< 路得记 1 >
1 当士师秉政的时候,国中遭遇饥荒。在犹大的伯利恒,有一个人带着妻子和两个儿子往摩押地去寄居。
Mu nthawi imene oweruza ankalamulira Israeli, munali njala mʼdziko, ndipo munthu wina wa ku Betelehemu mʼdziko la Yuda anapita pamodzi ndi mkazi wake ndi ana ake aamuna awiri, kukakhala ku Mowabu kwa nthawi yochepa.
2 这人名叫以利米勒,他的妻名叫拿俄米;他两个儿子,一个名叫玛伦,一个名叫基连,都是犹大伯利恒的以法他人。他们到了摩押地,就住在那里。
Dzina la munthuyo linali Elimeleki, dzina la mkazi wake linali Naomi, ndipo mayina a ana awo aamuna anali Maaloni ndi Kiliyoni. Iwo anali Aefurati ochokera ku Betelehemu ku Yuda. Ndipo anapita kukakhala ku Mowabu.
3 后来拿俄米的丈夫以利米勒死了,剩下妇人和她两个儿子。
Kenaka Elimeleki, mwamuna wake wa Naomi anamwalira ndipo Naomiyo anatsala ndi ana ake aamuna awiri aja.
4 这两个儿子娶了摩押女子为妻,一个名叫俄珥巴,一个名叫路得,在那里住了约有十年。
Iwo anakwatira akazi a Chimowabu; wina dzina lake Oripa ndi wina Rute. Atakhala kumeneko pafupifupi zaka khumi,
5 玛伦和基连二人也死了,剩下拿俄米,没有丈夫,也没有儿子。
Maloni ndi Kiliyoni anamwaliranso kotero kuti Naomi anatsala yekha wopanda ana ake awiri aja ndi mwamuna wake.
6 她就与两个儿妇起身,要从摩押地归回;因为她在摩押地听见耶和华眷顾自己的百姓,赐粮食与他们。
Naomi ndi apongozi ake awiri aja ananyamuka kubwerera kwawo kuchokera ku Mowabu popeza anali atamva ali ku Mowabuko kuti Yehova anakomera mtima anthu ake ndi kuwapatsa chakudya.
7 于是她和两个儿妇起行离开所住的地方,要回犹大地去。
Naomi pamodzi ndi apongozi ake awiri aja anachoka kumene ankakhala ndi kuyamba ulendo obwerera kwawo ku Yuda.
8 拿俄米对两个儿妇说:“你们各人回娘家去吧。愿耶和华恩待你们,像你们恩待已死的人与我一样!
Kenaka Naomi anati kwa apongozi ake awiri aja, “Bwererani, aliyense kwa amayi ake. Yehova akukomereni mtima, monga munachita ndi malemu aja ndi ine ndemwe.
9 愿耶和华使你们各在新夫家中得平安!”于是拿俄米与她们亲嘴。她们就放声而哭,
“Yehova akuthandizeni kuti aliyense wa inu apeze pokhala pabwino komanso mwamuna.” Kenaka anawapsompsona koma awiriwo analira mokweza.
Ndipo anati kwa Naomi, “Ife tipita nawo kwa anthu akwanu.”
11 拿俄米说:“我女儿们哪,回去吧!为何要跟我去呢?我还能生子作你们的丈夫吗?
Koma Naomi anati, “Bwererani kwanu ana anga. Chifukwa chiyani mukufuna kupita ndi ine? Kodi ine ndingaberekenso ana ena kuti akhale amuna anu?
12 我女儿们哪,回去吧!我年纪老迈,不能再有丈夫;即或说,我还有指望,今夜有丈夫可以生子,
Bwererani kwanu ana anga muzipita kwanu. Ine ndakalamba kwambiri kotero kuti sindingakwatiwenso. Ngakhale ndikananena kuti ndili nacho chikhulupiriro, ngakhale ndikanakhala ndi mwamuna usiku uno, ndipo nʼkubala ana aamuna,
13 你们岂能等着他们长大呢?你们岂能等着他们不嫁别人呢?我女儿们哪,不要这样。我为你们的缘故甚是愁苦,因为耶和华伸手攻击我。”
kodi inu mukanadikira kuti akule? Kodi mukanakhalabe osakwatiwa kudikira iwowo? Ayi ana anga. Zimenezi zikundiwawa kwambiri kuposa inu, chifukwa ndi ineyo amene Yehova wafuna kuti ndizunzike.”
14 两个儿妇又放声而哭,俄珥巴与婆婆亲嘴而别,只是路得舍不得拿俄米。
Atamva zimenezi analiranso kwambiri, ndipo Oripa anapsompsona apongozi ake nawatsanzika, koma Rute anakakamirabe.
15 拿俄米说:“看哪,你嫂子已经回她本国和她所拜的神那里去了,你也跟着你嫂子回去吧!”
Naomi anati “Taona, mʼbale wako wabwerera kwawo kwa anthu ake ndi kwa milungu yake. Bwerera nawenso umulondole mʼbale wako.”
16 路得说:“不要催我回去不跟随你。你往哪里去,我也往那里去;你在哪里住宿,我也在那里住宿;你的国就是我的国,你的 神就是我的 神。
Koma Rute anayankha kuti, “Musandikakamize kuti ndikusiyeni kapena kuti ndibwerere osakutsatani. Kumene inu mupite ine ndipita komweko, ndipo kumene mukakhale inenso ndikakhala komweko. Abale anu adzakhala abale anga ndipo Mulungu wanu adzakhala Mulungu wanga.
17 你在哪里死,我也在那里死,也葬在那里。除非死能使你我相离!不然,愿耶和华重重地降罚与我。”
Kumene mukafere inenso ndidzafera komweko ndipo komweko ndikayikidwa mʼmanda. Yehova andichite choyipa chingakule motani, ngati china chingatirekanitse ife kupatula imfa.”
18 拿俄米见路得定意要跟随自己去,就不再劝她了。
Naomi atazindikira kuti Rute watsimikiza kupita naye, analeka kumukakamiza.
19 于是二人同行,来到伯利恒。她们到了伯利恒,合城的人就都惊讶。妇女们说:“这是拿俄米吗?”
Choncho amayi awiriwo anapitiriza ulendo wawo mpaka anakafika ku Betelehemu. Pamene ankafika mu Betelehemu, anthu onse a mʼmudzimo anatekeseka chifukwa cha iwowo ndipo amayi ambiri ankanena kuti, “Kodi uyu nʼkukhala Naomi?”
20 拿俄米对她们说:“不要叫我拿俄米,要叫我玛拉,因为全能者使我受了大苦。
Iye anawawuza kuti, “Musanditchenso Naomi. Muzinditchula ine kuti Mara, chifukwa Wamphamvuzonse wandizunza kwambiri.
21 我满满地出去,耶和华使我空空地回来。耶和华降祸与我;全能者使我受苦。既是这样,你们为何还叫我拿俄米呢?”
Ine ndinapita wolemera, koma Yehova wabwera nane wopanda kanthu. Nanga munditchulirenji Naomi pamene Yehova wandisautsa. Wamphamvuzonse uja wandigwetsera mavuto owawa.”
22 拿俄米和她儿妇摩押女子路得,从摩押地回来到伯利恒,正是动手割大麦的时候。
Naomi anabwerera kuchoka ku dziko la Mowabu pamodzi ndi Rute mpongozi wake. Ndipo anafika ku Betelehemu nthawi yoyamba kukolola barele.