< 诗篇 125 >
1 上行之诗。 倚靠耶和华的人 好像锡安山,永不动摇。
Nyimbo yoyimba pokwera ku Yerusalemu. Amene amadalira Yehova ali ngati phiri la Ziyoni, limene silingagwedezeke koma ndi lokhala mpaka muyaya.
2 众山怎样围绕耶路撒冷, 耶和华也照样围绕他的百姓, 从今时直到永远。
Monga mapiri azungulira Yerusalemu, momwemonso Yehova azungulira anthu ake kuyambira tsopano mpaka muyaya.
3 恶人的杖不常落在义人的分上, 免得义人伸手作恶。
Ndodo yaufumu ya anthu oyipa sidzakhala pa dziko limene lapatsidwa kwa anthu olungama, kuti anthu olungamawo angachite nawonso zoyipa.
Yehova chitirani zabwino amene ndi abwino, amene ndi olungama mtima
5 至于那偏行弯曲道路的人, 耶和华必使他和作恶的人一同出去受刑。 愿平安归于以色列!
Koma amene amatembenukira ku njira zokhotakhota, Yehova adzawachotsa pamodzi ndi anthu ochita zoyipa. Mtendere ukhale pa Israeli.