< 創世記 10 >
1 挪亞的兒子閃、含、雅弗的後代記在下面。洪水以後,他們都生了兒子。
Nayi mbiri ya ana a Nowa, Semu, Hamu ndi Yafeti. Ana atatuwa anabereka ana awo chitatha chigumula.
2 雅弗的兒子是歌篾、瑪各、瑪代、雅完、土巴、米設、提拉。
Ana aamuna a Yafeti anali: Gomeri, Magogi, Madai, Yavani, Tubala, Mesaki ndi Tirasi.
Ana aamuna a Gomeri anali: Asikenazi, Rifati ndi Togarima.
Ana aamuna a Yavani anali: Elisa, Tarisisi, Kitimu ndi Rodanimu.
5 這些人的後裔將各國的地土、海島分開居住,各隨各的方言、宗族立國。
(Amenewa ndiwo makolo a anthu okhala mʼmphepete mwa nyanja. Awa ndi ana a Yafeti monga mwa mafuko a mu mitundu yawo, uliwonse ndi chiyankhulo chake).
Ana aamuna a Hamu anali: Kusi, Miziraimu, Puti ndi Kanaani.
7 古實的兒子是西巴、哈腓拉、撒弗他、拉瑪、撒弗提迦。拉瑪的兒子是示巴、底但。
Ana aamuna a Kusi anali: Seba, Havila, Sabita, Raama ndi Sabiteka. Ana aamuna a Raama anali: Seba ndi Dedani.
Kusi anabereka Nimurodi amene anali wankhondo wamphamvu kwambiri pa dziko lapansi.
9 他在耶和華面前是個英勇的獵戶,所以俗語說:「像寧錄在耶和華面前是個英勇的獵戶。」
Iye anali mlenje wamphamvu kwambiri pamaso pa Yehova; nʼchifukwa chake anthu ali ndi chisudzo, chakuti, “Ndiwe mlenje wamphamvu kwambiri pamaso pa Yehova monga Nimurodi.”
10 他國的起頭是巴別、以力、亞甲、甲尼,都在示拿地。
Malo oyambirira a ufumu wake anali Babeli, Ereki, Akadi ndi Kaline. Malo onsewa anali mʼdziko la Sinara.
11 他從那地出來往亞述去,建造尼尼微、利河伯、迦拉,
Atachoka mʼdziko limeneli anapita ku Asiriya kumene anakamanga Ninive, Rehoboti-Iri, Kala,
ndi Reseni, mzinda waukulu umene uli pakati pa Ninive ndi Kala.
13 麥西生路低人、亞拿米人、利哈比人、拿弗土希人、
Igupto ndiye kholo la Aludi, Aanami, Alehabu, Anafutu,
14 帕斯魯細人、迦斯路希人、迦斐託人;從迦斐託出來的有非利士人。
Apaturusi, Akasilu ndi Akafitori (kumene kunachokera Afilisti).
Kanaani anabereka mwana wake wachisamba, Sidoni, ndipo anaberekanso Ahiti;
Ayebusi, Aamori, Agirigasi;
18 亞瓦底人、洗瑪利人、哈馬人,後來迦南的諸族分散了。
Aaravadi, Azemari ndi Ahamati. Pambuyo pake, mafuko a Akanaani anafalikira ponseponse,
19 迦南的境界是從西頓向基拉耳的路上,直到迦薩,又向所多瑪、蛾摩拉、押瑪、洗扁的路上,直到拉沙。
mpaka ku malire a Kanaani. Malirewo anachokera ku Sidoni kulowa cha ku Gerari mpaka ku Gaza, ndi kulowa ku Sodomu, Gomora, Adima ndi Zeboimu mpaka ku Lasa.
20 這就是含的後裔,各隨他們的宗族、方言,所住的地土、邦國。
Amenewa ndiwo ana aamuna a Hamu monga mwa mafuko ndi ziyankhulo zawo, mʼmadera omwe amakhala ndi mitundu yawo.
21 雅弗的哥哥閃,是希伯子孫之祖,他也生了兒子。
Semu amene anali mkulu wake wa Yafeti nayenso anabereka nakhala kholo la Eberi.
Ana aamuna a Semu anali: Elamu, Asuri, Aripakisadi, Ludi ndi Aramu.
Ana aamuna a Aramu anali: Uzi, Huri, Geteri ndi Mesaki.
Aripakisadi anabereka Sela, ndipo Selayo anabereka Eberi.
25 希伯生了兩個兒子,一個名叫法勒,因為那時人就分地居住;法勒的兄弟名叫約坍。
A Eberi anabereka ana aamuna awiri: Wina anamutcha Pelegi chifukwa pa nthawiyo anthu a pa dziko lapansi anagawikana. Dzina la mʼbale wake linali Yokitani.
Yokitani anabereka Alimodadi, Selefi, Hazari-Maveti, Yera,
Ofiri, Havila ndi Yobabu. Onsewa anali ana aamuna a Yokitani.
Chigawo chimene ankakhala chinayambira ku Mesa mpaka ku Seferi, ku dera la mapiri chakummawa.
31 這就是閃的子孫,各隨他們的宗族、方言,所住的地土、邦國。
Amenewa ndiwo ana a Semu monga mwa mafuko ndi ziyankhulo zawo, mʼmadera omwe ankakhala ndi mitundu yawo.
32 這些都是挪亞三個兒子的宗族,各隨他們的支派立國。洪水以後,他們在地上分為邦國。
Amenewa ndiwo mafuko a ana aamuna a Nowa monga mwa mibado ya mitundu yawo. Mitundu yonse ya anthu inatuluka mwa iwowa ndi kufalikira pa dziko lonse lapansi chitatha chigumula chija.