< 诗篇 20 >
1 大卫的诗,交与伶长。 愿耶和华在你遭难的日子应允你; 愿名为雅各 神的高举你。
Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la Davide. Yehova akuyankhe pamene uli pa msautso; dzina la Mulungu wa Yakobo likuteteze.
Iye atumize thandizo kuchokera ku malo ake opatulika; akugwirizize kuchokera ku Ziyoni.
Iye akumbukire nsembe zako zonse ndipo alandire nsembe zako zopsereza. (Sela)
Akupatse chokhumba cha mtima wako ndipo akuthandize kuti zonse wakonza zichitike.
5 我们要因你的救恩夸胜, 要奉我们 神的名竖立旌旗。 愿耶和华成就你一切所求的!
Ife tidzafuwula ndi chimwemwe pamene iwe wapambana ndipo tidzanyamula mbendera zathu mʼdzina la Mulungu wathu, Yehova ayankhe zopempha zako zonse.
6 现在我知道耶和华救护他的受膏者, 必从他的圣天上应允他, 用右手的能力救护他。
Tsopano ndadziwa kuti Yehova amapulumutsa wodzozedwa wake; Iye amamuyankha kuchokera kumwamba ku malo ake opatulika ndi mphamvu yopulumutsa ya dzanja lake lamanja.
7 有人靠车,有人靠马, 但我们要提到耶和华—我们 神的名。
Ena amadalira magaleta ndipo ena akavalo koma ife tidzadalira dzina la Yehova Mulungu wathu.
Iwo amagonjetsedwa ndi kugwa, koma ife timadzuka ndi kuyima chilili.
9 求耶和华施行拯救; 我们呼求的时候,愿王应允我们!
Inu Yehova, pulumutsani mfumu! Tiyankheni pamene tikuyitanani!