< 耶利米书 13 >

1 耶和华对我如此说:“你去买一根麻布带子束腰,不可放在水中。”
Yehova anandiwuza kuti, “Pita kagule lamba wansalu yosalala ndipo ukavale mʼchiwuno mwako, koma usakamuviyike mʼmadzi.”
2 我就照着耶和华的话,买了一根带子束腰。
Choncho ndinakagula lambayo, monga momwe anandiwuzira Yehova, ndipo ndinamanga mʼchiwuno mwanga.
3 耶和华的话第二次临到我说:
Kenaka Yehova anandiyankhulanso kachiwiri kuti,
4 “要拿着你所买的腰带,就是你腰上的带子,起来往幼发拉底河去,将腰带藏在那里的磐石穴中。”
“Tenga lamba amene unagula ndi kuvala mʼchiwuno mwako uja. Tsono pita ku mtsinje wa Yufurate ndipo ukamubise lambayo mʼmingʼalu ya mʼmatanthwe.”
5 我就去,照着耶和华所吩咐我的,将腰带藏在幼发拉底河边。
Ndipo ndinapitadi ndi kukabisa lambayo ku Yufurate, monga anenera Yehova.
6 过了多日,耶和华对我说:“你起来往幼发拉底河去,将我吩咐你藏在那里的腰带取出来。”
Patapita masiku ambiri Yehova anandiwuzanso kuti, “Pitanso ku Yufurate ndipo ukatenge lamba amene ndinakuwuza kuti ukamubise kumeneko.”
7 我就往幼发拉底河去,将腰带从我所藏的地方刨出来,见腰带已经变坏,毫无用了。
Choncho ndinapita ku Yufurate kukafukula lambayo ndi kumuchotsa pamalo pamene ndinamubisa, koma nthawi imeneyi nʼkuti lambayo atawonongeka kotheratu ndipo analibenso ntchito.
8 耶和华的话临到我说:
Pamenepo Yehova anandiwuza kuti,
9 “耶和华如此说:我必照样败坏犹大的骄傲和耶路撒冷的大骄傲。
“Izi ndi zimene ine ndikunena: ‘Umu ndi mmene ndidzawonongere zimene akunyadira kwambiri a ku Yuda ndi a ku Yerusalemu.
10 这恶民不肯听我的话,按自己顽梗的心而行,随从别神,事奉敬拜,他们也必像这腰带变为无用。”
Anthuwa ndi oyipa. Iwo akana kumvera mawu anga. Mʼmalo mwake amawumirira kutsata milungu ina, kuyitumikira ndi kuyipembedza. Anthu amenewa adzakhala ngati lamba wopanda ntchitoyu.
11 耶和华说:“腰带怎样紧贴人腰,照样,我也使以色列全家和犹大全家紧贴我,好叫他们属我为子民,使我得名声,得颂赞,得荣耀;他们却不肯听。”
Monga momwe lamba amakanirira mʼchiwuno cha munthu, momwemonso ndinakonza kuti nyumba yonse ya Israeli ndi nyumba yonse ya Yuda indikangamire Ine kuti akhale anthu anga, kuti azitamanda dzina langa ndi kulemekeza Ine. Koma iwo sanamvere,’ akutero Yehova.
12 “所以你要对他们说:‘耶和华—以色列的 神如此说:各坛都要盛满了酒。’他们必对你说:‘我们岂不确知各坛都要盛满了酒呢?’
“Awuze anthuwo kuti, ‘Yehova Mulungu wa Israeli akuti: Mtsuko uliwonse adzawudzaza ndi vinyo.’ Ndipo ngati iwo anena kwa iwe kuti, ‘Kodi ngati ife sitikudziwa kuti mtsuko uliwonse udzadzazidwa ndi vinyo?’
13 你就要对他们说:‘耶和华如此说:我必使这地的一切居民,就是坐大卫宝座的君王和祭司,与先知,并耶路撒冷的一切居民,都酩酊大醉。’”
Tsono iwe uwawuze kuti, Yehova akuti ‘Ine ndidzaledzeretsa anthu onse okhala mʼdziko muno, kuyambira mafumu amene amakhala pa mpando waufumu wa Davide, ansembe, aneneri, pamodzi ndi anthu onse amene akukhala mu Yerusalemu.
14 耶和华说:“我要使他们彼此相碰,就是父与子彼此相碰;我必不可怜,不顾惜,不怜悯,以致灭绝他们。”
Ndidzawagundanitsa mitu kuti aphwanyane okhaokha ngati mitsuko, makolo ndi ana awo, akutero Yehova. Sindidzawamvera chisoni kapena kuwachitira chifundo kapena kukhudzidwa nawo kuti ndileke kuwawononga.’”
15 你们当听,当侧耳而听。 不要骄傲,因为耶和华已经说了。
Imvani inu Aisraeli ndipo tcherani khutu, musadzitukumule, pakuti ndi Yehova amene akuyankhula.
16 耶和华—你们的 神未使黑暗来到, 你们的脚未在昏暗山上绊跌之先, 当将荣耀归给他; 免得你们盼望光明, 他使光明变为死荫, 成为幽暗。
Lemekezani Yehova Mulungu wanu asanagwetse mdima, mapazi anu asanayambe kupunthwa mʼchisisira chamʼmapiri. Asanasandutse kuwala mukuyembekezerako kukhala mdima wandiweyani.
17 你们若不听这话, 我必因你们的骄傲在暗地哭泣; 我眼必痛哭流泪, 因为耶和华的群众被掳去了。
Koma ngati simumvera, ndidzalira kwambiri chifukwa cha kunyada kwanu. Mʼmaso mwanga mwadzaza ndi misozi yowawa chifukwa nkhosa za Yehova zatengedwa ukapolo.
18 你要对君王和太后说: 你们当自卑,坐在下边; 因你们的头巾, 就是你们的华冠,已经脱落了。
Uza mfumu pamodzi ndi amayi ake kuti, “Tsikani pa mipando yaufumuyo, pakuti zipewa zanu zaufumu zokongolazo zagwa pansi.”
19 南方的城尽都关闭, 无人开放; 犹大全被掳掠, 且掳掠净尽。
Mizinda ya ku Negevi yatsekedwa ndipo palibe wina woti nʼkuyitsekula. Yuda yense watengedwa kupita ku ukapolo, watengedwa yense ukapolo.
20 你们要举目观看从北方来的人。 先前赐给你的群众, 就是你佳美的群众, 如今在哪里呢?
Tukula maso ako kuti uwone amene akubwera kuchokera kumpoto. Kodi nkhosa zimene anakusungitsa zili kuti, nkhosa zanu zokongola zija?
21 耶和华立你自己所交的朋友为首,辖制你, 那时你还有什么话说呢? 痛苦岂不将你抓住像产难的妇人吗?
Kodi udzanena chiyani pamene [Yehova] adzakuyikira anthu amene unkanena kuti ndi abale ako akukugonjetsa ndi kukulamulira? Kodi sudzamva zowawa ngati za mayi pa nthawi yake yochira?
22 你若心里说:这一切事为何临到我呢? 你的衣襟揭起, 你的脚跟受伤, 是因你的罪孽甚多。
Ndipo ngati udzadzifunsa kuti, “Kodi zimenezi zandichitikira chifukwa chiyani?” Ndi chifukwa cha machimo anu ambiri kuti zovala zanu zingʼambike ndiponso kuti akuchitireni nkhanza.
23 古实人岂能改变皮肤呢? 豹岂能改变斑点呢? 若能,你们这习惯行恶的便能行善了。
Kodi wa dziko la Kusi nʼkusintha khungu lake, kapena kambuku kusintha mawanga ake? Inunso amene munazolowera kuchita zoyipa simungathe kusintha.
24 所以我必用旷野的风吹散他们, 像吹过的碎秸一样。
“Ine ndidzakumwazani ngati mankhusu amene amawuluka ndi mphepo ya ku chipululu.
25 耶和华说:这是你所当得的, 是我量给你的分; 因为你忘记我, 倚靠虚假。
Limeneli ndiye gawo lanu, chilango chimene ndakukonzerani chifukwa chondiyiwala Ine ndi kutumikira milungu yabodza, akutero Yehova.
26 所以我要揭起你的衣襟, 蒙在你脸上, 显出你的丑陋。
Ine ndidzakwinya zovala zanu mpaka ku maso kuti umaliseche wanu uwonekere.
27 你那些可憎恶之事— 就是在田野的山上行奸淫, 发嘶声,做淫乱的事— 我都看见了。 耶路撒冷啊,你有祸了! 你不肯洁净,还要到几时呢?
Ndaona zonyansa zanu: zigololo zanu, kutchetcherera kwanu ndi ziwerewere zanu, zochitika pa mapiri ndi mʼminda. Tsoka iwe Yerusalemu! Udzakhala wosayeretsedwa pa zachipembedzo mpaka liti?”

< 耶利米书 13 >