< 民数记 26 >
1 瘟疫之后,耶和华晓谕摩西和祭司亚伦的儿子以利亚撒说:
Utatha mliri Yehova anati kwa Mose ndi Eliezara mwana wa Aaroni,
2 “你们要将以色列全会众,按他们的宗族,凡以色列中从二十岁以外、能出去打仗的,计算总数。”
“Werengani Aisraeli onse mwa mabanja awo, onse a zaka makumi awiri kapena kuposera pamenepo omwe angathe kugwira ntchito ya usilikali mʼgulu lankhondo la Israeli.”
3 摩西和祭司以利亚撒在摩押平原与耶利哥相对的约旦河边向以色列人说:
Kotero mu zigwa za Mowabu pafupi ndi mtsinje wa Yorodani ku Yeriko, Mose ndi wansembe Eliezara anayankhula nawo kuti,
4 “将你们中间从二十岁以外的计算总数”;是照耶和华吩咐出埃及地的摩西和以色列人的话。
“Werengani amuna a zaka makumi awiri kapena kuposera pamenepo, monga momwe Yehova walamulira Mose.” Aisraeli omwe anachokera ku Igupto ndi awa:
5 以色列的长子是吕便。吕便的众子:属哈诺的,有哈诺族;属法路的,有法路族;
Zidzukulu za Rubeni, mwana woyamba wamwamuna wa Israeli, zinali izi: kuchokera mwa Hanoki, fuko la Ahanoki; kuchokera mwa Palu, fuko la Apalu;
kuchokera mwa Hezironi, fuko la Ahezironi; kuchokera mwa Karimi, fuko la Akarimi.
7 这就是吕便的各族;其中被数的,共有四万三千七百三十名。
Awa anali mafuko a Rubeni: onse amene anawerengedwa analipo 43,730.
Mwana wa Palu anali Eliabu,
9 以利押的众子是尼母利、大坍、亚比兰。这大坍、亚比兰,就是从会中选召的,与可拉一党同向耶和华争闹的时候也向摩西、亚伦争闹;
ndipo ana a Eliabu anali Nemueli, Datani ndi Abiramu. Datani ndi Abiramu anali gulu la akuluakulu aja amene anawukira Mose ndi Aaroni ndipo analinso mʼgulu la otsatira Kora pamene anawukira Yehova.
10 地便开口吞了他们,和可拉、可拉的党类一同死亡。那时火烧灭了二百五十个人;他们就作了警戒。
Nthaka inangʼambika ndi kuwameza pamodzi ndi Kora, kotero kuti gulu lawo linafa pamene moto unapsereza anthu 250 aja, nasanduka chenjezo.
Koma ana a Kora sanafe nawo.
12 按着家族,西缅的众子:属尼母利的,有尼母利族;属雅悯的,有雅悯族;属雅斤的,有雅斤族;
Zidzukulu za Simeoni mwa mafuko awo zinali izi: kuchokera mwa Nemueli, fuko la Anemuele; kuchokera mwa Yamini, fuko la Ayamini; kuchokera mwa Yakini fuko la Ayakini;
kuchokera mwa Zera, mbumba ya Zera; kuchokera mwa Sauli, fuko la Asauli.
Awa anali mafuko a Simeoni. Iwowa analipo amuna 22,200.
15 按着家族,迦得的众子:属洗分的,有洗分族;属哈基的,有哈基族;属书尼的,有书尼族;
Zidzukulu za Gadi mwa mafuko awo ndi izi: kuchokera mwa Zefoni, fuko la Azefoni; kuchokera mwa Hagi, fuko la Ahagi; kuchokera mwa Suni, fuko la Asuni;
16 属阿斯尼的,有阿斯尼族;属以利的,有以利族;
kuchokera mwa Ozini, fuko la Aozini; kuchokera mwa Eri, fuko la Aeri;
17 属亚律的,有亚律族;属亚列利的,有亚列利族。
kuchokera mwa Arodi, fuko la Aarodi; kuchokera mwa Arieli, fuko la a Areli.
18 这就是迦得子孙的各族,照他们中间被数的,共有四万零五百名。
Awa ndiwo anali mafuko a Gadi. Onse amene anawerengedwa analipo 40,500.
19 犹大的儿子是珥和俄南。这珥和俄南死在迦南地。
Eri ndi Onani anali ana aamuna a Yuda, koma anafera mu Kanaani.
20 按着家族,犹大其余的众子:属示拉的,有示拉族;属法勒斯的,有法勒斯族;属谢拉的有谢拉族。
Zidzukulu za Yuda monga mwa mafuko awo zinali izi: kuchokera mwa Sela, fuko la Asera; kuchokera mwa Perezi, fuko la Aperezi; kuchokera mwa Zera, mbumba ya Zera.
21 法勒斯的儿子:属希斯 的,有希斯 族;属哈母勒的,有哈母勒族。
Zidzukulu za Perezi zinali izi: kuchokera mwa Hezironi, fuko la Ahezironi; kuchokera mwa Hamuli, fuko la Ahamuli.
22 这就是犹大的各族,照他们中间被数的,共有七万六千五百名。
Awa ndiwo anali mafuko a Yuda. Amene anawerenga analipo 76,500.
23 按着家族,以萨迦的众子:属陀拉的,有陀拉族;属普瓦的,有普瓦族;
Zidzukulu za Isakara monga mwa mafuko awo zinali izi: kuchokera mwa Tola, fuko la Atola; kuchokera mwa Puwa, fuko la Apuwa;
kuchokera mwa Yasubu, fuko la Ayasubu. Kuchokera mwa Simironi, fuko la Asimironi.
25 这就是以萨迦的各族,照他们中间被数的,共有六万四千三百名。
Awa ndi amene anali a fuko la Isakara. Amene anawerengedwa analipo 64,300.
26 按着家族,西布伦的众子:属西烈的,有西烈族;属以伦的,有以伦族;属雅利的,有雅利族。
Zidzukulu za Zebuloni mwa mafuko awo zinali izi: kuchokera mwa Seredi, fuko la Aseredi; kuchokera mwa Eloni, fuko la Aeloni; kuchokera mwa Yahaleeli, fuko la Ayahaleeli.
27 这就是西布伦的各族,照他们中间被数的,共有六万零五百名。
Awa ndiwo anali mafuko a Zebuloni. Amene anawerengedwa analipo 60,500.
Zidzukulu za Yosefe mwa mafuko awo kupyolera mwa Manase ndi Efereimu zinali izi:
29 玛拿西的众子:属玛吉的,有玛吉族;玛吉生基列;属基列的,有基列族。
Zidzukulu za Manase: kuchokera mwa Makiri, fuko la Amakiri (Makiri anali abambo ake a Giliyadi); kuchokera mwa Giliyadi, fuko la Agiliyadi.
30 基列的众子:属伊以谢的,有伊以谢族;属希勒的,有希勒族;
Izi ndizo zinali zidzukulu za Giliyadi; kuchokera mwa Iyezeri, fuko la Aiyezeri; kuchokera mwa Heleki, fuko la Aheleki;
31 属亚斯烈的,有亚斯烈族;属示剑的,有示剑族;
kuchokera mwa Asirieli, fuko la Aasirieli; kuchokera mwa Sekemu, fuko la Asekemu;
32 属示米大的,有示米大族;属希弗的,有希弗族。
kuchokera mwa Semida, fuko la Asemida; kuchokera mwa Heferi, fuko la Aheferi.
33 希弗的儿子:西罗非哈没儿子,只有女儿。西罗非哈女儿的名字就是玛拉、挪阿、曷拉、密迦、得撒。
(Zelofehadi mwana wa Heferi analibe ana aamuna koma ana aakazi okha, amene mayina awo anali: Mala, Nowa, Hogila, Milika ndi Tiriza.)
34 这就是玛拿西的各族;他们中间被数的,共有五万二千七百名。
Awa ndiwo anali mafuko a Manase. Amene anawerengedwa analipo 52,700.
35 按着家族,以法莲的众子:属书提拉的,有书提拉族;属比结的,有比结族;属他罕的,有他罕族。
Zidzukulu za Efereimu monga mwa mafuko awo zinali izi; kuchokera mwa Sutela, fuko la Asutela; kuchokera mwa Bekeri, fuko la Abekeri; kuchokera mwa Tahani, fuko la Atahani.
Zidzukulu za Sutela zinali izi: kuchokera mwa Erani, fuko la Aerani.
37 这就是以法莲子孙的各族,照他们中间被数的,共有三万二千五百名。按着家族,这都是约瑟的子孙。
Awa ndiwo anali mafuko a Efereimu. Amene anawerengedwa analipo 32,500. Zimenezi zinali zidzukulu za Yosefe monga mwa mafuko awo.
38 按着家族,便雅悯的众子:属比拉的,有比拉族;属亚实别的,有亚实别族;属亚希兰的,有亚希兰族;
Zidzukulu za Benjamini monga mwa mabanja awo zinali izi: kuchokera mwa Bela, fuko la Abela; kuchokera mwa Asibeli, fuko la Aasibeli; kuchokera mwa Ahiramu, fuko la Ahiramu;
kuchokera mwa Sufamu, fuko la Asufamu; kuchokera mwa Hufamu, fuko la Ahufamu;
40 比拉的众子是亚勒、乃幔。属 亚勒 的,有亚勒族;属乃幔的,有乃幔族。
Zidzukulu za Bela kupyolera mwa Aridi ndi Naamani zinali izi: kuchokera mwa Aridi, fuko la Aaridi; kuchokera mwa Naamani, fuko la Anaamani;
41 按着家族,这就是便雅悯的子孙,其中被数的,共有四万五千六百名。
Awa ndiwo anali mabanja a Benjamini. Amene nawerengedwa analipo 45,600.
42 按着家族,但的众子:属书含的,有书含族。按着家族,这就是但的各族。
Zidzukulu za Dani mwa mabanja awo zinali izi: kuchokera mwa Suhamu fuko la Asuhamu. Izi zinali zidzukulu za Dani.
43 照其中被数的,书含所有的各族,共有六万四千四百名。
Onse a fuko la Asuhamu amene anawerengedwa analipo 64,400.
44 按着家族,亚设的众子:属音拿的,有音拿族;属亦施韦的,有亦施韦族;属比利亚的,有比利亚族。
Zidzukulu za Aseri monga mwa mafuko awo zinali izi: kuchokera mwa Imina, fuko la Aimuna; kuchokera mwa Isivi, fuko la Ayisivi; kuchokera mwa Beriya, fuko la Aberiya;
45 比利亚的众子:属希别的,有希别族;属玛结的,有玛结族。
ndipo kupyolera mwa zidzukulu za Beriya: kuchokera mwa Heberi, fuko la Aheberi; kuchokera mwa Malikieli, fuko la Amalikieli;
(Aseri anali ndi mwana wamkazi dzina lake Sera)
47 这就是亚设子孙的各族,照他们中间被数的,共有五万三千四百名。
Awa ndiwo anali mafuko a Aseri. Onse amene anawerengedwa analipo 53,400.
48 按着家族,拿弗他利的众子:属雅薛的,有雅薛族;属沽尼的,有沽尼族;
Zidzukulu za Nafutali mwa mafuko awo zinali izi: kuchokera mwa Yahazeeli, fuko la Ayahazeeli; kuchokera mwa Guni, fuko la Aguni;
kuchokera mwa Yezeri, fuko la Ayezeri; kuchokera mwa Silemu, fuko la Asilemu.
50 按着家族,这就是拿弗他利的各族;他们中间被数的,共有四万五千四百名。
Awa ndiwo anali mafuko a Nafutali. Onse amene anawerengedwa analipo 45,400.
51 以色列人中被数的,共有六十万零一千七百三十名。
Chiwerengero chonse cha amuna mu Israeli chinalipo 601,730.
Yehova anawuza Mose kuti,
“Uwagawire dziko anthu awa kuti likhale cholowa chawo molingana ndi chiwerengero cha mayina awo.
54 人多的,你要把产业多分给他们;人少的,你要把产业少分给他们;要照被数的人数,把产业分给各人。
Gulu lalikulu ulipatse cholowa chachikulu, ndipo lochepa cholowa chocheperapo. Gulu lililonse lilandire cholowa chake molingana ndi chiwerengero cha amene anawerengedwa.
55 虽是这样,还要拈阄分地。他们要按着祖宗各支派的名字承受为业。
Dzikolo uligawe pochita maere. Alandire cholowa chawocho potsata mayina a mafuko a makolo awo.
56 要按着所拈的阄,看人数多,人数少,把产业分给他们。”
Cholowa chawo uchigawe pakati pa fuko lalikulu ndi lalingʼono mwa maere.”
57 利未人,按着他们的各族被数的:属革顺的,有革顺族;属哥辖的,有哥辖族;属米拉利的,有米拉利族。
Alevi omwe anawerengedwa monga mwa mafuko awo ndi awa: kuchokera mwa Geresoni, fuko la Ageresoni; kuchokera mwa Kohati, fuko la Akohati; kuchokera mwa Merari, fuko la Amerari.
58 利未的各族有立尼族、希伯伦族、玛利族、母示族、可拉族。哥辖生暗兰。
Awanso anali mabanja a Alevi: banja la Alibini, banja la Ahebroni, banja la Amali, banja la Amusi, fuko la Kora banja la Akohati, (Kohati anali abambo a Amramu.
59 暗兰的妻名叫约基别,是利未女子,生在埃及。她给暗兰生了亚伦、摩西,并他们的姊姊米利暗。
Dzina la mkazi wa Amramu linali Yokobedi, mdzukulu wa Levi, yemwe anabadwa mwa Alevi mu Igupto. Yokobedi anaberekera Amramu Aaroni, Mose ndi Miriamu mlongo wawo.
Aaroni anali abambo a Nadabu, Abihu, Eliezara ndi Itamara.
61 拿答、亚比户在耶和华面前献凡火的时候就死了。
Koma Nadabu ndi Abihu anafa pamene anapereka nsembe pamaso pa Yehova ndi moto wachilendo).
62 利未人中,凡一个月以外、被数的男丁,共有二万三千。他们本来没有数在以色列人中;因为在以色列人中,没有分给他们产业。
Alevi onse aamuna a mwezi umodzi kapena kuposera pamenepa analipo 23,000. Iwowo sanawerengedwe pamodzi ndi Aisraeli ena chifukwa sanalandire cholowa pakati pawo.
63 这些就是被摩西和祭司以利亚撒所数的;他们在摩押平原与耶利哥相对的约旦河边数点以色列人。
Awa ndi amene anawerengedwa ndi Mose ndi Eliezara wansembe pamene ankawerenga Aisraeli pa zigwa za ku Mowabu mʼmbali mwa Yorodani ku Yeriko.
64 但被数的人中,没有一个是摩西和祭司亚伦从前在西奈的旷野所数的以色列人,
Mwa anthu amenewa panalibe ndi mmodzi yemwe amene anali mʼgulu la Aisraeli omwe Mose ndi wansembe Aaroni anawawerenga mʼchipululu cha Sinai;
65 因为耶和华论到他们说:“他们必要死在旷野。”所以,除了耶孚尼的儿子迦勒和嫩的儿子约书亚以外,连一个人也没有存留。
Chifukwa Yehova anali atawuza Aisraeliwo kuti adzafera ndithu mʼchipululu, ndipo palibe ndi mmodzi yemwe amene anatsala kupatula Kalebe mwana wa Yefune ndi Yoswa mwana wa Nuni.