< 歷代志下 3 >

1 所羅門就在耶路撒冷、耶和華向他父大衛顯現的摩利亞山上,就是耶布斯人阿珥楠的禾場上、大衛所指定的地方預備好了,開工建造耶和華的殿。
Pamenepo Solomoni anayamba kumanga Nyumba ya Yehova mu Yerusalemu pa Phiri la Moriya, pamene Yehova anaonekera Davide abambo ake. Panali pabwalo lopunthirapo tirigu la Arauna Myebusi, malo amene anapereka Davide.
2 所羅門作王第四年二月初二日開工建造。
Iye anayamba kumanga pa tsiku lachiwiri la mwezi wachiwiri mʼchaka chachinayi cha ulamuliro wake.
3 所羅門建築上帝殿的根基,乃是這樣:長六十肘,寬二十肘,都按着古時的尺寸。
Maziko amene Solomoni anayika pomanga Nyumba ya Mulungu ndi awa: Mulitali munali mamita 27, mulifupi munali mamita asanu ndi anayi (potsata miyeso yakale).
4 殿前的廊子長二十肘,與殿的寬窄一樣,高一百二十肘;裏面貼上精金。
Chipinda cha polowera mulitali mwake chinali mamita asanu ndi anayi ofanana ndi mulifupi mwake mwa nyumbayo. Msinkhu wake unali mamita 54. Iye anakuta nyumbayo mʼkati mwake ndi golide woyengeka bwino.
5 大殿的牆都用松木板遮蔽,又貼了精金,上面雕刻棕樹和鍊子;
Chipinda chachikulu, khoma lake anakhomera matabwa a payini ndipo analikutira ndi golide wabwino ndi kulikongoletsa ndi zithunzi za kanjedza ndi maunyolo.
6 又用寶石裝飾殿牆,使殿華美;所用的金子都是巴瓦音的金子。
Iye anakongoletsa Nyumba ya Mulunguyo ndi miyala yokongola. Ndipo golide amene anagwiritsa ntchito anali golide wa ku Paravaimu.
7 又用金子貼殿和殿的棟樑、門檻、牆壁、門扇;牆上雕刻基路伯。
Iye anakutira ndi golide mitanda ya ku denga, maferemu a zitseko, makoma ndi zitseko za Nyumba ya Mulungu, ndipo anajambula Akerubi mʼmakoma mwake.
8 又建造至聖所,長二十肘,與殿的寬窄一樣,寬也是二十肘;貼上精金,共用金子六百他連得。
Iye anamanga Malo Opatulika Kwambiri ndipo mulitali mwake munali mofanana ndi mulifupi mwa Nyumba mamita asanu ndi anayi. Anakuta mʼkati mwake ndi golide wosalala wolemera matani makumi awiri.
9 金釘重五十舍客勒。樓房都貼上金子。
Misomali yagolide imalemera magalamu 570. Anakutanso ndi golide zipinda zapamwamba.
10 在至聖所按造像的法子造兩個基路伯,用金子包裹。
Ku Malo Opatulika Kwambiri iye anapangako Akerubi awiri achitsulo ndipo anawakuta ndi golide.
11 兩個基路伯的翅膀共長二十肘。這基路伯的一個翅膀長五肘,挨着殿這邊的牆;那一個翅膀也長五肘,與那基路伯翅膀相接。
Kutalika kwa mapiko onse a Akerubi kunali mamita asanu ndi anayi. Phiko la Kerubi woyamba linali loposerapo mamita awiri ndipo limakhudza khoma la Nyumba ya Mulungu, pamene phiko linalo, lotalikanso koposerapo mamita awiri, limakhudza phiko la Kerubi winayo.
12 那基路伯的一個翅膀長五肘,挨着殿那邊的牆;那一個翅膀也長五肘,與這基路伯的翅膀相接。
Chimodzimodzinso phiko la Kerubi wachiwiri linali loposerapo mamita awiri ndipo limakhudza mbali ina ya khoma la Nyumba ya Mulungu, ndipo linalo limene linalinso loposera mamita awiri, limakhudza phiko la Kerubi woyamba uja.
13 兩個基路伯張開翅膀,共長二十肘,面向外殿而立。
Mapiko a Akerubiwa akawatambasula amatalika mamita asanu ndi anayi. Akerubiwa anayimirira pa mapazi awo, kuyangʼana chipinda chachikulu.
14 又用藍色、紫色、朱紅色線和細麻織幔子,在其上繡出基路伯來。
Solomoni anapanga nsalu zotchingira zobiriwira, zapepo ndi zofiira ndi nsalu zofewa zosalala, atajambulapo Akerubi.
15 在殿前造了兩根柱子,高三十五肘;每柱頂高五肘。
Kutsogolo kwa Nyumba ya Mulungu anamangako zipilala ziwiri, zimene zonse pamodzi zinali zotalika mamita khumi ndi asanu ndi theka; chipilala chilichonse chinali ndi mutu woposera mamita awiri.
16 又照聖所內鍊子的樣式做鍊子,安在柱頂上;又做一百石榴,安在鍊子上。
Iye anapanga maunyolo olumikizanalumikizana ndipo anawayika pamwamba pa zipilalazo. Anapanganso makangadza 100 ndipo anawalumikiza ku maunyolo aja.
17 將兩根柱子立在殿前,一根在右邊,一根在左邊;右邊的起名叫雅斤,左邊的起名叫波阿斯。
Solomoni anayimika nsanamirazo kutsogolo kwa Nyumba ya Mulungu, imodzi mbali ya kummwera ndi inayo mbali ya kumpoto. Nsanamira ya kummwera anayitcha Yakini ndipo ya kumpoto anayitcha Bowazi.

< 歷代志下 3 >