< 诗篇 108 >

1 大卫的诗歌。 神啊,我心坚定; 我口要唱诗歌颂!
Nyimbo. Salimo la Davide. Mtima wanga ndi wokhazikika, Inu Mulungu; ndidzayimba nyimbo, inde ndidzayimba nyimbo zotamanda ndi moyo wanga wonse.
2 琴瑟啊,你们当醒起! 我自己要极早醒起!
Dzukani, zeze ndi pangwe! Ine ndidzadzutsa mʼbandakucha.
3 耶和华啊,我要在万民中称谢你, 在列邦中歌颂你!
Ndidzakutamandani Yehova, pakati pa anthu a mitundu ina; ndidzayimba za Inu pakati pa anthu a mitundu ina.
4 因为,你的慈爱大过诸天; 你的诚实达到穹苍。
Pakuti chikondi chanu nʼchachikulu, kutalika kwake kuposa kumwamba; kukhulupirika kwanu kumafika mlengalenga.
5 神啊,愿你崇高过于诸天! 愿你的荣耀高过全地!
Kwezekani Inu Mulungu, kuposa mayiko akumwamba, ndipo ulemerero wanu uphimbe dziko lonse lapansi.
6 求你应允我们,用右手拯救我们, 好叫你所亲爱的人得救。
Tipulumutseni ndi kutithandiza ndi dzanja lanu lamanja kuti iwo amene mumawakonda apulumutsidwe.
7 神已经指着他的圣洁说: 我要欢乐;我要分开示剑, 丈量疏割谷。
Mulungu wayankhula kuchokera ku malo ake opatulika: “Mwachipambano Ine ndidzagawa Sekemu ndipo ndidzayesa chigwa cha Sukoti.
8 基列是我的; 玛拿西是我的; 以法莲是护卫我头的; 犹大是我的杖;
Giliyadi ndi wanga, Manase ndi wanganso; Efereimu ndi chipewa changa chodzitetezera, Yuda ndi ndodo yanga yaufumu.
9 摩押是我的沐浴盆; 我要向以东抛鞋; 我必因胜非利士呼喊。
Mowabu ndi mbale yanga yosambiramo ndidzaponya nsapato zanga pa Edomu; ndidzafuwula mopambana pa Filisitiya.”
10 谁能领我进坚固城? 谁能引我到以东地?
Ndani adzandifikitsa ku mzinda wotetezedwa? Ndani adzanditsogolera ku Edomu?
11 神啊,你不是丢弃了我们吗? 神啊,你不和我们的军兵同去吗?
Kodi sindinu Mulungu, Inu amene mwatikana ndipo simuperekezanso magulu athu ankhondo?
12 求你帮助我们攻击敌人, 因为人的帮助是枉然的。
Tithandizeni ife kulimbana ndi mdani, pakuti thandizo la munthu ndi lopanda pake.
13 我们倚靠 神才得施展大能, 因为践踏我们敌人的就是他。
Chifukwa cha Mulungu wathu, ife tidzapeza chipambano, ndipo adzapondereza pansi adani athu.

< 诗篇 108 >