< 箴言 23 >
Ngati ukhala pansi kuti udye pamodzi ndi wolamulira, uyangʼane bwino zimene zili pamaso pako,
ngati ndiwe munthu wadyera udziletse kuti usaonetse dyera lakolo.
Usasirire zakudya zake, pakuti zimenezo ndi zakudya zachinyengo.
Usadzitopetse wekha ndi kufuna chuma, ukhale ndi nzeru ya kudziretsa.
5 你岂要定睛在虚无的钱财上吗? 因钱财必长翅膀,如鹰向天飞去。
Ukangoti wachipeza chumacho uwona posachedwa kuti palibepo. Chumacho chimachita ngati chamera mapiko mwadzidzidzi ndi kuwuluka kunka kumwamba ngati chiwombankhanga.
Usadye chakudya cha munthu waumbombo, usalakalake zakudya zake zokoma;
7 因为他心怎样思量, 他为人就是怎样。 他虽对你说,请吃,请喝, 他的心却与你相背。
paja iye ndi munthu amene nthawi zonse amaganizira za mtengo wake ngakhale amati kwa iwe, “Idya ndi kumwa,” koma sakondweretsedwa nawe.
8 你所吃的那点食物必吐出来; 你所说的甘美言语也必落空。
Udzasanza zimene wadyazo ndipo mawu ako woyamikira adzapita pachabe.
9 你不要说话给愚昧人听, 因他必藐视你智慧的言语。
Usayankhule munthu wopusa akumva, pakuti adzanyoza mawu ako anzeru.
10 不可挪移古时的地界, 也不可侵入孤儿的田地;
Usasunthe mwala wa mʼmalire akalekale kapena kulowerera mʼminda ya ana amasiye,
11 因他们的救赎主大有能力, 他必向你为他们辨屈。
paja Mpulumutsi wawo ndi wamphamvu; iye adzawateteza pa milandu yawo kutsutsana nawe.
Mtima wako uzikhala pa malangizo ndipo makutu ako azimvetsera mawu a chidziwitso.
13 不可不管教孩童; 你用杖打他,他必不至于死。
Usaleke kumulangiza mwana; ngati umulanga ndi chikwapu sadzafa.
14 你要用杖打他, 就可以救他的灵魂免下阴间。 (Sheol )
Ukamukwapula ndi tsatsa udzapulumutsa moyo wake. (Sheol )
Mwana wanga, ngati mtima wako ukhala wanzeru, inenso mtima wanga udzakondwera.
Mtima wanga udzakondwera pamene ndidzakumva ukuyankhula zolungama.
Mtima wako usachite nsanje ndi anthu ochimwa, koma uziopa Yehova tsiku ndi tsiku.
Ndithu za mʼtsogolo zilipo ndipo chiyembekezo chakocho sichidzalephereka.
19 我儿,你当听,当存智慧, 好在正道上引导你的心。
Tamvera mwana wanga, ndipo ukhale wanzeru, mtima wako uwuyendetse mʼnjira yabwino.
Usakhale pakati pa anthu amene amaledzera kapena pakati pa anthu amene amadya nyama mwadyera.
21 因为好酒贪食的,必致贫穷; 好睡觉的,必穿破烂衣服。
Paja anthu oledzera ndi adyera amadzakhala amphawi ndipo aulesi adzavala sanza.
22 你要听从生你的父亲; 你母亲老了,也不可藐视她。
Mvera abambo ako amene anakubala, usanyoze amayi ako pamene akalamba.
23 你当买真理; 就是智慧、训诲,和聪明也都不可卖。
Gula choonadi ndipo usachigulitse; ugulenso nzeru, mwambo ndiponso kumvetsa zinthu bwino.
24 义人的父亲必大得快乐; 人生智慧的儿子,必因他欢喜。
Abambo a munthu wolungama ali ndi chimwemwe chachikulu; Wobala mwana wanzeru adzakondwera naye.
Abambo ndi amayi ako asangalale; amene anakubereka akondwere!
26 我儿,要将你的心归我; 你的眼目也要喜悦我的道路。
Mwana wanga, undikhulupirire ndipo maso ako apenyetsetse njira zanga.
Paja mkazi wachiwerewere ali ngati dzenje lozama; ndipo mkazi woyendayenda ali ngati chitsime chopapatiza.
Amabisala ngati mbala yachifwamba, ndipo amuna amakhala osakhulupirika chifukwa cha iyeyu.
29 谁有祸患?谁有忧愁? 谁有争斗?谁有哀叹? 谁无故受伤?谁眼目红赤?
Ndani ali ndi tsoka? Ndani ali ndi chisoni? Ndani ali pa mkangano? Ndani ali ndi madandawulo? Ndani ali ndi zipsera zosadziwika uko zachokera? Ndani ali ndi maso ofiira?
Ndi amene amakhalitsa pa mowa, amene amapita nalawa vinyo osakanizidwa.
31 酒发红,在杯中闪烁, 你不可观看, 虽然下咽舒畅, 终久是咬你如蛇,刺你如毒蛇。
Usatengeke mtima ndi kufiira kwa vinyo, pamene akuwira mʼchikho pamene akumweka bwino!
Potsiriza pake amaluma ngati njoka, ndipo amajompha ngati mphiri.
Maso ako adzaona zinthu zachilendo ndipo maganizo ndi mawu ako adzakhala osokonekera.
Udzakhala ngati munthu amene ali gone pakati pa nyanja, kapena ngati munthu wogona pa msonga ya mlongoti ya ngalawa.
35 你必说:人打我,我却未受伤; 人鞭打我,我竟不觉得。 我几时清醒,我仍去寻酒。
Iwe udzanena kuti, “Anandimenya, koma sindinapwetekedwe! Andimenya koma sindinamve kanthu! Kodi ndidzuka nthawi yanji? Ndiye ndifunefunenso vinyo wina.”