< 诗篇 23 >

1 大卫的诗。 耶和华是我的牧者, 我必不致缺乏。
Salimo la Davide. Yehova ndiye mʼbusa wanga, sindidzasowa kanthu.
2 他使我躺卧在青草地上, 领我在可安歇的水边。
Amandigoneka pa msipu wobiriwira, amanditsogolera ku madzi akumwa abwino,
3 他使我的灵魂苏醒, 为自己的名引导我走义路。
amatsitsimutsa moyo wanga. Amanditsogolera mʼnjira zachilungamo chifukwa cha dzina lake.
4 我虽然行过死荫的幽谷, 也不怕遭害, 因为你与我同在; 你的杖,你的竿,都安慰我。
Ngakhale ndiyende mʼchigwa cha mdima wakuda bii, sindidzaopa choyipa, pakuti Inu muli ndi ine; chibonga chanu ndi ndodo yanu zimanditonthoza.
5 在我敌人面前,你为我摆设筵席; 你用油膏了我的头,使我的福杯满溢。
Mumandikonzera chakudya adani anga akuona. Mumadzoza mutu wanga ndi mafuta; chikho changa chimasefukira.
6 我一生一世必有恩惠慈爱随着我; 我且要住在耶和华的殿中,直到永远。
Zoonadi, zokoma ndi chikondi chosasinthika zidzanditsata masiku onse a moyo wanga, ndipo ndidzakhala mʼNyumba ya Yehova kwamuyaya.

< 诗篇 23 >