< 约书亚记 21 >

1 那时,利未人的众族长来到祭司以利亚撒和嫩的儿子约书亚,并以色列各支派的族长面前,
Tsono atsogoleri a mabanja a fuko la Levi anabwera kwa wansembe Eliezara, Yoswa mwana wa Nuni, ndi kwa atsogoleri a mabanja a mafuko onse a Aisraeli,
2 在迦南地的示罗对他们说:“从前耶和华借着摩西吩咐给我们城邑居住,并城邑的郊野可以牧养我们的牲畜。”
ku Silo mʼdziko la Kanaani ndipo anati, “Yehova analamula kudzera mwa Mose kuti atipatse mizinda kuti tikhalemo, pamodzi ndi malo odyetseramo ziweto zathu.”
3 于是以色列人照耶和华所吩咐的,从自己的地业中,将以下所记的城邑和城邑的郊野给了利未人。
Choncho, Aisraeli anapereka kwa fuko la Levi mizinda iyi pamodzi ndi malo owetera ziweto zawo kuchokera ku madera awo, monga Yehova analamulira:
4 为哥辖族拈阄:利未人的祭司、亚伦的子孙,从犹大支派、西缅支派、便雅悯支派的地业中,按阄得了十三座城。
Maere oyamba anagwera mabanja a Kohati, Alevi amene anali zidzukulu za wansembe Aaroni anapatsidwa mizinda 13 kuchokera ku mafuko a Yuda, Simeoni ndi Benjamini.
5 哥辖其余的子孙,从以法莲支派、但支派、玛拿西半支派的地业中,按阄得了十座城。
Ndipo mabanja otsala a Kohati anapatsidwa mizinda khumi kuchokera ku mafuko a Efereimu, Dani ndi theka la fuko la Manase.
6 革顺的子孙,从以萨迦支派、亚设支派、拿弗他利支派、住巴珊的玛拿西半支派的地业中,按阄得了十三座城。
Zidzukulu za Geresoni zinapatsidwa mizinda 13 kuchokera ku mabanja a mafuko a Isakara, Aseri, Nafutali ndi theka la fuko la Manase ku Basani.
7 米拉利的子孙,按着宗族,从吕便支派、迦得支派、西布伦支派的地业中,按阄得了十二座城。
Mabanja a Merari anapatsidwa mizinda khumi ndi iwiri kuchokera ku mafuko a Rubeni, Gadi ndi Zebuloni.
8 以色列人照着耶和华借摩西所吩咐的,将这些城邑和城邑的郊野,按阄分给利未人。
Choncho Aisraeli anapereka kwa fuko la Levi mizindayi pamodzi ndi malo odyetserako ziweto pogwiritsa ntchito maere, monga Yehova analamula kudzera mwa Mose.
9 从犹大支派、西缅支派的地业中,将以下所记的城给了利未支派哥辖宗族亚伦的子孙;因为给他们拈出头一阄,
Awa ndi mayina a mizinda ya mafuko a Yuda ndi Simeoni imene inaperekedwa kwa zidzukulu za Aaroni,
ku banja la Kohati amene anali Alevi. Paja maere oyamba anagwera mabanja a Kohati kuti alandira mizinda.
11 将犹大山地的基列·亚巴和四围的郊野给了他们。亚巴是亚衲族的始祖。(基列·亚巴就是希伯 )。
Anapatsidwa mzinda wa Kiriati Ariba. (Paja Ariba ndiye kholo la Anaaki). Dzina lina la mzindawu ndi Hebroni, ndipo unali mʼdziko la mapiri la Yuda. Pamodzi ndi mzindawu anapatsidwanso mabusa ake onse ozungulira.
12 惟将属城的田地和村庄给了耶孚尼的儿子迦勒为业。
Komabe minda ndi midzi yozungulira mizindayi inali itaperekedwa kale kwa Kalebe, mwana wa Yefune kuti ikhale cholowa chake.
13 以色列人将希伯 ,就是误杀人的逃城和属城的郊野,给了祭司亚伦的子孙;又给他们立拿和属城的郊野,
Choncho zidzukulu za Aaroni wansembe, zinapatsidwa Hebroni (mzinda wopulumukirako amene wapha munthu), Libina,
14 雅提珥和属城的郊野,以实提莫和属城的郊野,
Yatiri, Esitemowa,
15 何 和属城的郊野,底璧和属城的郊野,
Holoni, Debri,
16 亚因和属城的郊野,淤他和属城的郊野,伯·示麦和属城的郊野,共九座城,都是从这二支派中分出来的。
Aini, Yuta, ndi Beti-Semesi pamodzi ndi mabusa odyetseramo ziweto ozungulira mizindayi. Yonse pamodzi inali mizinda isanu ndi inayi yochokera ku mafuko awiriwa.
17 又从便雅悯支派的地业中给了他们基遍和属城的郊野,迦巴和属城的郊野,
Fuko la Benjamini linapereka Gibiyoni, Geba,
18 亚拿突和属城的郊野,亚勒们和属城的郊野,共四座城。
Anatoti ndi Alimoni, pamodzi ndi mabusa odyetsera ziweto ozungulira mizindayi. Yonse pamodzi inali mizinda inayi.
19 亚伦子孙作祭司的共有十三座城,还有属城的郊野。
Choncho mizinda 13 pamodzi ndi malo odyetsera ziweto anapatsidwa kwa ansembe, zidzukulu za Aaroni.
20 利未支派中哥辖的宗族,就是哥辖其余的子孙,拈阄所得的城有从以法莲支派中分出来的。
Mabanja ena otsalira a Kohati a fuko la Levi anapatsidwa mizinda iyi kuchokera ku fuko la Efereimu:
21 以色列人将以法莲山地的示剑,就是误杀人的逃城和属城的郊野,给了他们;又给他们基色和属城的郊野,
Mizinda ya Sekemu ndi Gezeri ndiye inali mizinda wopulumukirako munthu aliyense wopha mnzake mwangozi. Mizindayi inali ku mapiri a Efereimu.
22 基伯先和属城的郊野,伯·和 和属城的郊野,共四座城;
Analandiranso mizinda ya Gezeri, Kibuzaimu, Beti-Horoni pamodzi ndi malo odyetsera ziweto ozungulira mizindayi. Yonse pamodzi inali mizinda inayi.
23 又从但支派的地业中给了他们伊利提基和属城的郊野,基比顿和属城的郊野,
Fuko la Dani linapereka mizinda ya Eliteke, Gibetoni,
24 亚雅 和属城的郊野,迦特·临门和属城的郊野,共四座城;
Ayaloni, Gati-Rimoni pamodzi ndi mabusa odyetsera ziweto ozungulira mizindayi. Yonse pamodzi inali mizinda inayi.
25 又从玛拿西半支派的地业中给了他们他纳和属城的郊野,迦特·临门和属城的郊野,共两座城。
Kuchokera ku theka la fuko la Manase analandira Taanaki ndi Gati-Rimoni pamodzi ndi malo awo owetera ziweto, mizinda iwiri.
26 哥辖其余的子孙共有十座城,还有属城的郊野。
Mizinda khumi yonseyi pamodzi ndi malo odyetsera ziweto, zinapatsidwa ku mabanja ena onse a Akohati.
27 以色列人又从玛拿西半支派的地业中将巴珊的哥兰,就是误杀人的逃城和属城的郊野,给了利未支派革顺的子孙;又给他们比·施提拉和属城的郊野,共两座城;
Mabanja a Ageresoni a fuko la Levi anapatsidwa mizinda iwiri kuchokera ku theka la Manase wa kummawa, Golani ku Basani (mzinda wopulumukirako amene wapha munthu mwangozi) ndi Beesitera, pamodzi ndi malo awo odyetserako ziweto.
28 又从以萨迦支派的地业中给了他们基善和属城的郊野,大比拉和属城的郊野,
Fuko la Isakara linapereka mizinda ya Kisoni, Daberati,
29 耶末和属城的郊野,隐·干宁和属城的郊野,共四座城;
Yarimuti ndi Eni Ganimu, pamodzi ndi malo awo odyetsera ziweto. Yonse pamodzi inali mizinda inayi.
30 又从亚设支派的地业中给了他们米沙勒和属城的郊野,押顿和属城的郊野,
Fuko la Aseri linapereka mizinda ya Misali, Abidoni,
31 黑甲和属城的郊野,利合和属城的郊野,共四座城;
Helikati ndi Rehobu pamodzi ndi malo awo odyetsera ziweto. Yonse pamodzi inali mizinda inayi.
32 又从拿弗他利支派的地业中将加利利的基低斯,就是误杀人的逃城和属城的郊野,给了他们;又给他们哈末·多珥和属城的郊野,加珥坦和属城的郊野,共三座城。
Fuko la Nafutali linapereka mizinda ya Kedesi wa ku Galileya, mzinda umene unali wopulumukiramo munthu wopha mnzake mwangozi. Analandiranso mizinda ya Hamoti-Dori ndi Karitani. Kuphatikizira apa, analandira malo odyetsera ziweto a mizindayi. Yonse pamodzi inali mizinda inayi.
33 革顺人按着宗族所得的城,共十三座,还有属城的郊野。
Mabanja onse a Ageresoni analandira mizinda 13 pamodzi ndi malo awo odyetsera a ziweto.
34 其余利未支派米拉利子孙,从西布伦支派的地业中所得的,就是约念和属城的郊野,加珥他和属城的郊野,
Mabanja a Merari amene anali otsala a fuko la Levi, anapatsidwa mizinda iyi kuchokera ku fuko la Zebuloni: Yokineamu, Karita,
35 丁拿和属城的郊野,拿哈拉和属城的郊野,共四座城;
Dimuna ndi Nahalali, pamodzi ndi malo awo odyetsera ziweto. Yonse pamodzi inali mizinda inayi.
36 又从吕便支派的地业中给了他们比悉和属城的郊野,雅杂和属城的郊野,
Kuchokera ku fuko la Rubeni analandira Bezeri, Yahaza,
37 基底莫和属城的郊野,米法押和属城的郊野,共四座城;
Kedemoti ndi Mefaati, pamodzi ndi malo awo odyetsera ziweto. Yonse pamodzi inali mizinda inayi.
38 又从迦得支派的地业中,将基列的拉末,就是误杀人的逃城和属城的郊野,给了他们;又给他们玛哈念和属城的郊野,
Kuchokera ku fuko la Gadi analandira mzinda wa Ramoti ku Giliyadi. Mzinda umene unali wopulumukiramo munthu wopha mnzake mwangozi.
39 希实本和属城的郊野,雅谢和属城的郊野,共四座城。
Analandiranso mizinda ya Mahanaimu, Hesiboni, Yazeri pamodzi ndi malo odyetserako ziweto ozungulira mizinda yonseyi. Yonse pamodzi inali mizindayi anayi.
40 其余利未支派的人,就是米拉利的子孙,按着宗族拈阄所得的,共十二座城。
Choncho mabanja onse a Merari, amene anali otsala a fuko la Levi analandira mizinda khumi ndi iwiri pogwiritsa ntchito maere.
41 利未人在以色列人的地业中所得的城,共四十八座,并有属城的郊野。
Motero mizinda 48 ya mʼdziko limene Aisraeli analanda inapatsidwa kwa Alevi, kuphatikizapo malo ake odyetsera ziweto.
42 这些城四围都有属城的郊野,城城都是如此。
Iliyonse mwa mizindayi inali ndi malo owetera ziweto oyizungulira.
43 这样,耶和华将从前向他们列祖起誓所应许的全地赐给以色列人,他们就得了为业,住在其中。
Motero Yehova anapereka kwa Israeli dziko limene analumbira kulipereka kwa makolo awo. Atalilandira anadzakhalamo.
44 耶和华照着向他们列祖起誓所应许的一切话,使他们四境平安;他们一切仇敌中,没有一人在他们面前站立得住。耶和华把一切仇敌都交在他们手中。
Yehova anawapatsa mtendere mʼdziko lonse monga momwe analonjezera makolo awo. Palibe ndi mmodzi yemwe mwa adani awo amene anatha kuwagonjetsa chifukwa Yehova anapereka adani awo onse mʼmanja mwawo.
45 耶和华应许赐福给以色列家的话一句也没有落空,都应验了。
Yehova anakwaniritsa zonse zimene analonjeza kwa Aisraeli.

< 约书亚记 21 >