< 箴言 12 >
1 喜爱管教的,就是喜爱知识; 恨恶责备的,却是畜类。
Munthu amene amakonda mwambo amakonda kudziwa zinthu, koma amene amadana ndi chidzudzulo ndi wopusa.
2 善人必蒙耶和华的恩惠; 设诡计的人,耶和华必定他的罪。
Munthu wabwino amapeza kuyanja pamaso pa Yehova, koma Yehova amatsutsa munthu wochita chinyengo.
Munthu sangakhazikike bwino pochita zoyipa, koma maziko a anthu olungama sadzatekeseka.
4 才德的妇人是丈夫的冠冕; 贻羞的妇人如同朽烂在她丈夫的骨中。
Mkazi wakhalidwe labwino ali ngati chipewa chaufumu kwa mwamuna wake, koma mkazi wochititsa manyazi ali ngati chilonda cha mafinya kwa mwamuna wake.
Maganizo a anthu olungama ndi owongoka, koma malangizo a anthu oyipa ndi achinyengo.
6 恶人的言论是埋伏流人的血; 正直人的口必拯救人。
Mawu a anthu oyipa ndi ophetsa, koma mawu a anthu olungama amapulumutsa.
Anthu oyipa amagonjetsedwa ndipo amayiwalika, koma nyumba ya anthu olungama idzakhalabe.
8 人必按自己的智慧被称赞; 心中乖谬的,必被藐视。
Munthu amatamandidwa malinga ndi nzeru zake, koma anthu amitima yokhota amanyozedwa.
Nʼkwabwino kukhala munthu wonyozeka koma wodzigwirira ntchito nʼkukhala ndi zonse zofunika, kuposa kukhala wodzikuza koma ulibe ndi chakudya chomwe.
Munthu wolungama amasamalira moyo wa ziweto zake, koma chifundo cha munthu woyipa ndi chakhanza.
11 耕种自己田地的,必得饱食; 追随虚浮的,却是无知。
Wolima mʼmunda mwake mwakhama adzakhala ndi chakudya chochuluka, koma wotsata zopanda pake alibe nzeru.
Munthu woyipa amalakalaka zofunkha za anthu oyipa, koma mizu ya anthu olungama imabereka zipatso.
13 恶人嘴中的过错是自己的网罗; 但义人必脱离患难。
Munthu woyipa amakodwa mu msampha wa mayankhulidwe ake oyipa; koma munthu wolungama amatuluka mʼmavuto.
14 人因口所结的果子,必饱得美福; 人手所做的,必为自己的报应。
Munthu amakhala ndi zabwino zambiri chifukwa cha mawu ake ndipo ntchito zimene munthu agwira ndi manja ake zimamupindulira.
15 愚妄人所行的,在自己眼中看为正直; 惟智慧人肯听人的劝教。
Zochita za chitsiru mwini wakeyo amaziona ngati zabwino, koma munthu wanzeru amamvera malangizo.
Mkwiyo wa chitsiru umadziwika nthawi yomweyo, koma munthu wanzeru sasamala kunyozedwa.
17 说出真话的,显明公义; 作假见证的,显出诡诈。
Woyankhula zoona amapereka umboni woona, koma mboni yabodza imafotokoza zonama.
18 说话浮躁的,如刀刺人; 智慧人的舌头却为医人的良药。
Munthu woyankhula mosasamala mawu ake amalasa ngati lupanga, koma mawu a munthu wanzeru amachiritsa.
Mawu woona amakhala mpaka muyaya koma mawu abodza sakhalitsa.
20 图谋恶事的,心存诡诈; 劝人和睦的,便得喜乐。
Mʼmitima ya anthu amene amakonza zoyipa muli chinyengo; koma anthu olimbikitsa za mtendere amakhala ndi chimwemwe.
Palibe choyipa chimene chimagwera munthu wolungama, koma munthu woyipa mavuto samuthera.
22 说谎言的嘴为耶和华所憎恶; 行事诚实的,为他所喜悦。
Pakamwa pa bodza pamamunyansa Yehova, koma amakondwera ndi anthu oyankhula zoona.
Munthu wochenjera amabisa nzeru zake, koma munthu wopusa amaonetsa uchitsiru wake poyera.
Ogwira ntchito mwakhama adzalamulira, koma aulesi adzakhala ngati kapolo.
Nkhawa imakhala ngati katundu wolemera mu mtima mwa munthu, koma mawu abwino amamusangalatsa.
Munthu wolungama amatsogolera mnansi wake, koma ntchito za anthu oyipa zimawasocheretsa.
27 懒惰的人不烤打猎所得的; 殷勤的人却得宝贵的财物。
Munthu waulesi sapeza chimene akufuna, koma munthu wakhama amapeza chuma chamtengo wapatali.
Mʼnjira yachilungamo muli moyo; koma njira ya munthu woyipa imafikitsa ku imfa.