< 撒迦利亚书 11 >

1 黎巴嫩哪,开开你的门, 任火烧灭你的香柏树。
Tsekula zitseko zako, iwe Lebanoni, kuti moto unyeketse mikungudza yako!
2 松树啊,应当哀号; 因为香柏树倾倒,佳美的树毁坏。 巴珊的橡树啊,应当哀号, 因为茂盛的树林已经倒了。
Lira mwachisoni, iwe mtengo wa payini, pakuti mkungudza wagwa; mtengo wamphamvu wawonongeka! Lirani mwachisoni, inu mitengo ya thundu ya Basani; nkhalango yowirira yadulidwa!
3 听啊,有牧人哀号的声音, 因他们荣华的草场毁坏了。 有少壮狮子咆哮的声音, 因约旦河旁的丛林荒废了。
Imvani kulira mwachisoni kwa abusa; msipu wawo wobiriwira wawonongeka! Imvani kubangula kwa mikango; nkhalango yowirira ya ku Yorodani yawonongeka!
4 耶和华—我的 神如此说:“你—撒迦利亚要牧养这将宰的群羊。
Yehova Mulungu wanga akuti, “Dyetsa nkhosa zimene zikukaphedwa.
5 买他们的宰了他们,以自己为无罪;卖他们的说:‘耶和华是应当称颂的,因我成为富足。’牧养他们的并不怜恤他们。
Amene amagula nkhosazo amazipha ndipo salangidwa. Amene amazigulitsa amanena kuti, ‘Alemekezeke Yehova, ine ndalemera!’ Abusa ake omwe sazimvera chisoni nkhosazo.
6 耶和华说:‘我不再怜恤这地的居民,必将这民交给各人的邻舍和他们王的手中。他们必毁灭这地,我也不救这民脱离他们的手。’”
Pakuti Ine sindidzamveranso chisoni anthu okhala mʼdziko,” akutero Yehova. “Ndidzapereka munthu aliyense mʼmanja mwa mnansi wake ndi mwa mfumu yake. Iwo adzazunza dziko, ndipo Ine sindidzawapulumutsa mʼmanja mwawo.”
7 于是,我牧养这将宰的群羊,就是群中最困苦的羊。我拿着两根杖,一根我称为“荣美”,一根我称为“联索”。这样,我牧养了群羊。
Choncho ine ndinadyetsa nkhosa zokaphedwa, makamaka nkhosa zoponderezedwa. Pamenepo ndinatenga ndodo ziwiri ndipo yoyamba ndinayitcha Kukoma mtima ndipo yachiwiri ndinayitcha Umodzi ndipo ndinadyetsa nkhosazo.
8 一月之内,我除灭三个牧人,因为我的心厌烦他们;他们的心也憎嫌我。
Pa mwezi umodzi ndinachotsa abusa atatu. Abusawo anadana nane, ndipo ndinatopa nawo.
9 我就说:“我不牧养你们。要死的,由他死;要丧亡的,由他丧亡;余剩的,由他们彼此相食。”
Ndinawuza gulu la nkhosalo kuti, “Sindidzakhalanso mʼbusa wanu. Imene ikufa, ife, ndipo imene ikuwonongeka, iwonongeke, zimene zatsala zizidyana.”
10 我折断那称为“荣美”的杖,表明我废弃与万民所立的约。
Kenaka ndinatenga ndodo yanga yotchedwa Kukoma mtima ndi kuyithyola, kuphwanya pangano limene ndinachita ndi mitundu yonse ya anthu.
11 当日就废弃了。这样,那些仰望我的困苦羊就知道所说的是耶和华的话。
Linaphwanyidwa tsiku limenelo ndipo nkhosa zosautsidwa zimene zimandiyangʼanitsitsa zinadziwa kuti anali mawu a Yehova.
12 我对他们说:“你们若以为美,就给我工价。不然,就罢了!”于是他们给了三十块钱作为我的工价。
Ndinawawuza kuti, “Ngati mukuganiza kuti zili bwino, patseni malipiro anga; koma ngati si choncho, sungani malipirowo.” Kotero anandipatsa ndalama zasiliva makumi atatu.
13 耶和华吩咐我说:“要把众人所估定美好的价值丢给窑户。”我便将这三十块钱,在耶和华的殿中丢给窑户了。
Ndipo Yehova anandiwuza kuti, “Ziponye kwa wowumba mbiya,” mtengo woyenera umene anapereka pondigula Ine! Choncho ndinatenga ndalama zasiliva makumi atatu ndi kuziponya mʼnyumba ya Yehova kwa wowumba mbiya.
14 我又折断称为“联索”的那根杖,表明我废弃犹大与以色列弟兄的情谊。
Kenaka ndinathyola ndodo yanga yachiwiri yotchedwa Umodzi, kuthetsa ubale pakati pa Yuda ndi Israeli.
15 耶和华又吩咐我说:“你再取愚昧牧人所用的器具,
Pamenepo Yehova anayankhula nane kuti, “Tenganso zida za mʼbusa wopusa.
16 因我要在这地兴起一个牧人。他不看顾丧亡的,不寻找分散的,不医治受伤的,也不牧养强壮的;却要吃肥羊的肉,撕裂它的蹄子。
Pakuti ndidzawutsa mʼbusa mʼdzikomo amene sadzasamalira zotayika, kapena kufunafuna zazingʼono, kapena zovulala, kapena kudyetsa nkhosa zabwino, koma iye adzadya nyama ya nkhosa zonenepa, nʼkumakukuta ndi ziboda zomwe.
17 无用的牧人丢弃羊群有祸了! 刀必临到他的膀臂和右眼上。 他的膀臂必全然枯干; 他的右眼也必昏暗失明。”
“Tsoka kwa mʼbusa wopandapake, amene amasiya nkhosa! Lupanga limukanthe pa mkono wake ndi pa diso lake lakumanja! Mkono wake ufote kotheratu, diso lake lamanja lisaonenso.”

< 撒迦利亚书 11 >