< 士师记 16 >

1 参孙到了迦萨,在那里看见一个妓女,就与她亲近。
Tsiku lina Samsoni anapita ku Gaza. Kumeneko anaonako mkazi wachiwerewere, ndipo analowa mu nyumba yake.
2 有人告诉迦萨人说:“参孙到这里来了!”他们就把他团团围住,终夜在城门悄悄埋伏,说:“等到天亮我们便杀他。”
Anthu a ku Gaza anawuzidwa kuti, “Samsoni ali kuno!” Choncho anthuwo anazungulira malowo, kumubisalira usiku wonse ku chipata cha mzindawo. Iwo anakhala chete usiku wonse namanena kuti, “Tidzamupha mmamawa.”
3 参孙睡到半夜,起来,将城门的门扇、门框、门闩,一齐拆下来,扛在肩上,扛到希伯 前的山顶上。
Koma Samsoni anangogonako mpaka pakati pa usiku. Kenaka pakati pa usiku anadzuka nagwira zitseko za chipata cha mzinda ndi maferemu ake awiri, ndipo anazizula zonse pamodzi ndi mpiringidzo womwe. Anazisenza pa mapewa pake napita nazo pamwamba pa phiri loyangʼanana ndi Hebroni.
4 后来,参孙在梭烈谷喜爱一个妇人,名叫大利拉。
Pambuyo pake, Samsoni anayamba kukonda mtsikana wina wa ku chigwa cha Soreki dzina lake Delila.
5 非利士人的首领上去见那妇人,对她说:“求你诓哄参孙,探探他因何有这么大的力气,我们用何法能胜他,捆绑克制他。我们就每人给你一千一百舍客勒银子。”
Olamulira Afilisti anapita kwa mkaziyo ndipo anati, “Umunyengerere Samsoni kuti udziwe chinsinsi cha mphamvu zake zoopsazi, komanso ndi mmene ife tingamupambanire kuti timumange ndi kumugonjetsa. Ukatero aliyense wa ife adzakupatsa ndalama zasiliva 1,100.”
6 大利拉对参孙说:“求你告诉我,你因何有这么大的力气,当用何法捆绑克制你。”
Choncho Delila anati kwa Samsoni, “Inu tandiwuzani pamene pagona mphamvu zanu zoopsazi ndi mmene anthu akhoza kukumangirani kuti akugonjetseni.”
7 参孙回答说:“人若用七条未干的青绳子捆绑我,我就软弱像别人一样。”
Samsoni anamuyankha kuti, “Ngati wina atandimanga ndi zingwe zisanu ndi ziwiri zatsopano zosawuma, ndidzafowoka ndi kusanduka ngati munthu wina aliyense.”
8 于是非利士人的首领拿了七条未干的青绳子来,交给妇人,她就用绳子捆绑参孙。
Tsono atsogoleri a Afilisti aja anapita kwa mkazi uja namupatsa zingwe zisanu ndi ziwiri zatsopano zosawuma, ndipo mkaziyo anamanga nazo Samsoni.
9 有人预先埋伏在妇人的内室里。妇人说:“参孙哪,非利士人拿你来了!”参孙就挣断绳子,如挣断经火的麻线一般。这样,他力气的根由人还是不知道。
Nthawi imeneyo nʼkuti mkazi uja atayika anthu omubisalira mʼchipinda. Tsono anati kwa mwamuna wake, “Amuna anga, Afilisti aja afika!” Koma iye anangodula zingwe zija ngati mmene imadukira nkhosi ya chingwe ikamapsa. Choncho chinsinsi cha mphamvu zake sichinadziwike.
10 大利拉对参孙说:“你欺哄我,向我说谎言。现在求你告诉我当用何法捆绑你。”
Kenaka Delila anati kwa Samsoni, “Inu mwandipusitsa ndi kundiwuza zabodza. Chonde tandiwuzani mmene munthu angakumangireni.”
11 参孙回答说:“人若用没有使过的新绳捆绑我,我就软弱像别人一样。”
Iye anati, “Ngati aliyense atandimanga ine ndi zingwe zatsopano zimene sanazigwiritseko ntchito, ndidzasanduka wofowoka ndi kukhala monga munthu wina aliyense.”
12 大利拉就用新绳捆绑他,对他说:“参孙哪,非利士人拿你来了!”有人预先埋伏在内室里。参孙将臂上的绳挣断了,如挣断一条线一样。
Choncho Delila anatenga zingwe zatsopano namumanga nazo. Kenaka anati “Amuna anga, Afilisti aja afikanso!” Nthawi iyi nʼkuti anthu omubisalira aja ali mʼchipinda chamʼkati. Koma iye anadulanso zingwe mʼmanja ake ngati akudula ulusi wa thonje.
13 大利拉对参孙说:“你到如今还是欺哄我,向我说谎言。求你告诉我,当用何法捆绑你。”参孙回答说:“你若将我头上的七条发绺,与纬线同织就可以了。”
Ndipo Delila anati kwa Samsoni, “Mpaka tsopano mwakhala mukundipusitsa ndi kumandiwuza zabodza. Chonde, tandiwuzani mmene munthu angakumangireni.” Iye anayankha kuti, “Ngati njombi zisanu ndi ziwiri za kumutu kwanga utazilukira mu cholukira nsalu ndi kuchimanga molimbika ndi chikhomo, ndidzasanduka wofowoka ndi kukhala wofanana ndi munthu wina aliyense.”
14 于是大利拉将他的发绺与纬线同织,用橛子钉住,对他说:“参孙哪,非利士人拿你来了!”参孙从睡中醒来,将机上的橛子和纬线一齐都拔出来了。
Choncho iye akugona, Delila analukira njombi za ku mutu kwa Samsoni mu cholukira nsalu nachimanga molimba ndi chikhomo. Pambuyo pake anati kwa Samsoni, “Amuna anga, Afilisti aja abwera!” Tsono iye anadzuka ku tulo, nazula chikhomo chija ndipo njombi zinachoka mu cholukira chija.
15 大利拉对参孙说:“你既不与我同心,怎么说你爱我呢?你这三次欺哄我,没有告诉我,你因何有这么大的力气。”
Tsono mkaziyo ananenanso kwa iye kuti, “Munganene bwanji kuti mumandikonda pamene mtima wanu suli pa ine? Aka ndi kachitatu mukundipusitsa ndipo simunandiwuze pamene pagona mphamvu zanu zoopsazi.”
16 大利拉天天用话催逼他,甚至他心里烦闷要死。
Tsono popeza anamupanikiza ndi mawu ake tsiku ndi tsiku ndi kumukakamiza, mtima wa Samsoni unatopa pafupi kufa.
17 参孙就把心中所藏的都告诉了她,对她说:“向来人没有用剃头刀剃我的头,因为我自出母胎就归 神作拿细耳人;若剃了我的头发,我的力气就离开我,我便软弱像别人一样。”
Choncho anamuwuza mkaziyo zonse za mu mtima mwake nati “Lumo silinapitepo pa mutu wanga chifukwa ndakhala ndili Mnaziri wopatulikira Mulungu chibadwire. Ngati nditametedwa mphamvu zanga zidzandichokera, ndidzasanduka wofowoka ndipo ndidzafanana ndi munthu wina aliyense.”
18 大利拉见他把心中所藏的都告诉了她,就打发人到非利士人的首领那里,对他们说:“他已经把心中所藏的都告诉了我,请你们再上来一次。”于是非利士人的首领手里拿着银子,上到妇人那里。
Delila ataona kuti wamuwuza zonse za mu mtima mwake anatumiza uthenga kukayitana akuluakulu a Afilisti nati, “Bweraninso kamodzi kano kokha popeza wandiwululira zonse za mu mtima mwake.” Choncho akuluakulu a Afilisti aja anabwera ndi ndalama za siliva mʼmanja mwawo.
19 大利拉使参孙枕着她的膝睡觉,叫了一个人来剃除他头上的七条发绺。于是大利拉克制他,他的力气就离开他了。
Mkazi uja anagoneka Samsoni pa miyendo yake. Kenaka anayitana munthu wina ndipo anadzameta Samsoni njombi zisanu ndi ziwiri zija kumutu kwake. Pamenepo anayamba kufowoka, ndipo mphamvu zake zinamuchokera.
20 大利拉说:“参孙哪,非利士人拿你来了!”参孙从睡中醒来,心里说:“我要像前几次出去活动身体”;他却不知道耶和华已经离开他了。
Pambuyo pake mkaziyo anamuyitana kuti, “Amuna anga, Afilisti aja abwera!” Iye anadzuka kutuloko, naganiza kuti, “Ndituluka monga ndimachitira nthawi zonse ndi kudzimasula.” Koma sanadziwe kuti Yehova wamuchokera.
21 非利士人将他拿住,剜了他的眼睛,带他下到迦萨,用铜链拘索他;他就在监里推磨。
Afilisti anamugwira ndipo anamukolowola maso. Kenaka anapita naye ku Gaza atamumanga ndi maunyolo achitsulo. Kumeneko anakhala wa pamphero mu ndende.
22 然而他的头发被剃之后,又渐渐长起来了。
Pambuyo pake tsitsi la pa mutu wake, monga linametedwa, linayambanso kumera.
23 非利士人的首领聚集,要给他们的神大衮献大祭,并且欢乐,因为他们说:“我们的神将我们的仇敌参孙交在我们手中了。”
Tsono atsogoleri a Afilisti anasonkhana kuti adzapereke nsembe yayikulu kwa Dagoni mulungu wawo ndi kukondwerera popeza ankanena kuti, “Mulungu wathu wapereka Samsoni mdani wathu mʼmanja mwathu.”
24 众人看见参孙,就赞美他们的神说:“我们的神将毁坏我们地、杀害我们许多人的仇敌交在我们手中了。”
Anthuwo atamuona Samsoni, anayamba kutamanda mulungu wawo popeza ankanena kuti, “Mulungu wathu wapereka mdani wathu mʼmanja mwathu, ndiye amene anawononga dziko lathu, napha anthu athu ambirimbiri.”
25 他们正宴乐的时候,就说:“叫参孙来,在我们面前戏耍戏耍。”于是将参孙从监里提出来,他就在众人面前戏耍。他们使他站在两柱中间。
Ali mʼkati mosangalala, anthu aja amafuwula kuti, “Mutulutseni Samsoniyo kuti adzatisangalatse.” Choncho anamutulutsadi Samsoni mʼndende, ndipo anawasangalatsadi. Ndipo anamuyimiritsa pakati pa mizati.
26 参孙向拉他手的童子说:“求你让我摸着托房的柱子,我要靠一靠。”
Pambuyo pake Samsoni anawuza mnyamata amene anamugwira dzanja kuti, “Ndilole kuti ndikhudze mizati imene yachirikiza nyumba yonseyi kuti ndiyitsamire.”
27 那时房内充满男女,非利士人的众首领也都在那里。房的平顶上约有三千男女观看参孙戏耍。
Nthawi imeneyi nʼkuti nyumbayo ili yodzaza ndi anthu aamuna ndi aakazi. Olamulira onse a Afilisti anali momwemo, ndipo pamwamba pa nyumbayo panali anthu 3,000 aamuna ndi aakazi amene amaonerera Samsoni akusewera.
28 参孙求告耶和华说:“主耶和华啊,求你眷念我。 神啊,求你赐我这一次的力量,使我在非利士人身上报那剜我双眼的仇。”
Tsono Samsoni anapemphera kwa Yehova kuti, “Inu Yehova Ambuye anga, ndikumbukireni. Chonde ndilimbitseni nthawi yokha ino, inu Yehova, kuti ndiwabwezere Afilistiwa chifukwa cha maso anga awiri.”
29 参孙就抱住托房的那两根柱子:左手抱一根,右手抱一根,
Choncho Samsoni anagwira mizati iwiri yapakati imene inkachirikiza nyumbayo. Anayitsamira ndi mphamvu zake zonse, dzanja lake lamanja ku mzati wina ndi dzanja lamanzere ku mzati winanso,
30 说:“我情愿与非利士人同死!”就尽力屈身,房子倒塌,压住首领和房内的众人。这样,参孙死时所杀的人比活着所杀的还多。
ndipo Samsoni anati, “Ndife nawo pamodzi!” Nthawi yomweyo anakankha ndi mphamvu zake zonse ndipo mizati inagwera atsogoleri a Afilisti ndi anthu onse anali mʼmenemo. Tsono chiwerengero cha anthu amene Samsoni anapha pa nthawi ya imfa yake chinaposa cha iwo amene anawapha akanali ndi moyo.
31 参孙的弟兄和他父的全家都下去取他的尸首,抬上来葬在琐拉和以实陶中间,在他父玛挪亚的坟墓里。参孙作以色列的士师二十年。
Kenaka abale ake ndi onse a pa banja la abambo ake anapita kukamutenga. Ndipo anakamuyika pakati pa Zora ndi Esitaoli mʼmanda a abambo ake, Manowa. Iye anatsogolera Israeli kwa zaka makumi awiri.

< 士师记 16 >