< 以西結書 38 >

1 耶和華的話臨到我說:
Yehova anandiyankhula kuti:
2 「人子啊,你要面向瑪各地的歌革,就是羅施、米設、土巴的王發預言攻擊他,
“Iwe mwana wa munthu, tembenukira kwa Gogi, wa ku dziko la Magogi, amene ali kalonga wamkulu wa mzinda wa Mesaki ndi Tubala. Umuyimbe mlandu.
3 說主耶和華如此說:羅施、米設、土巴的王歌革啊,我與你為敵。
Umuwuze mawu a Ine Ambuye Yehova akuti, ‘Ine ndikudana nawe, iwe Gogi, kalonga wamkulu wa ku Mesaki ndi Tubala.
4 我必用鉤子鉤住你的腮頰,調轉你,將你和你的軍兵、馬匹、馬兵帶出來,都披掛整齊,成了大隊,有大小盾牌,各拿刀劍。
Ndidzakuzunguza, ndidzakukola ndi mbedza mʼkamwa mwako. Ndidzakutulutsa iweyo pamodzi ndi gulu lako lonse la nkhondo, akavalo ako ndi okwerapo ake. Onse adzakhala atanyamula zida za nkhondo, zishango ndi malihawo ndipo malupanga awo adzakhala osolola.
5 波斯人、古實人,和弗人,各拿盾牌,頭上戴盔;
Pamodzi ndi iwowo, padzakhalanso ankhondo a ku Perisiya, ku Kusi, ndi ku Puti. Onsewa adzakhala atanyamula zishango ndi kuvala zipewa zankhondo.
6 歌篾人和他的軍隊,北方極處的陀迦瑪族和他的軍隊,這許多國的民都同着你。
Padzakhalanso Gomeri pamodzi ndi ankhondo ake onse ndiponso banja la Togarima ndi gulu lake lonse lankhondo lochokera kutali kumpoto. Padzakhaladi mitundu yambiri ya anthu pamodzi ndi iwe.
7 「那聚集到你這裏的各隊都當準備;你自己也要準備,作他們的大帥。
“‘Konzekani! Mukhaledi okonzeka, iweyo pamodzi ndi gulu lonse la nkhondo limene lakusonkhanira. Iweyo udzawatsogolera pokamenya nkhondo.
8 過了多日,你必被差派。到末後之年,你必來到脫離刀劍從列國收回之地,到以色列常久荒涼的山上;但那從列國中招聚出來的必在其上安然居住。
Pakapita masiku ambiri ndidzakuyitana. Zaka zikubwerazi ndidzakulowetsa mʼdziko limene lapulumuka ku nkhondo. Anthu ake anasonkhanitsidwa kuchokera ku mitundu ya anthu ambiri nʼkukakhazikika pa mapiri a Israeli amene kwa nthawi yayitali anali ngati chipululu. Anthu onsewa tsopano akukhala mwa mtendere.
9 你和你的軍隊,並同着你許多國的民,必如暴風上來,如密雲遮蓋地面。」
Tsono iwe pamodzi ndi ankhondo ako onse ndiponso mitundu yambiri ya anthu imene ili nawe mudzabwera ngati mphepo yamkuntho. Mudzaphimba dziko lonse ngati mitambo.
10 主耶和華如此說:「到那時,你心必起意念,圖謀惡計,
“Ine Ambuye Yehova ndikuti: Pa tsiku limenelo mu mtima mwako mudzabwera maganizo ofuna kukonzekera kuchita zoyipa.
11 說:『我要上那無城牆的鄉村,我要到那安靜的民那裏,他們都沒有城牆,無門、無閂,安然居住。
Iwe udzanena kuti, ‘Ndikukathira nkhondo dziko la midzi yopanda mipanda; ndikathira nkhondo anthu okhala mwamtendere, anthu amene satchinjirizidwa ndi mipanda, zipata kapena mipiringidzo.
12 我去要搶財為擄物,奪貨為掠物,反手攻擊那從前荒涼、現在有人居住之地,又攻擊那住世界中間、從列國招聚、得了牲畜財貨的民。』
Ndipita kukalanda chuma chawo ndi kukafunkha zinthu zawo. Ndidzalimbana ndi midzi imene kale inali mabwinja. Ndikathira nkhondo anthu amene anasonkhanitsidwa kuchokera kwa anthu a mitundu ina. Iwowa ali ndi ziweto zambiri, katundu wochuluka ndiponso amakhala pakatikati pa dziko lapansi.’
13 示巴人、底但人、他施的客商,和其間的少壯獅子都必問你說:『你來要搶財為擄物嗎?你聚集軍隊要奪貨為掠物嗎?要奪取金銀,擄去牲畜、財貨嗎?要搶奪許多財寶為擄物嗎?』
Anthu a ku Seba, a ku Dedani ndiponso amalonda a ku Tarisisi pamodzi ndi midzi yake yonse adzakufunsa kuti, ‘Kodi wabwera kudzafunkha? Kodi wasonkhanitsa gulu lako la nkhondo kudzalanda chuma, kudzatenga siliva ndi golide, ziweto ndi katundu kuti zikhale zofunkha zochuluka?’”
14 「人子啊,你要因此發預言,對歌革說,主耶和華如此說:到我民以色列安然居住之日,你豈不知道嗎?
“Nʼchifukwa chake, iwe mwana wa munthu, nenera ndipo uwuze Gogi kuti, ‘Ine Ambuye Yehova ndikuti: Pa nthawi imene anthu anga adzakhala pa mtendere, iwe udzanyamuka.
15 你必從本地,從北方的極處率領許多國的民來,都騎着馬,乃一大隊極多的軍兵。
Udzabwera kuchokera ku dziko lako kutali kumpoto, iwe pamodzi ndi mitundu yambiri ya anthu imene ili nawe, onse okwera akavalo, gulu lankhondo lalikulu ndi lamphamvu.
16 歌革啊,你必上來攻擊我的民以色列,如密雲遮蓋地面。末後的日子,我必帶你來攻擊我的地,到我在外邦人眼前,在你身上顯為聖的時候,好叫他們認識我。
Udzabwera kudzalimbana ndi anthu anga Aisraeli ngati mtambo wophimba dziko. Masiku amenewo, iwe Gogi, ndidzabwera nawe kuti ulimbane ndi dziko langa, kuti anthu a mitundu ina andidziwe Ine, pamene ndidzaonetsa kuyera kwanga pa zimene ndidzakuchite iweyo.
17 主耶和華如此說:我在古時藉我的僕人以色列的先知所說的,就是你嗎?當日他們多年預言我必帶你來攻擊以色列人。」
“‘Ine Ambuye Yehova ndikuti: Kodi iwe si amene ndinayankhula za iwe masiku amakedzana kudzera mwa atumiki anga aneneri a Israeli? Pa zaka zambiri iwo ankalengeza kuti ndidzawutsa iwe kuti udzalimbane ndi Israeli.
18 主耶和華說:「歌革上來攻擊以色列地的時候,我的怒氣要從鼻孔裏發出。
Zimene chidzachitika pa tsiku limenelo ndi izi: Gogi akadzathira nkhondo dziko la Israeli, mkwiyo wanga woopsa udzayaka. Ndikutero Ine Ambuye Wamphamvuzonse.
19 我發憤恨和烈怒如火說:那日在以色列地必有大震動,
Chifukwa cha mkwiyo ndi ukali wanga woyakawo Ine ndikunenetsa kuti pa nthawi imeneyo padzakhala chivomerezi chachikulu mʼdziko la Israeli.
20 甚至海中的魚、天空的鳥、田野的獸,並地上的一切昆蟲,和其上的眾人,因見我的面就都震動;山嶺必崩裂,陡巖必塌陷,牆垣都必坍倒。」
Nsomba za mʼnyanja, mbalame zamumlengalenga, zirombo zakuthengo, cholengedwa chilichonse chimene chimakwawa pansi, ndiponso anthu onse okhala pa dziko lapansi, adzanjenjemera pamaso panga. Mapiri adzangʼambika, malo okwera kwambiri adzagumuka ndipo khoma lililonse lidzagwa pansi.
21 主耶和華說:「我必命我的諸山發刀劍來攻擊歌革;人都要用刀劍殺害弟兄。
Ndidzawutsira Gogi nkhondo kuchokera ku mapiri anga. Ndikutero Ine Ambuye Yehova. Anthu a Gogiyo adzaphana okhaokha ndi malupanga.
22 我必用瘟疫和流血的事刑罰他。我也必將暴雨、大雹與火,並硫磺降與他和他的軍隊,並他所率領的眾民。
Ine ndidzamulanga ndi mliri ndi imfa. Ndidzagwetsa mvula yoopsa ya matalala, ndiponso sulufule ndi miyala ya moto pa iye ndi pa asilikali ake ndiponso pa mitundu yambiri ya anthu imene ili naye.
23 我必顯為大,顯為聖,在多國人的眼前顯現;他們就知道我是耶和華。」
Motero ndidzadzionetsa kuti ndine wamphamvu ndi woyera. Ndiponso ndidzadziwika pamaso pa anthu a mitundu ina yambiri. Momwemo adzadziwadi kuti Ine ndine Yehova.’”

< 以西結書 38 >