< 尼希米记 8 >

1 到了七月,以色列人住在自己的城里。那时,他们如同一人聚集在水门前的宽阔处,请文士以斯拉将耶和华借摩西传给以色列人的律法书带来。
Anthu onse anasonkhana ngati munthu mmodzi pabwalo limene lili patsogolo pa Chipata cha Madzi. Iwo anawuza mlembi Ezara kuti abwere ndi buku la malamulo a Mose limene Yehova anapereka kwa Aisraeli.
2 七月初一日,祭司以斯拉将律法书带到听了能明白的男女会众面前。
Choncho pa tsiku loyamba la mwezi wachisanu ndi chiwiri wansembe Ezara, anabwera ndi buku la malamulo ku msonkhano wa amuna, akazi ndi ana onse amene ankatha kumvetsa zinthu bwino.
3 在水门前的宽阔处,从清早到晌午,在众男女、一切听了能明白的人面前读这律法书。众民侧耳而听。
Choncho Ezara anawerenga bukulo atayangʼana bwalo la Chipata cha Madzi kuyambira mmawa mpaka masana pamaso pa amuna, akazi ndi onse amene ankamvetsa bwino zinthu. Ndipo anthu onse anatchera khutu kuti amve malamulowo.
4 文士以斯拉站在为这事特备的木台上。玛他提雅、示玛、亚奈雅、乌利亚、希勒家,和玛西雅站在他的右边;毗大雅、米沙利、玛基雅、哈顺、哈拔大拿、撒迦利亚,和米书兰站在他的左边。
Mlembi Ezara anayimirira pa nsanja ya mitengo imene anthu anamanga chifukwa cha msonkhanowu. Ku dzanja lake lamanja kunayimirira Matitiya, Sema, Anaya, Uriya, Hilikiya ndi Maaseya, ndipo kudzanja lake lamanzere kunali Pedaya, Misaeli, Malikiya, Hasumu, Hasibadana, Zekariya ndi Mesulamu.
5 以斯拉站在众民以上,在众民眼前展开这书。他一展开,众民就都站起来。
Tsono Ezara anatsekula buku, akuona popeza anayima pa nsanja. Pamene anafutukula bukulo anthu onse anayimirira.
6 以斯拉称颂耶和华至大的 神;众民都举手应声说:“阿们!阿们!”就低头,面伏于地,敬拜耶和华。
Ezara anatamanda Yehova, Mulungu wamkulu, ndipo anthu onse anakweza manja awo ndi kuyankha kuti, “Ameni, ameni.” Pambuyo pake onse anaweramitsa pansi mitu yawo napembedza Yehova akanali chizolikire choncho.
7 耶书亚、巴尼、示利比、雅悯、亚谷、沙比太、荷第雅、玛西雅、基利他、亚撒利雅、约撒拔、哈难、毗莱雅,和利未人使百姓明白律法;百姓都站在自己的地方。
Anthuwo atayimiriranso Alevi awa: Yesuwa, Bani, Serebiya, Yamini, Akubu, Sabetayi, Hodiya, Maaseya, Kerita, Azariya, Yozabadi, Hanani ndi Pelaya anawathandiza kuti amvetse bwino malamulowo.
8 他们清清楚楚地念 神的律法书,讲明意思,使百姓明白所念的。
Iwo anawerenga buku la malamulo a Mulungu momveka bwino ndi kutanthauzira mawuwo kuti anthu amvetse bwino zowerengedwazo.
9 省长尼希米和作祭司的文士以斯拉,并教训百姓的利未人,对众民说:“今日是耶和华—你们 神的圣日,不要悲哀哭泣。”这是因为众民听见律法书上的话都哭了;
Tsono bwanamkubwa Nehemiya pamodzi ndi wansembe ndi mlembi Ezara komanso Alevi amene amaphunzitsa anthu anati kwa anthu onse, “Lero ndi tsiku lopatulika kwa Yehova Mulungu wanu. Musakhale ndi chisoni ndipo musalire.” Anayankhula choncho popeza anthu onse ankalira atamva mawu a buku la malamulo lija.
10 又对他们说:“你们去吃肥美的,喝甘甜的,有不能预备的就分给他,因为今日是我们主的圣日。你们不要忧愁,因靠耶和华而得的喜乐是你们的力量。”
Nehemiya anatinso, “Pitani, kachiteni phwando ku nyumba ndipo mukawagawireko ena amene alibe kanthu kalikonse popeza lero ndi tsiku lopatulika kwa Yehova. Musakhale ndi chisoni, pakuti chimwemwe cha Yehova ndiye mphamvu yanu.”
11 于是利未人使众民静默,说:“今日是圣日;不要作声,也不要忧愁。”
Alevi anakhalitsa bata anthu onse powawuza kuti, “Khalani chete, pakuti lero ndi tsiku lopatulika ndipo musakhale ndi chisoni.”
12 众民都去吃喝,也分给人,大大快乐,因为他们明白所教训他们的话。
Anthu onse anachoka kupita kukadya ndi kumwa. Chakudya china anatumiza kwa anzawo. Choncho panali chikondwerero chachikulu popeza tsopano anali atamvetsa bwino mawu a Mulungu amene anawawerengera ndi kuwafotokozerawo.
13 次日,众民的族长、祭司,和利未人都聚集到文士以斯拉那里,要留心听律法上的话。
Mmawa mwake atsogoleri a mabanja pamodzi ndi ansembe ndi alevi anasonkhana kwa Ezara, mlembi wa malamulo kuti aphunzire mawu a malamulowo.
14 他们见律法上写着,耶和华借摩西吩咐以色列人要在七月节住棚,
Tsono anapeza kuti zinalembedwa mʼbuku la malamulo kuti Yehova analamula kudzera mwa Mose kuti Aisraeli azikhala mʼzithando pa nthawi yonse ya chikondwerero cha mwezi wachisanu ndi chiwiri.
15 并要在各城和耶路撒冷宣传报告说:“你们当上山,将橄榄树、野橄榄树、番石榴树、棕树,和各样茂密树的枝子取来,照着所写的搭棚。”
Choncho analengeza ndi kufalitsa mʼmizinda yawo yonse ndi mu Yerusalemu kuti, “Pitani ku phiri mukadule nthambi za mtengo wa olivi, za mtengo wa olivi wa kutchire, za mtengo wa mchisu, za mtengo wa mgwalangwa ndiponso za mitengo ina ya masamba, zomangira zithando monga zalembedweramu ndi kubwera nazo.”
16 于是百姓出去,取了树枝来,各人在自己的房顶上,或院内,或 神殿的院内,或水门的宽阔处,或以法莲门的宽阔处搭棚。
Choncho anthu anapita kukatenga nthambi ndipo aliyense anadzimangira misasa pa denga ya nyumba yake, mʼmabwalo awo, mʼmabwalo a Nyumba ya Mulungu, mʼbwalo la pa Chipata cha Madzi ndiponso mʼbwalo la pa Chipata cha Efereimu.
17 从掳到之地归回的全会众就搭棚,住在棚里。从嫩的儿子约书亚的时候直到这日,以色列人没有这样行。于是众人大大喜乐。
Gulu lonse la anthu limene linabwera ku ukapolo linamanga misasa ndipo linakhala mʼmenemo. Kuyambira nthawi ya Yoswa mwana wa Nuni mpaka tsiku limenelo nʼkuti Aisraeli asanachitepo zimenezi. Choncho panali chimwemwe chachikulu.
18 从头一天直到末一天,以斯拉每日念 神的律法书。众人守节七日,第八日照例有严肃会。
Tsiku ndi tsiku, kuyambira tsiku loyamba mpaka lomaliza, Ezara ankawerenga buku la malamulo a Mulungu. Anthu anachita chikondwerero masiku asanu ndi awiri. Pa tsiku lachisanu ndi chitatu panachitika msonkhano potsata buku la malamulo lija.

< 尼希米记 8 >