< 约伯记 6 >

1 约伯回答说:
Tsono Yobu anayankha kuti,
2 惟愿我的烦恼称一称, 我一切的灾害放在天平里;
“Achikhala mavuto anga anayezedwa, ndipo zipsinjo zanga zonse zikanayikidwa pa sikelo!
3 现今都比海沙更重, 所以我的言语急躁。
Ndithu, zikanalemera kupambana mchenga wa ku nyanja; nʼchifukwa chake mawu anga akhala okhadzula.
4 因全能者的箭射入我身; 其毒,我的灵喝尽了; 神的惊吓摆阵攻击我。
Mivi ya Wamphamvuzonse yandibaya, thupi langa likumva ululu wa miviyo; zoopsa za Mulungu zandizinga.
5 野驴有草岂能叫唤? 牛有料岂能吼叫?
Kodi bulu wakuthengo amalira akakhala ndi msipu, nanga ngʼombe imalira ikakhala ndi chakudya?
6 物淡而无盐岂可吃吗? 蛋青有什么滋味呢?
Kodi chakudya chosakoma nʼkuchidya chopanda mchere, nanga choyera cha dzira chimakoma?
7 看为可厌的食物, 我心不肯挨近。
Zakudya zimenezi sindifuna nʼkuzilawa komwe; zakudya zimenezi zimabwerera kukhosi.
8 惟愿我得着所求的, 愿 神赐我所切望的;
“Aa, ndikanalandira chimene ndikuchipempha, chikhala Mulungu anandipatsa chimene ndikuchiyembekezera,
9 就是愿 神把我压碎, 伸手将我剪除。
achikhala chinamukomera Mulungu kuti anditswanye, kulola dzanja lake kuti lindimenye ndi kundiwonongeratu!
10 我因没有违弃那圣者的言语, 就仍以此为安慰, 在不止息的痛苦中还可踊跃。
Pamenepo ine ndikanakhalabe ndi chitonthozo ichi, ndikanakondwa mu ululu wanga wosalekezawu podziwa kuti sindinakane mawu a Woyerayo.
11 我有什么气力使我等候? 我有什么结局使我忍耐?
“Kodi mphamvu zanga nʼzotani kuti ndizikhalabe ndi chiyembekezo? Nanga zoyembekezera zanga nʼzotani kuti ndipirirebe?
12 我的气力岂是石头的气力? 我的肉身岂是铜的呢?
Kodi ine ndili ndi mphamvu? Nanga thupi langa ndi lolimba ngati chitsulo?
13 在我岂不是毫无帮助吗? 智慧岂不是从我心中赶出净尽吗?
Kodi ndili ndi mphamvu zodzithandizira ndekha, nanga pakuti thandizo lachotsedwa kwa ine?
14 那将要灰心、离弃全能者、 不敬畏 神的人, 他的朋友当以慈爱待他。
“Munthu amene ali kakasi ayenera kukhala ndi abwenzi odzipereka, ngakhale kuti iyeyo wasiya kuopa Wamphamvuzonse.
15 我的弟兄诡诈,好像溪水, 又像溪水流干的河道。
Koma abale anga ndi wosadalirika ngati mitsinje yowuma msanga, ngati mitsinje imene imathamanga.
16 这河因结冰发黑, 有雪藏在其中;
Ali ngati mitsinje ya madzi akuda nthawi ya dzinja, imene madzi ake amakhala ambiri chifukwa chakuchuluka kwa mvula,
17 天气渐暖就随时消化, 日头炎热便从原处干涸。
koma madziwo amasiya kuyenda nthawi yachilimwe, ndipo nthawi yotentha madziwo amawumiratu mʼmitsinjemo.
18 结伴的客旅离弃大道, 顺河偏行,到荒野之地死亡。
Anthu oyenda pa ngamira amapatukirako kufuna madzi; iwo amangoyendayenda nʼkufera mʼchipululu.
19 提玛结伴的客旅瞻望; 示巴同伙的人等候。
Anthu oyenda pa ngamira a ku Tema amafunafuna madzi, anthu amalonda apaulendo a ku Seba amafunafuna mwa chiyembekezo.
20 他们因失了盼望就抱愧, 来到那里便蒙羞。
Amataya mtima chifukwa ankayembekezera kupeza madzi; koma akafika kumeneko, amangokhumudwako.
21 现在你们正是这样, 看见惊吓的事便惧怕。
Tsono inunso mukuonetsa kuti ndinu osathandiza, mukuona chinthu choopsa kwambiri ndipo mukuchita mantha.
22 我岂说:请你们供给我, 从你们的财物中送礼物给我?
Kodi ine ndinanenapo kuti, ‘Ndiperekereni kenakake, ndilipirireni dipo kuchokera pa chuma chanu,
23 岂说:拯救我脱离敌人的手吗? 救赎我脱离强暴人的手吗?
ndilanditseni mʼdzanja la mdani, ndiwomboleni mʼdzanja la munthu wankhanza?’
24 请你们教导我,我便不作声; 使我明白在何事上有错。
“Phunzitseni, ndipo ine ndidzakhala chete; ndionetseni pomwe ndalakwitsa.
25 正直的言语力量何其大! 但你们责备是责备什么呢?
Ndithu, mawu owona ndi opweteka! Koma mawu anu otsutsa akufuna kuonetsa chiyani?
26 绝望人的讲论既然如风, 你们还想要驳正言语吗?
Kodi inu mukufuna kundidzudzula pa zimene ndikunena, ndipo mukufuna kuyesa mawu a munthu wosweka mtima ngati mphepo chabe?
27 你们想为孤儿拈阄, 以朋友当货物。
Inu mungathe kuchita maere kuti mugulitse ana amasiye ndi kumugulitsa bwenzi lanu.
28 现在请你们看看我, 我决不当面说谎。
“Koma tsopano ndichitireni chifundo pamene mukundiyangʼana. Kodi ine ndingayankhule zabodza pamaso panu?
29 请你们转意,不要不公; 请再转意,我的事有理。
Fewani mtima, musachite zosalungama; ganiziraninso popeza chilungamo changa chikanalipobe.
30 我的舌上岂有不义吗? 我的口里岂不辨奸恶吗?
Kodi pali choyipa chilichonse pa milomo yanga? Kodi pakamwa panga sipangathe kuzindikira kanthu koyipa?

< 约伯记 6 >