< 歷代志上 4 >
1 猶大的兒子是法勒斯、希斯崙、迦米、戶珥、朔巴。
Ana a Yuda anali awa: Perezi, Hezironi, Karimi, Huri ndi Sobali.
2 朔巴的兒子利亞雅生雅哈;雅哈生亞戶買和拉哈。這是瑣拉人的諸族。
Reaya mwana wa Sobala anabereka Yahati, ndipo Yahati anabereka Ahumai ndi Lahadi. Awa anali mabanja a Azorati.
3 以坦之祖的兒子是耶斯列、伊施瑪、伊得巴;他們的妹子名叫哈悉勒玻尼。
Ana a Etamu anali awa: Yezireeli, Isima ndi Idibasi. Dzina la mlongo wawo linali Hazeleliponi.
4 基多之祖是毗努伊勒。戶沙之祖是以謝珥。這都是伯利恆之祖以法她的長子戶珥所生的。
Penueli anabereka Gedori, ndipo Ezeri anabereka Husa. Awa anali ana a Huri, mwana wachisamba wa Efurata ndi abambo a Betelehemu.
5 提哥亞之祖亞施戶有兩個妻子:一名希拉,一名拿拉。
Asihuri abambo a Tekowa anali ndi akazi awiri, Hela ndi Naara.
6 拿拉給亞施戶生亞戶撒、希弗、提米尼、哈轄斯他利。這都是拿拉的兒子。
Naara anamuberekera Ahuzamu, Heferi, Temani ndi Haahasitari. Awa ndiwo anali ana a Naara.
Ana a Hela: Zereti, Zohari, Etinani,
ndi Kozi, amene anali abambo ake a Anubi ndi Hazo-Beba ndi mabanja a Ahariheli mwana wa Harumi.
9 雅比斯比他眾弟兄更尊貴,他母親給他起名叫雅比斯,意思說:我生他甚是痛苦。
Yabesi anali munthu wolemekezeka kwambiri kuposa abale ake. Amayi ake anamutcha Yabesi kutanthauza kuti, “Chifukwa ndinamubala ndi ululu wambiri.”
10 雅比斯求告以色列的上帝說:「甚願你賜福與我,擴張我的境界,常與我同在,保佑我不遭患難,不受艱苦。」上帝就應允他所求的。
Yabesi analira kwa Mulungu wa Israeli kuti, “Mundidalitse ndipo mukulitse dziko langa! Dzanja lanu likhale pa ine ndipo mundisunge kuti choyipa chisandigwere ndi kundisautsa.” Ndipo Mulungu anamupatsa chopempha chakecho.
Kelubi, mʼbale wa Suha, anabereka Mehiri, amene anabereka Esitoni.
12 伊施屯生伯拉巴、巴西亞,並珥拿轄之祖提欣拿,這都是利迦人。
Esitoni anabereka Beti-Rafa, Paseya ndi Tehina amene anabereka Iri Nahasi. Amenewa ndiwo anthu a ku Reka.
13 基納斯的兒子是俄陀聶、西萊雅。俄陀聶的兒子是哈塔。
Ana a Kenazi anali awa: Otanieli ndi Seraya. Ana a Otanieli anali awa: Hatati ndi Meonotai.
14 憫挪太生俄弗拉;西萊雅生革‧夏納欣人之祖約押。他們都是匠人。
Meonotai anabereka Ofura. Seraya anabereka Yowabu, amene anabereka Ge-Harasimu. Anawatcha dzina ili chifukwa anthu ake anali amisiri.
15 耶孚尼的兒子是迦勒;迦勒的兒子是以路、以拉、拿安。以拉的兒子是基納斯。
Ana a Kalebe mwana wa Yefune anali awa: Iru, Ela ndi Naama. Mwana wa Ela anali Kenazi.
Ana a Yehaleleli anali awa: Zifi, Zifa, Tiriya ndi Asareli.
17 以斯拉的兒子是益帖、米列、以弗、雅倫。米列娶法老女兒比提雅為妻,生米利暗、沙買,和以實提摩之祖益巴。米列又娶猶大女子為妻,生基多之祖雅列,梭哥之祖希伯,和撒挪亞之祖耶古鐵。
Ana a Ezara anali awa: Yeteri, Meredi, Eferi ndi Yaloni. Mmodzi mwa akazi a Meredi anabereka Miriamu, Samai ndi Isiba abambo ake a Esitemowa.
(Mkazi wake wa Chiyuda anabereka Yaredi abambo ake a Gedori, Heberi abambo ake a Soko ndi Yekutieli abambo a Zanowa). Awa anali ana a mwana wamkazi wa Farao, Bitia, amene Meredi anakwatira.
19 荷第雅的妻是拿含的妹子,她所生的兒子是迦米人基伊拉和瑪迦人以實提摩之祖。
Ana a mkazi wa Hodiya, mlongo wa Nahamu anali awa: abambo ake a Keila wa ku Garimi ndi Esitemowa wa ku Maaka.
20 示門的兒子是暗嫩、林拿、便‧哈南、提倫。 以示的兒子是梭黑與便‧梭黑。
Ana a Simeoni anali awa: Amnoni, Rina, Beni-Hanani ndi Tiloni. Ana a Isi anali awa: Zoheti ndi Beni-Zoheti.
21 猶大的兒子是示拉;示拉的兒子是利迦之祖珥,瑪利沙之祖拉大,和屬亞實比族織細麻布的各家。
Ana a Sela mwana wa Yuda anali awa: Eri amene anabereka Leka, Laada amene anabereka Maresa ndi mabanja a anthu owomba nsalu zofewa ndi zosalala a ku Beti-Asibeya,
22 還有約敬、哥西巴人、約阿施、薩拉,就是在摩押地掌權的,又有雅叔比利恆。這都是古時所記載的。
Yokimu, anthu a ku Kozeba, ndiponso Yowasi ndi Sarafi, amene ankalamulira Mowabu ndi Yasibu-Lehemu. (Nkhani zimenezi ndi zakalekale).
23 這些人都是窯匠,是尼他應和基低拉的居民;與王同處,為王做工。
Iwo anali owumba mbiya amene ankakhala ku Netaimu ndi Gederi. Ankakhala kumeneko ndi kumatumikira mfumu.
24 西緬的兒子是尼母利、雅憫、雅立、謝拉、掃羅。
Ana a Simeoni anali awa: Nemueli, Yamini, Yaribu, Zera ndi Sauli;
25 掃羅的兒子是沙龍;沙龍的兒子是米比衫;米比衫的兒子是米施瑪;
Salumu anali mwana wa Sauli, Mibisamu anali mwana wa Salumu ndipo Misima anali mwana wa Mibisamu.
26 米施瑪的兒子是哈母利;哈母利的兒子是撒刻;撒刻的兒子是示每。
Zidzukulu za Misima zinali izi: Hamueli, Zakuri ndi Simei.
27 示每有十六個兒子,六個女兒,他弟兄的兒女不多,他們各家不如猶大族的人丁增多。
Simei anali ndi ana aamuna 16 ndi ana aakazi 6, koma abale ake sanabereke ana ambiri; kotero banja lawo silinakule ngati anthu ena a ku Yuda.
Iwo amakhala ku Beeriseba, Molada, Hazari-Suwali,
Betueli, Horima, Zikilagi,
31 伯‧瑪嘉博、哈薩‧蘇撒、伯‧比利、沙拉音,這些城邑直到大衛作王的時候都是屬西緬人的。
Beti-Marikaboti, Hazari-Susimu, Beti-Biri ndi Saaraimu. Iyi inali mizinda yawo mpaka pa nthawi ya ulamuliro wa Davide.
32 他們的五個城邑是以坦、亞因、臨門、陀健、亞珊;
Midzi yowazungulira inali Etamu, Aini, Rimoni, Tokeni ndi Asani, midzi isanu
33 還有屬城的鄉村,直到巴力。這是他們的住處,他們都有家譜。
ndi midzi yonse yozungulira mizinda imeneyi mpaka ku Baala. Awa anali malo awo okhalapo. Ndipo anasunga mbiri ya makolo awo.
Mesobabu, Yamuleki, Yosa mwana wa Amaziya,
35 約珥、約示比的兒子耶戶;約示比是西萊雅的兒子;西萊雅是亞薛的兒子。
Yoweli, Yehu mwana wa Yosibiya, mwana wa Seraya, mwana wa Asieli,
36 還有以利約乃、雅哥巴、約朔海、亞帥雅、亞底業、耶西篾、比拿雅、
komanso Eliyoenai, Yaakoba, Yesohaya, Asaya, Adieli, Yesimieli, Benaya,
37 示非的兒子細撒。示非是亞龍的兒子;亞龍是耶大雅的兒子;耶大雅是申利的兒子;申利是示瑪雅的兒子。
ndiponso Ziza mwana wa Sifi, mwana wa Aloni, mwana wa Yedaya, mwana wa Simiri, mwana wa Semaya.
38 以上所記的人名都是作族長的,他們宗族的人數增多。
Anthu amene atchulidwawa anali atsogoleri a mabanja awo. Mabanja awo anakula kwambiri
39 他們往平原東邊基多口去,尋找牧放羊群的草場,
ndipo anakafika ku malire a Gedori ku chigwa cha kummawa kufuna msipu wodyetsa ziweto zawo.
40 尋得肥美的草場地,又寬闊又平靜。從前住那裏的是含族的人。
Anapeza msipu wobiriwira ndi wabwino ndipo dziko linali lalikulu, la mtendere ndi bata. Kumeneko kunkakhala fuko la Hamu poyamba.
41 以上錄名的人,在猶大王希西家年間,來攻擊含族人的帳棚和那裏所有的米烏尼人,將他們滅盡,就住在他們的地方,直到今日,因為那裏有草場可以牧放羊群。
Anthu amene mayina awowa alembedwa, anabwera pa nthawi ya Hezekiya mfumu ya Yuda. Iwo anathira nkhondo fuko la Hamu mʼmalo awo amene amakhala komanso Ameuni amene anali kumeneko ndipo anawononga onsewo kotero kuti mbiri yawo simvekanso mpaka lero lino. Kotero iwo anakhala mʼmalo awo chifukwa kunali msipu wa ziweto zawo.
42 這西緬人中,有五百人上西珥山,率領他們的是以示的兒子毗拉提、尼利雅、利法雅,和烏薛,
Ndipo anthu 500 a fuko la Simeoni, motsogozedwa ndi Pelatiya, Neariya, Refaya ndi Uzieli, ana a Isi, analanda dziko lamapiri la Seiri.
43 殺了逃脫剩下的亞瑪力人,就住在那裏直到今日。
Iwo anapha Aamaleki otsala amene anali atapulumuka ndipo akukhala kumeneko mpaka lero lino.