< 以赛亚书 36 >
1 希西家王十四年,亚述王西拿基立上来攻击犹大的一切坚固城,将城攻取。
Chaka cha khumi ndi chinayi cha ulamuliro wa Mfumu Hezekiya, Senakeribu mfumu ya ku Asiriya anathira nkhondo mizinda yonse yotetezedwa ya ku Yuda, nayilanda.
2 亚述王从拉吉差遣拉伯沙基率领大军往耶路撒冷,到希西家王那里去。他就站在上池的水沟旁,在漂布地的大路上。
Kenaka mfumu ya ku Asiriya inatuma kazembe wake wankhondo pamodzi ndi gulu lalikulu lankhondo kuchokera ku Lakisi kupita kwa mfumu Hezekiya ku Yerusalemu. Tsono kazembeyo anayima pafupi ndi ngalande yamadzi yochokera ku Dziwe lakumtunda pa msewu wopita ku malo a munda wa mmisiri wochapa zovala.
3 于是希勒家的儿子家宰以利亚敬,并书记舍伯那和亚萨的儿子史官约亚,出来见拉伯沙基。
Panali anthu atatu. Woyamba anali Eliyakimu mwana wa Hilikiya komanso ndiye woyangʼanira nyumba ya mfumu. Wachiwiri anali Sebina amene anali mlembi wa bwalo; ndipo wachitatu anali Yowa mwana wa Asafu komanso anali wolemba zochitika. Anthu awa anatuluka kukakumana ndi kazembe wa ankhondo uja.
4 拉伯沙基对他们说:“你们去告诉希西家说,亚述大王如此说:‘你所倚靠的有什么可仗赖的呢?
Kazembe wa ankhondo anawawuza kuti, “Kamuwuzeni Hezekiya kuti, “Mfumu yayikulu, mfumu ya ku Asiriya ikunena kuti, Kodi chikukulimbitsa mtima ndi chiyani?
5 你说,有打仗的计谋和能力,我看不过是虚话。你到底倚靠谁才背叛我呢?
Iwe ukuti uli ndi luso ndiponso mphamvu pa nkhondo, komatu ukuyankhula mawu opanda pake. Kodi tsono iwe ukudalira yani kuti undiwukire ine?
6 看哪,你所倚靠的埃及是那压伤的苇杖,人若靠这杖,就必刺透他的手。埃及王法老向一切倚靠他的人也是这样。
Taona tsono, iwe ukudalira Igupto, bango lothyokalo, limene limalasa mʼmanja mwa munthu ngati waliyesa ndodo yoyendera! Umo ndi mmene Farao mfumu ya ku Igupto imachitira aliyense amene akuyidalira.
7 你若对我说:我们倚靠耶和华—我们的 神。希西家岂不是将 神的邱坛和祭坛废去,且对犹大和耶路撒冷的人说:你们当在这坛前敬拜吗?
Ndipo ngati ukunena kwa ine kuti, ‘Ife tikudalira Yehova Mulungu wathu,’ kodi si Mulungu yemweyo amene nyumba zake ndi maguwa ake, Hezekiya anachotsa, nawuza anthu a ku Yuda ndi a ku Yerusalemu kuti, ‘Muzipembedza pa guwa lansembe ili?’
8 现在你把当头给我主亚述王,我给你二千匹马,看你这一面骑马的人够不够。
“Ndipo tsopano bwera udzakambirane ndi mbuye wanga, mfumu ya ku Asiriya: Ine ndidzakupatsa akavalo 2,000 ngati ungathe kupeza okwerapo!
9 若不然,怎能打败我主臣仆中最小的军长呢?你竟倚靠埃及的战车马兵吗?
Iwe ungathe bwanji kugonjetsa ngakhale mmodzi mwa akazembe angʼonoangʼono a mbuye wanga, pamene ukudalira Igupto kuti akupatse magaleta ndi anthu okwera pa akavalo.
10 现在我上来攻击毁灭这地,岂没有耶和华的意思吗?耶和华吩咐我说,你上去攻击毁灭这地吧!’”
Kuwonjezera pamenepa, kodi ine ndabwera kudzathira nkhondo ndi kuwononga dziko lino popanda chilolezo cha Yehova? Yehova mwini ndiye anandiwuza kuti ndidzathire nkhondo ndi kuwononga dziko lino.”
11 以利亚敬、舍伯那、约亚对拉伯沙基说:“求你用亚兰言语和仆人说话,因为我们懂得;不要用犹大言语和我们说话,达到城上百姓的耳中。”
Pamenepo Eliyakimu, Sebina ndi Yowa anawuza kazembeyo kuti, “Chonde yankhulani kwa atumiki anufe mʼChiaramu, popeza timachimva. Musayankhule nafe mu Chihebri kuopa kuti anthu onse amene ali pa khomapa angamve.”
12 拉伯沙基说:“我主差遣我来,岂是单对你和你的主说这些话吗?不也是对这些坐在城上、要与你们一同吃自己粪喝自己尿的人说吗?”
Koma kazembeyo anayankha kuti, “Kodi mbuye wanga wandituma kuti ndidzanene zinthu izi kwa mbuye wanu yekha ndi inu nokha basi? Ayi, komanso kwa anthu amene akhala pa khomawa. Iwowa adzadya chimbudzi chawo chomwe ndi kumwa mkodzo wawo womwe monga momwe mudzachitire inuyonso.”
13 于是,拉伯沙基站着,用犹大言语大声喊着说:“你们当听亚述大王的话。
Tsono kazembeyo anayimirira nafuwula mu Chihebri kuti, “Imvani mawu a mfumu yayikulu, mfumu ya ku Asiriya!
14 王如此说:‘你们不要被希西家欺哄了,因他不能拯救你们。
Zimene mfumu ikunena ndi izi: Musalole kuti Hezekiya akunamizeni. Iye sangakupulumutseni!
15 也不要听希西家使你们倚靠耶和华说:耶和华必要拯救我们,这城必不交在亚述王的手中。
Hezekiya asakukakamizeni kudalira Yehova ndi mawu akuti, ‘Ndithu, Yehova adzatipulumutsa; ndipo sadzapereka mzindawu mʼdzanja la mfumu ya ku Asiriya.’
16 不要听希西家的话,因亚述王如此说:你们要与我和好。出来投降我,各人就可以吃自己葡萄树和无花果树的果子,喝自己井里的水。
“Musamumvere Hezekiya. Zimene mfumu ya ku Asiriya ikunena ndi izi: Pangani mtendere ndi ine ndipo mutuluke mu mzinda. Mukatero aliyense wa inu adzadya mphesa ndi nkhuyu za mʼmunda mwake ndiponso adzamwa madzi a mʼchitsime chake,
17 等我来领你们到一个地方,与你们本地一样,就是有五谷和新酒之地,有粮食和葡萄园之地。
mpaka mfumuyo itabwera kudzakutengani kupita ku dziko lofanana ndi lanulo, dziko limene lili ndi tirigu ndi vinyo watsopano, dziko loyenda mkaka ndi uchi.
18 你们要谨防,恐怕希西家劝导你们说:耶和华必拯救我们。列国的神有哪一个救他本国脱离亚述王的手呢?
“Inu musalole kuti Hezekiya akusocheretseni pamene iye akuti, ‘Yehova adzatipulumutsa.’ Kodi alipo mulungu wa anthu a mtundu wina amene anapulumutsa dziko lake mʼdzanja la mfumu ya ku Asiriya?
19 哈马和亚珥拔的神在哪里呢?西法瓦音的神在哪里呢?他们曾救撒马利亚脱离我的手吗?
Kodi ili kuti milungu ya Hamati ndi Aripadi? Ili kuti milungu ya Sefaravaimu? Kodi inapulumutsa Samariya mʼdzanja langa?
20 这些国的神有谁曾救自己的国脱离我的手呢?难道耶和华能救耶路撒冷脱离我的手吗?’”
Kodi ndi milungu iti mwa milungu yonse ya mayiko awa amene anapulumutsa dziko lake mʼdzanja? Nanga tsono Yehova adzapulumutsa Yerusalemu mʼdzanja langa motani?”
21 百姓静默不言,并不回答一句,因为王曾吩咐说:“不要回答他。”
Koma anthu anakhala chete ndipo sanayankhepo kanthu, chifukwa mfumu inawalamula kuti, “Musayankhe.”
22 当下希勒家的儿子家宰以利亚敬和书记舍伯那,并亚萨的儿子史官约亚,都撕裂衣服,来到希西家那里,将拉伯沙基的话告诉了他。
Pamenepo anthu atatu aja Eliyakimu, mwana wa Hilikiya amene ankayangʼanira nyumba ya mfumu; Sebina mlembi wa bwalo; ndi Yowa, mwana wa Asafu mlembi wa zochitika anapita kwa Hezekiya atangʼamba zovala zawo ndipo anamuwuza zonse zimene anayankhula kazembe uja.