< 民数记 23 >

1 巴兰对巴勒说:“你在这里给我筑七座坛,为我预备七只公牛,七只公羊。”
Balaamu anati kwa Balaki, “Mundimangire maguwa ansembe asanu ndi awiri pano, ndipo mukonzenso ngʼombe zazimuna zisanu ndi ziwiri ndi nkhosa zazimuna zisanu ndi ziwiri.”
2 巴勒照巴兰的话行了。巴勒和巴兰在每座坛上献一只公牛,一只公羊。
Balaki anachita monga Balaamu ananenera ndipo awiriwo anapereka ngʼombe imodzi ndi nkhosa yayimuna imodzi pa guwa lansembe lililonse.
3 巴兰对巴勒说:“你站在你的燔祭旁边,我且往前去,或者耶和华来迎见我。他指示我什么,我必告诉你。”于是巴兰上一净光的高处。
Kenaka Balaamu anati kwa Balaki, “Khalani pano pafupi ndi nsembe yanu ineyo ndipite pambali. Mwina Yehova adzabwera kuti akumane nane. Chilichonse chimene akandionetse ndidzakuwuzani” Choncho anapita ku malo okwera a chipululu.
4 神迎见巴兰;巴兰说:“我预备了七座坛,在每座坛上献了一只公牛,一只公羊。”
Mulungu anakumana naye ndipo Balaamu anati, “Ndakonza maguwa asanu ndi awiri ndipo pa guwa lililonse ndaperekapo nsembe ya ngʼombe yayimuna imodzi ndi nkhosa yayimuna imodzinso.”
5 耶和华将话传给巴兰,又说:“你回到巴勒那里,要如此如此说。”
Yehova anawuza Balaamu kuti, “Bwerera kwa Balaki ndipo ukamuwuze uthenga uwu.”
6 他就回到巴勒那里,见他同摩押的使臣都站在燔祭旁边。
Ndipo anabwerera kwa iye namupeza atayima pafupi ndi nsembe yake pamodzi ndi akuluakulu onse a Mowabu.
7 巴兰便题起诗歌说: 巴勒引我出亚兰, 摩押王引我出东山,说: 来啊,为我咒诅雅各; 来啊,怒骂以色列。
Ndipo Balaamu ananena uthenga wake: “Balaki ananditenga kuchoka ku Aramu, mfumu ya ku Mowabu kuchokera ku mapiri a kummawa. Iye anati, ‘Bwera, temberera Yakobo mʼmalo mwanga, pita nyoza Israeli.’
8 神没有咒诅的,我焉能咒诅? 耶和华没有怒骂的,我焉能怒骂?
Ndingatemberere bwanji amene Mulungu sanawatemberere? Ndinganyoze bwanji amene Yehova sanawanyoze?
9 我从高峰看他,从小山望他; 这是独居的民,不列在万民中。
Kuchokera pamwamba pa mapiri ndikuona anthu, ndikuwaona kuchokera pa zitunda. Ndikuona anthu okhala pawokha, osakhala mʼgulu limodzi ndi mitundu ina.
10 谁能数点雅各的尘土? 谁能计算以色列的四分之一? 我愿如义人之死而死; 我愿如义人之终而终。
Ndani angawerenge zidzukulu za Yakobo zochuluka ngati fumbi, kapena chimodzi mwa zigawo zinayi za Israeli? Lekeni ndife imfa ya oyera mtima, ndi chimaliziro changa chikhale ngati chawo!”
11 巴勒对巴兰说:“你向我做的是什么事呢?我领你来咒诅我的仇敌,不料,你竟为他们祝福。”
Balaki anati kwa Balaamu, “Wandichitira chiyani? Ndinakuyitana kuti utemberere adani anga, ndipo taona, sunachite chilichonse koma kuwadalitsa!”
12 他回答说:“耶和华传给我的话,我能不谨慎传说吗?”
Iye anayankha kuti, “Kodi sindinayenera kuyankhula zimene Yehova anandiwuza?”
13 巴勒说:“求你同我往别处去,在那里可以看见他们;你不能全看见,只能看见他们边界上的人。在那里要为我咒诅他们。”
Kenaka Balaki anawuza Balaamu kuti, “Tiye tipite limodzi ku malo ena komwe ungawaone. Udzangoona gulu limodzi osati onsewo. Ndipo pamenepo, ukawatemberere mʼmalo mwanga.”
14 于是领巴兰到了琐腓田,上了毗斯迦山顶,筑了七座坛;每座坛上献一只公牛,一只公羊。
Tsono anamutengera ku munda wa Zofimu pamwamba pa phiri la Pisiga ndipo kumeneko anamanga maguwa ansembe asanu ndi awiri ndipo anapereka nsembe ngʼombe yayimuna imodzi ndi nkhosa yayimuna imodzi pa guwa lansembe lililonse.
15 巴兰对巴勒说:“你站在这燔祭旁边,等我往那边去迎见耶和华。”
Balaamu anawuza Balaki kuti, “Khalani pano pafupi ndi nsembe yanu pamene ine ndikukakumana ndi Mulungu cha uko.”
16 耶和华临到巴兰那里,将话传给他;又说:“你回到巴勒那里,要如此如此说。”
Yehova anakumana ndi Balaamu ndipo anamuyankhula kuti, “Bwerera kwa Balaki ndipo ukamuwuze uthenga uwu.”
17 他就回到巴勒那里,见他站在燔祭旁边;摩押的使臣也和他在一处。巴勒问他说:“耶和华说了什么话呢?”
Ndipo anapita kwa iye ndipo anamupeza atayimirira pafupi ndi nsembe yake pamodzi ndi akuluakulu a ku Mowabu. Balaki anafunsa Balaamu kuti, “Yehova wayankhula chiyani?”
18 巴兰就题诗歌说: 巴勒,你起来听; 西拨的儿子,你听我言。
Pamenepo Balaamu ananena uthenga wake: “Nyamuka Balaki ndipo tamvera; Undimvere iwe mwana wa Zipori.
19 神非人,必不致说谎, 也非人子,必不致后悔。 他说话岂不照着行呢? 他发言岂不要成就呢?
Mulungu si munthu kuti aname, kapena mwana wa munthu kuti asinthe maganizo ake. Kodi amayankhula koma osachita? Kodi amalonjeza koma osakwaniritsa?
20 我奉命祝福; 神也曾赐福,此事我不能翻转。
Wandilamula kuti ndidalitse, Iyeyo wadalitsa ndipo sindingasinthe.
21 他未见雅各中有罪孽, 也未见以色列中有奸恶。 耶和华—他的 神和他同在; 有欢呼王的声音在他们中间。
“Palibe kuwukira kulikonse kumene wakuona mwa Yakobo, sanaone chovuta mu Israeli. Yehova Mulungu wawo ali nawo: mfuwu wa mfumu uli pakati pawo.
22 神领他们出埃及; 他们似乎有野牛之力。
Mulungu wowatulutsa mʼdziko la Igupto, ali ndi mphamvu ngati za njati.
23 断没有法术可以害雅各, 也没有占卜可以害以色列。 现在必有人论及雅各,就是论及以色列说: 神为他行了何等的大事!
Palibe matsenga amene angalimbane ndi Yakobo, palibe mawula amene angalimbane ndi Israeli. Tsopano za Yakobo ndi Israeli adzanena kuti, ‘Onani zimene Mulungu wachita!’
24 这民起来,仿佛母狮, 挺身,好像公狮, 未曾吃野食, 未曾喝被伤者之血,决不躺卧。
Taonani, anthu anyamuka ngati mkango waukazi; adzuka okha ngati mkango waumuna umene supuma mpaka utadya nyama imene wagwira ndi kumwa magazi a nyama yogwidwayo.”
25 巴勒对巴兰说:“你一点不要咒诅他们,也不要为他们祝福。”
Ndipo Balaki anati kwa Balaamu, “Usawatemberere ndi pangʼono pomwe kapena kuwadalitsa!
26 巴兰回答巴勒说:“我岂不是告诉你说‘凡耶和华所说的,我必须遵行’吗?”
“Balaamu anayankha Balaki kuti, ‘Kodi sindinakuwuzeni kuti ndiyenera kuchita zimene Yehova wanena?’”
27 巴勒对巴兰说:“来吧,我领你往别处去,或者 神喜欢你在那里为我咒诅他们。”
Kenaka Balaki anati kwa Balaamu, “Bwera ndikutengere ku malo ena. Mwina chidzamukondweretsa Mulungu kuti uwatemberere kumeneko mʼmalo mwanga.”
28 巴勒就领巴兰到那下望旷野的毗珥山顶上。
Ndipo Balaki anamutengera Balaamu pamwamba pa Peori, poyangʼanana ndi chipululu.
29 巴兰对巴勒说:“你在这里为我筑七座坛,又在这里为我预备七只公牛,七只公羊。”
Balaamu anati kwa Balaki, “Mundimangire maguwa ansembe asanu ndi awiri pano ndipo mundikonzere ngʼombe zazimuna zisanu ndi ziwiri, nkhosa zazimuna zisanu ndi ziwiri.”
30 巴勒就照巴兰的话行,在每座坛上献一只公牛,一只公羊。
Balaki anachita monga Balaamu ananenera ndipo anapereka nsembe ngʼombe imodzi yayimuna ndi nkhosa imodzi yayimuna pa guwa lililonse.

< 民数记 23 >