< 撒迦利亚书 14 >

1 耶和华的日子临近,你的财物必被抢掠,在你中间分散。
Taonani tsiku la Yehova likubwera pamene zinthu zimene adani ako anakulanda azidzagawana iwe ukuona.
2 因为我必聚集万国与耶路撒冷争战,城必被攻取,房屋被抢夺,妇女被玷污,城中的民一半被掳去;剩下的民仍在城中,不致剪除。
Ndidzasonkhanitsa anthu a mitundu yonse kuti adzathire nkhondo Yerusalemu; mzindawu udzalandidwa, nyumba zidzaphwasulidwa, ndipo akazi adzagwiriridwa. Theka la anthu a mu mzindamu lidzapita ku ukapolo, koma ena onse otsala mu mzindamu sadzachotsedwa.
3 那时,耶和华必出去与那些国争战,好像从前争战一样。
Pamenepo Yehova adzabwera kudzamenyana ndi mitundu ya anthu imeneyi, ngati mmene amachitira pa nthawi ya nkhondo.
4 那日,他的脚必站在耶路撒冷前面朝东的橄榄山上。这山必从中间分裂,自东至西成为极大的谷。山的一半向北挪移,一半向南挪移。
Tsiku limenelo adzayimirira pa Phiri la Olivi, kummawa kwa Yerusalemu, ndipo Phiri la Olivilo lidzagawikana pawiri kuyambira kummawa mpaka kumadzulo, kupanga chigwa chachikulu, kuchititsa kuti theka la phiri lisunthire kumpoto ndi linalo kummwera.
5 你们要从我山的谷中逃跑,因为山谷必延到亚萨。你们逃跑,必如犹大王乌西雅年间的人逃避大地震一样。耶和华—我的 神必降临,有一切圣者同来。
Inu mudzathawa podzera mʼchigwa chapakati pa phirilo, pakuti chidzafika mpaka ku Azeli. Mudzathawa monga munachitira pa tsiku la chivomerezi nthawi ya Uziya mfumu ya Yuda. Kenaka Yehova Mulungu wanga adzabwera, pamodzi ndi oyera ake onse.
6 那日,必没有光,三光必退缩。
Tsiku limenelo sipadzakhala kuwala, kuzizira kapena chisanu.
7 那日,必是耶和华所知道的,不是白昼,也不是黑夜,到了晚上才有光明。
Lidzakhala tsiku lapaderadera, silidzakhala usana kapena usiku; tsiku limeneli akulidziwa ndi Yehova yekha. Ikadzafika nthawi ya madzulo, kudzakhala kukuwalabe.
8 那日,必有活水从耶路撒冷出来,一半往东海流,一半往西海流;冬夏都是如此。
Tsiku limenelo madzi amoyo adzatuluka mu Yerusalemu, theka lidzapita ku nyanja ya kummawa ndipo theka lina ku nyanja ya kumadzulo, nthawi yachilimwe ndi nthawi yozizira yomwe.
9 耶和华必作全地的王。那日耶和华必为独一无二的,他的名也是独一无二的。
Ndipo Yehova adzakhala mfumu pa dziko lonse lapansi. Tsiku limenelo padzakhala Ambuye mmodzi yekha, ndipo dzina lidzakhala limodzi lomwelo.
10 全地,从迦巴直到耶路撒冷南方的临门,要变为亚拉巴。耶路撒冷必仍居高位,就是从便雅悯门到第一门之处,又到角门,并从哈楠业楼,直到王的酒榨。
Dziko lonse, kuyambira ku Geba mpaka ku Rimoni, kummwera kwa Yerusalemu, lidzakhala ngati Araba. Koma Yerusalemu adzakwezedwa ndipo adzakhala pamalo pakepo, kuyambira ku Chipata cha Benjamini mpaka ku malo amene ali ku Chipata Choyamba, ku Chipata Chapangodya, ndipo kuyambira ku Nsanja ya Hananeli mpaka ku malo opsinyira mphesa za mfumu.
11 人必住在其中,不再有咒诅。耶路撒冷人必安然居住。
Mʼmenemo mudzakhala anthu; sadzawonongedwanso. Yerusalemu adzakhala pa mtendere.
12 耶和华用灾殃攻击那与耶路撒冷争战的列国人,必是这样:他们两脚站立的时候,肉必消没,眼在眶中干瘪,舌在口中溃烂。
Mliri umene Yehova adzakanthire nawo mitundu yonse ya anthu imene inkamenyana ndi Yerusalemu ndi uwu: Matupi awo adzawola iwo eni akuyenda, maso awo adzawola ali mʼmalo mwake, ndipo malilime awo adzawola ali mʼkamwa mwawo.
13 那日,耶和华必使他们大大扰乱。他们各人彼此揪住,举手攻击。
Pa tsiku limenelo Yehova adzasokoneza anthu akuluakulu. Munthu aliyense adzagwira dzanja la mnzake, ndi kuyamba kumenyana okhaokha.
14 犹大也必在耶路撒冷争战。那时四围各国的财物,就是许多金银衣服,必被收聚。
Yuda nayenso adzachita nkhondo ku Yerusalemu. Chuma chonse cha anthu a mitundu yozungulira adzachisonkhanitsa pamodzi; golide, siliva ndi zovala zochuluka kwambiri.
15 那临到马匹、骡子、骆驼、驴,和营中一切牲畜的灾殃是与那灾殃一般。
Mliri womwewo udzapha akavalo ndi nyulu, ngamira ndi abulu, pamodzi ndi nyama zonse zokhala ku misasako.
16 所有来攻击耶路撒冷列国中剩下的人,必年年上来敬拜大君王—万军之耶和华,并守住棚节。
Kenaka opulumuka ochokera mwa mitundu yonse ya anthu amene anathira nkhondo Yerusalemu, azidzapita chaka ndi chaka kukapembedza Mfumu Yehova Wamphamvuzonse, ndiponso kukachita Chikondwerero cha Misasa.
17 地上万族中,凡不上耶路撒冷敬拜大君王—万军之耶和华的,必无雨降在他们的地上。
Ngati mitundu ina ya anthu pa dziko lapansi sidzapita ku Yerusalemu kukapembedza Mfumu Yehova Wamphamvuzonse, idzakhala wopanda mvula.
18 埃及族若不上来,雨也不降在他们的地上;凡不上来守住棚节的列国人,耶和华也必用这灾攻击他们。
Ndipo ngati anthu a ku Igupto sadzapita ndi kukakhala nawo kumeneko, adzakhala wopanda mvula. Yehova adzabweretsa pa iwo mliri umene analangira mitundu ina ya anthu imene sinapite ku Chikondwerero cha Misasa.
19 这就是埃及的刑罚和那不上来守住棚节之列国的刑罚。
Chimenechi chidzakhala chilango cha Igupto ndiponso mitundu ina yonse imene sidzapita ku Chikondwerero cha Misasa.
20 当那日,马的铃铛上必有“归耶和华为圣”的这句话。耶和华殿内的锅必如祭坛前的碗一样。
Pa tsiku limenelo pa maberu a akavalo padzalembedwa mawu oti wopatulikira Yehova, ndipo miphika ya mʼNyumba ya Yehova idzakhala yopatulika ngati mbale za ku guwa.
21 凡耶路撒冷和犹大的锅都必归万军之耶和华为圣。凡献祭的都必来取这锅,煮肉在其中。当那日,在万军之耶和华的殿中必不再有迦南人。
Mʼphika uliwonse ku Yerusalemu ndi ku Yuda udzakhala wopatulikira Yehova Wamphamvuzonse, ndipo onse amene adzabwera kudzapereka nsembe adzatenga miphika ina ndi kuphikiramo. Ndipo nthawi imeneyo simudzakhalanso Akanaani mʼNyumba ya Yehova Wamphamvuzonse.

< 撒迦利亚书 14 >