< 诗篇 13 >

1 大卫的诗,交与伶长。 耶和华啊,你忘记我要到几时呢?要到永远吗? 你掩面不顾我要到几时呢?
Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la Davide. Mpaka liti Yehova? Kodi mudzandiyiwala mpaka kalekale? Mpaka liti mudzandibisira nkhope yanu?
2 我心里筹算,终日愁苦,要到几时呢? 我的仇敌升高压制我,要到几时呢?
Ndidzalimbana ndi maganizo anga ndi kukhala ndi chisoni mu mtima mwanga tsiku lililonse mpaka liti? Mpaka liti adani anga adzandipambana?
3 耶和华—我的 神啊,求你看顾我,应允我! 使我眼目光明,免得我沉睡至死;
Ndiyangʼaneni ndi kundiyankha, Inu Yehova Mulungu wanga. Walitsani maso anga kuti ndingafe;
4 免得我的仇敌说:我胜了他; 免得我的敌人在我摇动的时候喜乐。
mdani wanga adzati, “Ndamugonjetsa,” ndipo adani anga adzakondwera pamene ine ndagwa.
5 但我倚靠你的慈爱; 我的心因你的救恩快乐。
Koma ndikudalira chikondi chanu chosasinthika; mtima wanga umakondwera ndi chipulumutso chanu.
6 我要向耶和华歌唱, 因他用厚恩待我。
Ine ndidzayimbira Yehova pakuti wandichitira zokoma.

< 诗篇 13 >