< 撒迦利亚书 13 >
1 “那日,必给大卫家和耶路撒冷的居民开一个泉源,洗除罪恶与污秽。”
“Pa tsiku limenelo nyumba ya Davide adzayitsekulira kasupe wa madzi pamodzi ndi okhala mu Yerusalemu, kuti awachotsere tchimo lawo ndi chodetsa chawo.
2 万军之耶和华说:“那日,我必从地上除灭偶像的名,不再被人记念;也必使这地不再有假先知与污秽的灵。
“Pa tsiku limenelo, ndidzafafaniziratu mayina a mafano mʼdziko, ndipo sadzawakumbukiranso,” akutero Yehova Wamphamvuzonse. “Ndidzachotsa mʼdziko aneneri pamodzi ndi mzimu wonyansa.
3 若再有人说预言,生他的父母必对他说:‘你不得存活,因为你托耶和华的名说假预言。’生他的父母在他说预言的时候,要将他刺透。
Ndipo ngati wina aliyense adzafuna kunenera, abambo ndi amayi ake amene anamubereka, adzamuwuza kuti, ‘Uyenera kufa, chifukwa wayankhula bodza mʼdzina la Yehova.’ Pamene anenera, makolo ake omwe adzamubaya.
4 那日,凡作先知说预言的必因他所论的异象羞愧,不再穿毛衣哄骗人。
“Pa tsiku limenelo mneneri aliyense adzachita manyazi chifukwa cha masomphenya ake. Sadzavala chovala chake chaubweya ndi cholinga chonamiza anthu.
5 他必说:‘我不是先知,我是耕地的;我从幼年作人的奴仆。’
Iye adzati, ‘Sindine mneneri. Ndine mlimi; ndakhala ndi kulima munda kuyambira ubwana wanga.’
6 必有人问他说:‘你两臂中间是什么伤呢?’他必回答说:‘这是我在亲友家中所受的伤。’”
Ngati wina adzamufunsa, ‘Zilonda zili mʼthupi lakoli ndi chiyani?’ Iye adzayankha kuti, ‘Zilondazi ndinazilandira mʼnyumba ya abwenzi anga.’
7 万军之耶和华说: 刀剑哪,应当兴起, 攻击我的牧人和我的同伴。 击打牧人,羊就分散; 我必反手加在微小者的身上。
“Dzambatuka iwe lupanga, ukanthe mʼbusa wanga, ukanthe munthu amene ali pafupi ndi Ine!” akutero Yehova Wamphamvuzonse. Kantha mʼbusa ndipo nkhosa zidzabalalika, ndipo ndidzatambalitsa dzanja langa kuwononga zazingʼono.
8 耶和华说:这全地的人, 三分之二必剪除而死, 三分之一仍必存留。
Mʼdziko monse, akutero Yehova Wamphamvuzonse, “zigawo ziwiri mwa zigawo zitatu za anthu zidzakanthidwa ndi kuwonongeka; koma chigawo chimodzi chidzatsala mʼdzikomo.
9 我要使这三分之一经火, 熬炼他们,如熬炼银子; 试炼他们,如试炼金子。 他们必求告我的名, 我必应允他们。 我要说:这是我的子民。 他们也要说:耶和华是我们的 神。
Chigawo chachitatuchi ndidzachiyika pa moto; ndidzawayeretsa monga momwe amayeretsera siliva ndi kuwayesa monga momwe amayesera golide. Adzayitana pa dzina langa ndipo Ine ndidzawayankha; Ine ndidzanena kuti, ‘Awa ndi anthu anga,’ ndipo iwo adzanena kuti, ‘Yehova ndiye Mulungu wathu.’”