zinachitika kale zija: “Ali kuti mkulu wa Asilikali uja? Ali kuti wokhometsa misonkho uja? Ali kuti mkulu woyangʼanira nsanja?”
19 你必不見那強暴的民, 就是說話深奧,你不能明白, 言語呢喃,你不能懂得的。
Simudzawaonanso anthu odzikuza aja, anthu aja achiyankhulo chosadziwika, chachilendo ndi chosamveka.
20 你要看錫安-我們守聖節的城! 你的眼必見耶路撒冷為安靜的居所, 為不挪移的帳幕, 橛子永不拔出, 繩索一根也不折斷。
Taonani Ziyoni, mzinda wa zikondwerero zachipembedzo chathu; maso anu adzaona Yerusalemu, mzinda wamtendere, tenti imene sidzachotsedwa, zikhomo zake sizidzazulidwa, kapena zingwe zake kuduka.
21 在那裏,耶和華必顯威嚴與我們同在, 當作江河寬闊之地; 其中必沒有盪槳搖櫓的船來往, 也沒有威武的船經過。
Kumeneko Yehova adzaonetsa ulemerero wake ndipo mzindawo udzakhala kasupe wa mitsinje yayikulu. Ngalawa za zopalasa sizidzapitamo, sitima zapamadzi zikuluzikulu sizidzayendamo.
22 因為,耶和華是審判我們的; 耶和華是給我們設律法的; 耶和華是我們的王; 他必拯救我們。
Pakuti Yehova ndi woweruza wathu, Yehova ndiye wotilamulira, Yehova ndiye mfumu yathu; ndipo ndiye amene adzatipulumutse.
23 你的繩索鬆開: 不能栽穩桅杆, 也不能揚起篷來。 那時許多擄來的物被分了; 瘸腿的把掠物奪去了。
Zingwe za sitima zapamadzi za adani athu zamasuka, sizikutha kulimbitsa mlongoti wake, matanga ake sakutheka kutambasuka. Ngakhale tidzagawana zofunkha zochuluka kwambiri ndipo ngakhale olumala adzatenga zofunkhazo.
24 城內居民必不說:我病了; 其中居住的百姓,罪孽都赦免了。
Palibe ndi mmodzi yemwe wokhala mʼZiyoni adzanene kuti, “Ndikudwala” ndipo anthu onse okhala mʼmenemo machimo awo adzakhululukidwa.

< 以賽亞書 33 >