< 诗篇 114 >

1 以色列出了埃及, 雅各家离开说异言之民;
Pamene Israeli anatuluka mu Igupto, nyumba ya Yakobo kuchoka ku mtundu wa anthu a chiyankhulo chachilendo,
2 那时,犹大为主的圣所, 以色列为他所治理的国度。
Yuda anasanduka malo opatulika a Mulungu, Israeli anasanduka ufumu wake.
3 沧海看见就奔逃; 约旦河也倒流。
Nyanja inaona ndi kuthawa, mtsinje wa Yorodani unabwerera mʼmbuyo;
4 大山踊跃,如公羊; 小山跳舞,如羊羔。
mapiri analumphalumpha ngati nkhosa zazimuna, timapiri ngati ana ankhosa.
5 沧海啊,你为何奔逃? 约旦哪,你为何倒流?
Nʼchifukwa chiyani iwe unathawa? iwe mtsinje wa Yorodani unabwereranji mʼmbuyo?
6 大山哪,你为何踊跃,如公羊? 小山哪,你为何跳舞,如羊羔?
inu mapiri, munalumphalumphiranji ngati nkhosa zazimuna, inu timapiri, ngati ana ankhosa?
7 大地啊,你因见主的面, 就是雅各 神的面,便要震动。
Njenjemera pamaso pa Ambuye iwe dziko lapansi, pamaso pa Mulungu wa Yakobo,
8 他叫磐石变为水池, 叫坚石变为泉源。
amene anasandutsa thanthwe kukhala chitsime, thanthwe lolimba kukhala akasupe a madzi.

< 诗篇 114 >