< 耶利米书 6 >
1 便雅悯人哪,你们要逃出耶路撒冷, 在提哥亚吹角, 在伯·哈基琳立号旗; 因为有灾祸与大毁灭从北方张望。
“Thawani, inu anthu a ku Benjamini! Tulukani mu Yerusalemu! Lizani lipenga ku Tekowa! Kwezani mbendera ku Beti-Hakeremu! Pakuti tsoka lalikulu likubwera kuchokera kumpoto, ndipo chiwonongekocho nʼchachikulu.
Kodi mzinda wa Ziyoni suli ngati msipu wokongola kwambiri, kumene abusa amafikako ndi ziweto zawo?
3 牧人必引他们的羊群到她那里, 在她周围支搭帐棚, 各在自己所占之地使羊吃草。
Abusa ndi nkhosa zawo adzabwera kudzalimbana nawo; adzamanga matenti awo mowuzinga, ndipo aliyense adzakhazika anthu ake pamalo pake.”
4 你们要准备攻击她。 起来吧,我们可以趁午时上去。 哀哉!日已渐斜, 晚影拖长了。
Adzanena kuti, “Konzekani kuwuthira nkhondo mzindawo! Nyamukani, kuti tiwuthire nkhondo mzindawu masana ano. Koma tili ndi tsoka, dzuwa lapendeka, ndipo zithunzithunzi za kumadzulo zikunka zitalika.
Tsono nyamukani kuti tiwuthire nkhondo mzindawu usiku uno ndi kuwononga malinga ake!”
6 因为万军之耶和华如此说: 你们要砍伐树木, 筑垒攻打耶路撒冷。 这就是那该罚的城, 其中尽是欺压。
Yehova Wamphamvuzonse akuti, “Dulani mitengo ndipo mumange mitumbira yankhondo kulimbana ndi Yerusalemu. Mzinda umenewu uyenera kulangidwa; wadzaza ndi kuponderezana.
7 井怎样涌出水来, 这城也照样涌出恶来; 在其间常听见有强暴毁灭的事, 病患损伤也常在我面前。
Monga momwe chitsime chimatulutsira madzi ndi mmenenso Yerusalemu amatulutsira zoyipa zake. Chiwawa ndi chiwonongeko ndi zomwe zimamveka mu mzindamo; nthenda yake ndi mabala ake ndimaziona nthawi zonse.
8 耶路撒冷啊,你当受教, 免得我心与你生疏, 免得我使你荒凉, 成为无人居住之地。
Iwe Yerusalemu, tengapo phunziro, kuopa kuti chikondi changa pa iwe chingakuchokere ndi kusandutsa dziko lako kukhala bwinja mopanda munthu wokhalamo.”
9 万军之耶和华曾如此说: 敌人必掳尽以色列剩下的民, 如同摘净葡萄一样。 你要像摘葡萄的人摘了又摘,回手放在筐子里。
Yehova Wamphamvuzonse anandiwuza kuti, “Adani adzawakunkha ndithu anthu otsala a Israeli, monga momwe amachitira populula mphesa. Tsono iwe yesetsa kupulumutsa amene ungathe monga mmene amachitira munthu wokolola mphesa.”
10 现在我可以向谁说话作见证,使他们听呢? 他们的耳朵未受割礼,不能听见。 看哪,耶和华的话他们以为羞辱, 不以为喜悦。
Kodi ndiyankhule ndi yani ndi kumuchenjeza? Ndinene mawu ochenjeza kwa yani kuti amve? Makutu awo ndi otsekeka kotero kuti sangathe kumva. Mawu a Yehova ndi onyansa kwa iwo; sasangalatsidwa nawo.
11 因此我被耶和华的忿怒充满,难以含忍。 我要倾在街中的孩童和聚会的少年人身上, 连夫带妻, 并年老的与日子满足的都必被擒拿。
Koma ine ndadzazidwa ndi mkwiyo wa Yehova, ndipo ndatopa ndi kusunga mkwiyo wa Yehova. Yehova anandiwuza kuti, “Tsono ndidzawutulutsira mkwiyo umenewu pa ana oyenda mʼmisewu ndi pa achinyamata amene asonkhana pamodzi; pakutinso mwamuna ndi mkazi wake adzatengedwa, pamodzi ndi okalamba amene ali ndi zaka zochuluka.
12 他们的房屋、田地, 和妻子都必转归别人; 我要伸手攻击这地的居民。 这是耶和华说的。
Nyumba zawo adzazipereka kwa ena, pamodzi ndi minda yawo ndi akazi awo. Ndidzatambasula dzanja langa kukantha anthu okhala mʼdzikomo,” akutero Yehova.
13 因为他们从最小的到至大的都一味地贪婪, 从先知到祭司都行事虚谎。
“Kuyambira wamngʼono mpaka wamkulu, onse ali ndi dyera lofuna kupeza phindu mwa kuba; aneneri pamodzi ndi ansembe omwe, onse amachita zachinyengo.
14 他们轻轻忽忽地医治我百姓的损伤, 说:平安了!平安了! 其实没有平安。
Amapoletsa zilonda za anthu anga pamwamba pokha. Iwo amanena kuti, ‘Mtendere, mtendere,’ pamene palibe mtendere.
15 他们行可憎的事知道惭愧吗? 不然,他们毫不惭愧, 也不知羞耻。 因此,他们必在仆倒的人中仆倒; 我向他们讨罪的时候, 他们必致跌倒。 这是耶和华说的。
Kodi amachita manyazi akamachita zonyansazo? Ayi, sachita manyazi ndi pangʼono pomwe; sadziwa ndi kugwetsa nkhope komwe. Choncho iwo adzagwera pakati pa anzawo amene agwa kale; adzagwa pansi tsiku limene ndidzawalange,” akutero Yehova.
16 耶和华如此说: 你们当站在路上察看, 访问古道, 哪是善道,便行在其间; 这样,你们心里必得安息。 他们却说:我们不行在其间。
Yehova akuti, “Imani pa mphambano ndipo mupenye; kumeneko ndiye kuli njira zakale, funsani kumene kuli njira yabwino. Yendani mʼmenemo, ndipo mudzapeza mpumulo wa miyoyo yanu. Koma inu munati, ‘Ife sitidzayenda njira imeneyo.’
17 我设立守望的人照管你们, 说:要听角声。 他们却说:我们不听。
Ine ndinakupatsani alonda oti akuyangʼanireni ndipo ndinati, ‘Imvani kulira kwa lipenga!’ koma inu munati, ‘Sitidzamvera.’
18 列国啊,因此你们当听! 会众啊,要知道他们必遭遇的事。
Nʼchifukwa chake imvani, inu anthu a mitundu ina; yangʼanitsitsani, inu amene mwasonkhana pano, chimene chidzawachitikire anthuwo.
19 地啊,当听! 我必使灾祸临到这百姓, 就是他们意念所结的果子; 因为他们不听从我的言语, 至于我的训诲,他们也厌弃了。
Imvani, inu anthu okhala pa dziko lapansi, ndikubweretsa masautso pa anthu awa. Zimenezi ndi mphotho ya ntchito zawo. Iwowa sanamvere mawu anga ndipo anakana lamulo langa.
20 从示巴出的乳香, 从远方出的菖蒲 奉来给我有何益呢? 你们的燔祭不蒙悦纳; 你们的平安祭,我也不喜悦。
Kodi pali phindu lanji ngakhale mubwere ndi lubani kuchokera ku Seba, kapena zonunkhira zina kuchokera ku dziko lakutali? Nsembe zanu zopsereza Ine sindidzalandira; nsembe zanu sizindikondweretsa.”
21 所以耶和华如此说: 我要将绊脚石放在这百姓前面。 父亲和儿子要一同跌在其上; 邻舍与朋友也都灭亡。
Choncho Yehova akuti, “Ndidzayika zokhumudwitsa pamaso pa anthu awa. Abambo ndi ana awo aamuna onse adzapunthwa ndi kugwa; anansi awo ndi abwenzi awo adzawonongeka.”
22 耶和华如此说: 看哪,有一种民从北方而来, 并有一大国被激动,从地极来到。
Yehova akunena kuti, “Taonani, gulu lankhondo likubwera kuchokera kumpoto; mtundu wa anthu amphamvu wanyamuka kuchokera kumathero a dziko lapansi.
23 他们拿弓和枪, 性情残忍,不施怜悯; 他们的声音像海浪匉訇。 锡安城啊, 他们骑马都摆队伍, 如上战场的人要攻击你。
Atenga mauta ndi mikondo; ndi anthu ankhanza ndi opanda chifundo. Phokoso lawo lili ngati mkokomo wa nyanja. Akwera pa akavalo awo ndipo akonzekera ngati anthu ankhondo, kudzakuthirani nkhondo anthu a ku Ziyoni.”
24 我们听见他们的风声,手就发软; 痛苦将我们抓住, 疼痛仿佛产难的妇人。
A ku Ziyoni akuti “Ife tamva mbiri yawo, ndipo manja anthu alefukiratu. Nkhawa yatigwira, ndipo tikumva ululu ngati mayi pa nthawi yake yochira.
25 你们不要往田野去, 也不要行在路上, 因四围有仇敌的刀剑和惊吓。
Musapite ku minda kapena kuyenda mʼmisewu, pakuti mdani ali ndi lupanga, ndipo ponseponse anthu akuchita mantha.
26 我民哪,应当腰束麻布,滚在灰中。 你要悲伤,如丧独生子痛痛哭号, 因为灭命的要忽然临到我们。
Inu anthu anga, valani ziguduli ndipo gubudukani pa phulusa; lirani mwamphamvu ngati munthu wolirira mwana wake mmodzi yekha, pakuti mwadzidzidzi wowonongayo adzabwera kudzatipha.
27 我使你在我民中为高台,为保障, 使你知道试验他们的行动。
“Iwe Yeremiya, ndakuyika kuti ukhale choyesera zitsulo. Uwayese anthu anga monga ungayesere chitsulo kuti uwone makhalidwe awo.
28 他们都是极悖逆的, 往来谗谤人。 他们是铜是铁, 都行坏事。
Onsewo ali ndi khalidwe lokanika ndi lowukira ndipo akunka nanena zamiseche. Iwo ndi olimba ngati mkuwa ndi chitsulo. Onse amangochita zoyipa zokhazokha.
29 风箱吹火,铅被烧毁; 他们炼而又炼,终是徒然; 因为恶劣的还未除掉。
Moto mu mvukuto ukuyaka kwambiri; mtovu watha kusungunuka ndi moto. Koma ntchito yosungunulayo sikupindula chifukwa zoyipa sizikuchokapo.
30 人必称他们为被弃的银渣, 因为耶和华已经弃掉他们。
Iwo ali ngati siliva wotayidwa, chifukwa Yehova wawakana.”