< 尼希米记 13 >

1 当日,人念摩西的律法书给百姓听,遇见书上写着说,亚扪人和摩押人永不可入 神的会;
Pa tsiku limenelo anawerenga buku la Mose anthu akumva. Ndipo anapeza mawu akuti, Mwamoni kapena Mmowabu asalowe konse mu msonkhano wa Mulungu.
2 因为他们没有拿食物和水来迎接以色列人,且雇了巴兰咒诅他们,但我们的 神使那咒诅变为祝福。
Paja iwowa sanawachingamire Aisraeli kukawapatsa chakudya ndi madzi. Mʼmalo mwake analemba ganyu Baalamu kuti adzawatemberere. Komabe Mulungu wathu anasandutsa tembererolo kukhala mdalitso.
3 以色列民听见这律法,就与一切闲杂人绝交。
Anthu atamva lamuloli, anachotsa pakati pawo onse amene anali achilendo.
4 先是蒙派管理我们 神殿中库房的祭司以利亚实与多比雅结亲,
Izi zisanachitike, wansembe Eliyasibu anali atasankhidwa kukhala woyangʼanira zipinda zosungiramo katundu za Nyumba ya Mulungu. Iyeyu ankagwirizana kwambiri ndi Tobiya.
5 便为他预备一间大屋子,就是从前收存素祭、乳香、器皿,和照命令供给利未人、歌唱的、守门的五谷、新酒,和油的十分之一,并归祭司举祭的屋子。
Choncho anamupatsa chipinda chachikulu chimene kale ankasungamo zopereka zakudya, lubani, ziwiya, zopereka za chakhumi za tirigu, vinyo ndi mafuta zoyenera kuperekedwa kwa Alevi, oyimba nyimbo ndi alonda a ku Nyumba ya Mulungu, komanso mphatso zoyenera kupereka kwa ansembe.
6 那时我不在耶路撒冷;因为巴比伦王亚达薛西三十二年,我回到王那里。过了多日,我向王告假。
Koma pamene izi zonse zinkachitika mu Yerusalemu, ine kunalibe popeza mʼchaka cha 32 cha Aritasasita mfumu ya Babuloni ine ndinabwerera kwa mfumu. Patapitanso nthawi ndinapempha chilolezo kwa mfumuyo
7 我来到耶路撒冷,就知道以利亚实为多比雅在 神殿的院内预备屋子的那件恶事。
ndipo ndinabwerera ku Yerusalemu. Kumeneko ndinamva za chinthu choyipa chimene Eliyasibu anachita pomupatsa Tobiya chipinda mʼbwalo la Nyumba ya Mulungu.
8 我甚恼怒,就把多比雅的一切家具从屋里都抛出去,
Ndinapsa mtima kwambiri ndipo ndinataya kunja katundu yense wa Tobiya amene anali mʼchipindamo.
9 吩咐人洁净这屋子,遂将 神殿的器皿和素祭、乳香又搬进去。
Ndinalamulira kuti ayeretse zipinda, ndipo kenaka ndinabwezeramo zida za mʼNyumba ya Mulungu, pamodzi ndi chopereka cha zakudya ndi lubani.
10 我见利未人所当得的分无人供给他们,甚至供职的利未人与歌唱的俱各奔回自己的田地去了。
Ndinapezanso kuti Alevi sankalandira magawo awo amene amayera kulandira. Chotsatira chake Alevi onse pamodzi ndi oyimba nyimbo amene ankagwira ku Nyumba ya Mulungu anathawa, aliyense kupita ku munda wake.
11 我就斥责官长说:“为何离弃 神的殿呢?”我便招聚利未人,使他们照旧供职。
Choncho ndinadzudzula akuluakulu aja ndipo ndinawafunsa kuti, “Nʼchifukwa chiyani Nyumba ya Mulungu yasiyidwa?” Ndipo ine ndinawayitanitsa pamodzi ndi kuwayika mʼmalo awo.
12 犹大众人就把五谷、新酒,和油的十分之一送入库房。
Pambuyo pake Ayuda anayambanso kubwera ndi zopereka zawo za chakhumi cha tirigu, vinyo ndi mafuta kuti ziperekedwe ku nyumba yosungiramo chuma.
13 我派祭司示利米雅、文士撒督,和利未人毗大雅作库官管理库房;副官是哈难。哈难是撒刻的儿子;撒刻是玛他尼的儿子。这些人都是忠信的,他们的职分是将所供给的分给他们的弟兄。
Ndipo ndinasankha wansembe Selemiya, mlembi Zadoki, ndi Mlevi wotchedwa Pedaya kukhala oyangʼanira zipinda zosungiramo. Ndinasankhanso Hanani mwana wa Zakuri mwana wa Mataniya kukhala wowathandizira chifukwa ndinaona kuti anthu awa anali odalirika. Ntchito yawo inali yogawira abale awo zinthu zofunika.
14 我的 神啊,求你因这事记念我,不要涂抹我为 神的殿与其中的礼节所行的善。
Inu Mulungu wanga, mundikumbukire pa zimenezi, ndipo musafafanize ntchito zanga zimene ndachita mokhulupirika pa Nyumba yanu pofuna kukutumikirani.
15 那些日子,我在犹大见有人在安息日榨酒,搬运禾捆驮在驴上,又把酒、葡萄、无花果,和各样的担子在安息日担入耶路撒冷,我就在他们卖食物的那日警戒他们。
Nthawi imeneyo ndinaona anthu a mu Yuda akuponda ndi kufinya mphesa pa tsiku la Sabata. Ena ankawunjika tirigu milumilu ndi kumasenzetsa abulu. Enanso ankabwera ndi vinyo, mphesa, mkuyu ndi katundu wa mitundumitundu ku Yerusalemu pa tsiku la Sabata. Choncho ndinawachenjeza za kugulitsa zakudya pa tsiku la Sabata.
16 又有泰尔人住在耶路撒冷;他们把鱼和各样货物运进来,在安息日卖给犹大人。
Nawonso anthu a ku Turo amene ankakhala mu Yerusalemu ankabweretsa nsomba ndi akatundu ena onse amalonda kudzagulitsa pa Sabata kwa anthu a mʼdziko la Yuda ndi a mu Yerusalemu.
17 我就斥责犹大的贵胄说:“你们怎么行这恶事犯了安息日呢?
Ndipo ndinadzudzula anthu olemekezeka a dziko la Yuda. Ndinawafunsa kuti, “Nʼchoyipa chanji mukuchitachi, kumayipitsa tsiku la Sabata chotere?
18 从前你们列祖岂不是这样行,以致我们 神使一切灾祸临到我们和这城吗?现在你们还犯安息日,使忿怒越发临到以色列!”
Makolo anu anachita zomwezi ndipo Mulungu wathu anadzetsa mavuto pa ife ndi pa mzinda uwu. Kodi inu mukufuna kuwutsanso mkwiyo wa Mulungu pa Israeli pamene mukudetsa tsiku la Sabata?”
19 在安息日的前一日,耶路撒冷城门有黑影的时候,我就吩咐人将门关锁,不过安息日不准开放。我又派我几个仆人管理城门,免得有人在安息日担什么担子进城。
Nʼchifukwa chake ndikulamula kuti pamene kuyamba kuda, tsiku la Sabata lisanayambe, azitseka zipata zonse za Yerusalemu ndipo asazitsekule mpaka sabata litatha. Ndinayika ena mwa antchito anga oyangʼanira pa zipata kuti katundu aliyense asalowe mu Yerusalemu pa tsiku la Sabata.
20 于是商人和贩卖各样货物的,一两次住宿在耶路撒冷城外。
Choncho kamodzi kapena kawiri anthu amalonda ndi anthu ogulitsa katundu osiyanasiyana ankagona usiku wonse kunja kwa Yerusalemu.
21 我就警戒他们说:“你们为何在城外住宿呢?若再这样,我必下手拿办你们。”从此以后,他们在安息日不再来了。
Koma ndinawachenjeza ndi kuwafunsa kuti, “Nʼchifukwa chiyani mukugona pafupi ndi khoma? Ngati muchitanso zimenezi, ine ndidzakugwirani.” Kuyambira nthawi imeneyo, sanabwerenso pa tsiku la Sabata.
22 我吩咐利未人洁净自己,来守城门,使安息日为圣。我的 神啊,求你因这事记念我,照你的大慈爱怜恤我。
Ndipo ndinalamulira Alevi kuti adziyeretse okha ndi kubwera kudzalonda pa zipata ndi cholinga choti tsiku la Sabata likhale tsiku loyera. Inu Mulungu wanga, kumbukireninso ine pa zimenezi ndipo mundisunge malingana ndi chikondi chanu chachikulu chosasinthika.
23 那些日子,我也见犹大人娶了亚实突、亚扪、摩押的女子为妻。
Masiku amenewo ndinaonanso anthu a ku Yuda amene anakwatira akazi ochokera ku Asidodi, Amoni ndi Mowabu.
24 他们的儿女说话,一半是亚实突的话,不会说犹大的话,所说的是照着各族的方言。
Theka la ana awo linkayankhula chiyankhulo cha Asidodi kapena chiyankhulo chimodzi cha anthu ena, ndipo sankathanso kuyankhula chiyankhulo cha Ayuda.
25 我就斥责他们,咒诅他们,打了他们几个人,拔下他们的头发,叫他们指着 神起誓,必不将自己的女儿嫁给外邦人的儿子,也不为自己和儿子娶他们的女儿。
Tsono ndinakangana nawo ndi kuwatemberera. Ndinamenya ena mwa anthuwo ndi kuzula tsitsi lawo. Ine ndinawalumbiritsa mʼdzina la Mulungu kuti, “Inu musapereke ana anu aakazi kuti akwatiwe ndi ana awo aamuna kapena inuyo ngakhale ana anu aamuna kukwatira ana awo aakazi.
26 我又说:“以色列王所罗门不是在这样的事上犯罪吗?在多国中并没有一王像他,且蒙他 神所爱, 神立他作以色列全国的王;然而连他也被外邦女子引诱犯罪。
Kodi Solomoni mfumu ya Israeli suja anachimwa chifukwa cha ukwati ngati umenewu. Pakati pa mitundu yambiri panalibe mfumu ngati iyi. Iye anakondedwa ndi Mulungu wake, ndipo Mulungu anamuyika kukhala mfumu ya Israeli yense, koma iyeyo anachimwa chifukwa cha akazi achilendo.
27 如此,我岂听你们行这大恶,娶外邦女子干犯我们的 神呢?”
Kodi tsopano ife tizimva inu kuti mukuchita choyipa chachikulu chimenechi, kupandukira Yehova Mulungu wathu pomakwatira akazi achilendo?”
28 大祭司以利亚实的孙子、耶何耶大的一个儿子是和伦人参巴拉的女婿,我就从我这里把他赶出去。
Mmodzi mwa ana aamuna a Yehoyada mwana Eliyasibu mkulu wa ansembe nʼkuti nthawi imeneyi ali mpongozi wa Sanibalati wa ku Horoni. Choncho ndinamuthamangitsa pamaso panga.
29 我的 神啊,求你记念他们的罪;因为他们玷污了祭司的职任,违背你与祭司利未人所立的约。
Inu Mulungu wanga, mukumbukire mmene iwo anayipitsira unsembe, pangano la unsembe komanso la Alevi.
30 这样,我洁净他们,使他们离绝一切外邦人,派定祭司和利未人的班次,使他们各尽其职。
Motero ndinayeretsa ansembe ndi Alevi powachotsera kalikonse kachilendo. Ndipo ndinakhazikitsa ntchito zawo, kuti aliyense akhale pa ntchito yake.
31 我又派百姓按定期献柴和初熟的土产。我的 神啊,求你记念我,施恩与我。
Ndiponso kupereka nkhuni ndi zipatso zoyamba kucha pa nthawi yake. Ndikumbukireni pondikomera mtima, Inu Mulungu wanga.

< 尼希米记 13 >