< 撒母耳記上 27 >

1 大衛心裏說:「必有一日我死在掃羅手裏,不如逃奔非利士地去。掃羅見我不在以色列的境內,就必絕望,不再尋索我;這樣我可以脫離他的手。」
Davide anaganiza mu mtima mwake nati, “Tsiku lina ine ndidzaphedwa ndi Sauli. Palibe chabwino ndingachite, koma kuthawira ku dziko la Afilisti. Kotero Sauli adzasiya kundifunafuna mʼdziko lonse la Israeli, ndipo ndidzapulumuka.”
2 於是大衛起身,和跟隨他的六百人投奔迦特王-瑪俄的兒子亞吉去了。
Choncho Davide ndi anthu 600 amene anali nawo anachoka napita kwa Akisi mwana wa Maoki mfumu ya ku Gati.
3 大衛和他的兩個妻,就是耶斯列人亞希暖和作過拿八妻的迦密人亞比該,並跟隨他的人,連各人的眷屬,都住在迦特的亞吉那裏。
Davide anakhala ndi Akisi ku Gati pamodzi ndi ankhondo ake, aliyense ndi banja lake. Davide ali ndi akazi ake awiri, Ahinoamu wa ku Yezireeli ndi Abigayeli wa ku Karimeli, mkazi wamasiye wa Nabala.
4 有人告訴掃羅說:「大衛逃到迦特。」掃羅就不再尋索他了。
Sauli anamva kuti Davide wathawira ku Gati, ndipo sanamufunefunenso.
5 大衛對亞吉說:「我若在你眼前蒙恩,求你在京外的城邑中賜我一個地方居住。僕人何必與王同住京都呢?」
Kenaka Davide anawuza Akisi kuti, “Ngati ndapeza kuyanja pamaso panu mundipatse malo dera limodzi la dziko lanu kuti ndizikhala kumeneko. Mtumiki wanu adzakhala mu mzinda waufumu chifukwa chiyani?”
6 當日亞吉將洗革拉賜給他,因此洗革拉屬猶大王,直到今日。
Choncho tsiku limenelo Akisi anamupatsa Zikilagi ndipo mzindawo wakhala wa mafumu a Yuda mpaka lero.
7 大衛在非利士地住了一年零四個月。
Davide anakhala mʼdziko la Afilisti kwa chaka chimodzi ndi miyezi inayi.
8 大衛和跟隨他的人上去,侵奪基述人、基色人、亞瑪力人之地。這幾族歷來住在那地,從書珥直到埃及。
Tsono Davide ndi anthu ake ankapita kukathira nkhondo Agesuri, Agirizi ndi Aamaleki. (Mitundu ya anthu imeneyi kuyambira kale inkakhala mʼdziko la pakati pa Suri ndi Igupto).
9 大衛擊殺那地的人,無論男女都沒有留下一個,又奪獲牛、羊、駱駝、驢,並衣服,回來見亞吉。
Davide ankati akathira nkhondo dera lina, sankasiya munthu wamoyo, mwamuna kapena mkazi, koma ankatenga nkhosa, ngʼombe, abulu, ngamira ndi zovala, pambuyo pake nʼkubwerera kwa Akisi.
10 亞吉說:「你們今日侵奪了甚麼地方呢?」大衛說:「侵奪了猶大的南方、耶拉篾的南方、基尼的南方。」
Akisi akafunsa kuti, “Kodi lero unapita kukathira nkhondo kuti?” Davide ankayankha kuti, “Ndinapita kukathira nkhondo kummwera kwa Yuda,” mwinanso ankanena kuti, “Ndinapita ku dziko la Ayerahimeeli” kapenanso ankanena kuti, “Ndinapita ku dziko la Akeni.”
11 無論男女,大衛沒有留下一個帶到迦特來。他說:「恐怕他們將我們的事告訴人,說大衛住在非利士地的時候常常這樣行。」
Davide sankasiya mwamuna kapena mkazi wamoyo kuti akafotokozere anthu a ku Gati zochitikazo kuopa kuti opulumukawo akhoza kudzanena kuti “Davide watichita zakutizakuti.” Tsono izi ndi zimene Davide ankachita pamene ankakhala mʼdziko la Afilisti.
12 亞吉信了大衛,心裏說:「大衛使本族以色列人憎惡他,所以他必永遠作我的僕人了。」
Akisi ankamukhulupirira Davide ndipo ankati mu mtima mwake, “Davide wadzisandutsa munthu woyipa kwambiri pakati pa anthu ake omwe, Aisraeli. Tsono adzakhala mtumiki wanga mpaka kalekale.”

< 撒母耳記上 27 >