< 诗篇 30 >

1 大卫在献殿的时候,作这诗歌。 耶和华啊,我要尊崇你, 因为你曾提拔我,不叫仇敌向我夸耀。
Salimo la Davide. Nyimbo yoyimba popereka Nyumba ya Mulungu. Ndidzakukwezani Yehova, chifukwa mwanditulutsa kwakuya, ndipo simunalole kuti adani anga akondwere pa ine.
2 耶和华—我的 神啊, 我曾呼求你,你医治了我。
Inu Yehova Mulungu wanga ndinapempha kwa Inu thandizo ndipo Inu munandichiritsa.
3 耶和华啊,你曾把我的灵魂从阴间救上来, 使我存活,不至于下坑。 (Sheol h7585)
Inu Yehova, munanditulutsa ku manda, munandisunga kuti ndisatsalire mʼdzenje. (Sheol h7585)
4 耶和华的圣民哪,你们要歌颂他, 称赞他可记念的圣名。
Imbirani Yehova inu anthu ake okhulupirika; tamandani dzina lake loyera.
5 因为,他的怒气不过是转眼之间; 他的恩典乃是一生之久。 一宿虽然有哭泣, 早晨便必欢呼。
Pakuti mkwiyo wake umakhala kwa kanthawi koma kukoma mtima kwake ndi kwa moyo wonse; utha kuchezera kulira usiku wonse, koma chimwemwe chimabwera mmawa.
6 至于我,我凡事平顺,便说: 我永不动摇。
Pamene ndinaona kuti ndili otetezedwa ndinati, “Sindidzagwedezekanso.”
7 耶和华啊,你曾施恩,叫我的江山稳固; 你掩了面,我就惊惶。
Inu Yehova, pamene munandikomera mtima, munachititsa phiri langa kuyima chilili; koma pamene munabisa nkhope yanu, ndinataya mtima.
8 耶和华啊,我曾求告你; 我向耶和华恳求,说:
Kwa Inu Yehova ndinayitana; kwa Ambuye ndinapempha chifundo;
9 我被害流血,下到坑中,有什么益处呢? 尘土岂能称赞你,传说你的诚实吗?
“Kodi pali phindu lanji powonongeka kwanga ngati nditsikira ku dzenje? Kodi fumbi lidzakutamandani Inu? Kodi lidzalengeza za kukhulupirika kwanu?
10 耶和华啊,求你应允我,怜恤我! 耶和华啊,求你帮助我!
Imvani Yehova ndipo mundichitire chifundo; Yehova mukhale thandizo langa.”
11 你已将我的哀哭变为跳舞, 将我的麻衣脱去,给我披上喜乐,
Inu munasandutsa kulira kwanga kukhala kuvina; munachotsa chiguduli changa ndi kundiveka ndi chimwemwe,
12 好叫我的灵歌颂你,并不住声。 耶和华—我的 神啊,我要称谢你,直到永远!
kuti mtima wanga uthe kuyimbira Inu usakhale chete. Yehova Mulungu wanga, ndidzapereka kwa Inu mayamiko kwamuyaya.

< 诗篇 30 >