< 列王紀上 4 >

1 所羅門作以色列眾人的王。
Ndipo Mfumu Solomoni inakhala mfumu ya Aisraeli onse.
2 他的臣子記在下面:撒督的兒子亞撒利雅作祭司,
Nduna zake zikuluzikulu zinali izi: Azariya mwana wa Zadoki anali wansembe;
3 示沙的兩個兒子以利何烈、亞希亞作書記,亞希律的兒子約沙法作史官,
Elihorefe ndi Ahiya, ana a Sisa, anali alembi; Yehosafati mwana wa Ahiludi, anali mlembi wa zochitika;
4 耶何耶大的兒子比拿雅作元帥,撒督和亞比亞他作祭司長,
Benaya mwana wa Yehoyada, anali mtsogoleri wa ankhondo; Zadoki ndi Abiatara, anali ansembe;
5 拿單的兒子亞撒利雅作眾吏長,王的朋友拿單的兒子撒布得作領袖,
Azariya mwana wa Natani, anali woyangʼanira nduna za mʼzigawo; Zabudi mwana wa Natani, anali wansembe ndi bwenzi la mfumu;
6 亞希煞作家宰,亞比大的兒子亞多尼蘭掌管服苦的人。
Ahisara, anali mkulu woyangʼanira nyumba ya mfumu; Adoniramu mwana wa Abida, anali mkulu woyangʼanira ntchito za thangata.
7 所羅門在以色列全地立了十二個官吏,使他們供給王和王家的食物,每年各人供給一月。
Solomoni analinso ndi abwanamkubwa khumi ndi awiri amene ankayangʼanira zigawo zonse za dziko la Israeli. Iwo ankapereka chakudya kwa mfumu ndiponso ku banja laufumu. Bwanamkubwa aliyense ankapereka chakudya mwezi umodzi pa chaka.
8 他們的名字記在下面:在以法蓮山地有便‧戶珥;
Mayina awo ndi awa: Beni-Huri, wa ku dziko la mapiri la Efereimu;
9 在瑪迦斯、沙賓、伯‧示麥、以倫‧伯‧哈南有便‧底甲;
Beni-Dekeri, woyangʼanira mizinda ya Makazi, Saalibimu, Beti-Semesi ndi Eloni Beti-Hanani;
10 在亞魯泊有便‧希悉,他管理梭哥和希弗全地;
Beni-Hesedi, woyangʼanira mizinda ya Aruboti (Soko ndi dziko lonse la Heferi);
11 在多珥山岡有便‧亞比拿達,他娶了所羅門的女兒她法為妻;
Beni-Abinadabu, woyangʼanira Nafoti Dori (iye anakwatira Tafati mwana wa Solomoni);
12 在他納和米吉多,並靠近撒拉他拿、耶斯列下邊的伯‧善全地,從伯‧善到亞伯‧米何拉直到約念之外,有亞希律的兒子巴拿;
Baana mwana wa Ahiludi, anali woyangʼanira Taanaki ndi Megido, ndi ku Beti Sani konse, kufupi ndi ku Zaretani kumunsi kwa Yezireeli, kuyambira ku Beti-Seani mpaka ku Abeli-Mehola kukafika mpaka ku Yokineamu;
13 在基列的拉末有便‧基別,他管理在基列的瑪拿西子孫睚珥的城邑,巴珊的亞珥歌伯地的大城六十座,都有城牆和銅閂;
Beni-Geberi, anali woyangʼanira Ramoti Giliyadi (midzi ya Yairi inali ya mwana wa Manase ku Giliyadi, pamodzinso ndi chigawo cha Arigobu ku Basani ndiponso mizinda yake yayikulu makumi asanu ndi umodzi yokhala ndi malinga ndi mipiringidzo yamkuwa).
14 在瑪哈念有易多的兒子亞希拿達;
Ahinadabu mwana wa Ido, anali woyangʼanira Mahanaimu;
15 在拿弗他利有亞希瑪斯,他也娶了所羅門的一個女兒巴實抹為妻;
Ahimaazi anali woyangʼanira Nafutali (iyeyu anakwatira Basemati mwana wa Solomoni);
16 在亞設和亞祿有戶篩的兒子巴拿;
Baana mwana wa Husai, anali woyangʼanira Aseri ndi Bealoti;
17 在以薩迦有帕路亞的兒子約沙法;
Yehosafati mwana wa Paruwa, anali woyangʼanira Isakara;
18 在便雅憫有以拉的兒子示每;
Simei mwana wa Ela, anali woyangʼanira Benjamini;
19 在基列地,就是從前屬亞摩利王西宏和巴珊王噩之地,有烏利的兒子基別一人管理。
Geberi mwana wa Uri, anali woyangʼanira Giliyadi (dziko la Sihoni mfumu ya Aamori ndi dziko la Ogi mfumu ya Basani). Iye ankayangʼanira chigawo chonsechi yekha.
20 猶大人和以色列人如同海邊的沙那樣多,都吃喝快樂。
Anthu a ku Yuda ndi ku Israeli anali ochuluka ngati mchenga wa mʼmbali mwa nyanja. Ankadya ndi kumwa ndipo ankasangalala.
21 所羅門統管諸國,從大河到非利士地,直到埃及的邊界。所羅門在世的日子,這些國都進貢服事他。
Ndipo Solomoni analamulira mayiko onse kuyambira ku mtsinje wa Yufurate mpaka ku dziko la Afilisti, kukafika mpaka ku malire a dziko la Igupto. Mayikowa ankabweretsa mphatso ndipo anali pansi pa ulamuliro wa Solomoni moyo wake wonse.
22 所羅門每日所用的食物:細麵三十歌珥,粗麵六十歌珥,
Chakudya cha tsiku ndi tsiku cha Solomoni chinali madengu 150 a ufa wosalala ndi madengu 300 a mgayiwa,
23 肥牛十隻,草場的牛二十隻,羊一百隻,還有鹿、羚羊、誁子,並肥禽。
ngʼombe khumi zonenepa zodyetsera mʼkhola, ngʼombe za ku busa makumi awiri, ndiponso nkhosa ndi mbuzi 100, pamodzinso ndi mbawala, agwape, mphoyo ndi mbalame zoweta zonona.
24 所羅門管理大河西邊的諸王,以及從提弗薩直到迦薩的全地,四境盡都平安。
Pakuti ankalamulira dziko lonse la kumadzulo kwa mtsinje wa Yufurate kuyambira ku Tifisa mpaka ku Gaza, mafumu onse a kumadzulo kwa Mtsinje, ndipo anali pa mtendere ndi mayiko onse ozungulira.
25 所羅門在世的日子,從但到別是巴的猶大人和以色列人都在自己的葡萄樹下和無花果樹下安然居住。
Pa nthawi ya Solomoni, Yuda ndi Israeli anali pa mtendere, kuyambira ku Dani mpaka ku Beeriseba. Munthu aliyense ankangodzikhalira pansi pa mpesa wake ndi mtengo wake wa mkuyu.
26 所羅門有套車的馬四萬,還有馬兵一萬二千。
Solomoni anali ndi zipinda 4,000 zodyeramo akavalo okoka magaleta ake ndi anthu 12,000 oyendetsa magaleta.
27 那十二個官吏各按各月供給所羅門王,並一切與他同席之人的食物,一無所缺。
Abwanamkubwa a zigawo aja, aliyense pa mwezi wake, ankapereka chakudya cha Mfumu Solomoni ndi cha anthu onse amene ankadya naye. Iwo ankaonetsetsa kuti pasasowe kalikonse.
28 眾人各按各分,將養馬與快馬的大麥和乾草送到官吏那裏。
Ankabweretsanso ku malo ake ofunikira muyeso wawo wa barele ndi udzu wa akavalo okoka magaleta ndiponso akavalo ena.
29 上帝賜給所羅門極大的智慧聰明和廣大的心,如同海沙不可測量。
Mulungu anamupatsa Solomoni nzeru ndi luntha losaneneka ndipo nzeru zake zinali zochuluka ngati mchenga wa mʼmbali mwa nyanja.
30 所羅門的智慧超過東方人和埃及人的一切智慧。
Nzeru za Solomoni zinali zoposa nzeru za anthu onse a Kummawa ndiponso nzeru zonse za ku Igupto.
31 他的智慧勝過萬人,勝過以斯拉人以探,並瑪曷的兒子希幔、甲各、達大的智慧。他的名聲傳揚在四圍的列國。
Iye anali wanzeru kuposa munthu wina aliyense, kuposa ngakhale Etani wa banja la Ezara, Hemani, Kalikoli ndi Darida, ana a Maholi. Ndipo mbiri yake inamveka kwa mitundu yonse ya anthu ozungulira.
32 他作箴言三千句,詩歌一千零五首。
Solomoni anapeka miyambi 3,000 ndi kulemba nyimbo 1,005.
33 他講論草木,自黎巴嫩的香柏樹直到牆上長的牛膝草,又講論飛禽走獸、昆蟲水族。
Iye ankaphunzitsa za mitengo, kuyambira mtengo wa mkungudza wa ku Lebanoni mpaka kachitsamba ka hisope khomera pa khoma. Iye ankaphunzitsanso za nyama ndi mbalame, zinthu zokwawa pansi ndiponso za nsomba.
34 天下列王聽見所羅門的智慧,就都差人來聽他的智慧話。
Anthu a mitundu yonse ankabwera kudzamva nzeru za Solomoni. Anthu amenewa ankatumizidwa ndi mafumu onse a dziko lapansi amene anamvapo za nzeru zakezo.

< 列王紀上 4 >