< 以赛亚书 21 >

1 论海旁旷野的默示: 有仇敌从旷野,从可怕之地而来, 好像南方的旋风,猛然扫过。
Uthenga wonena za chipululu cha mʼmbali mwa Nyanja. Ankhondo a ku Elamu ndi Mediya adzabwera ngati kamvuluvulu amene akuwomba modutsa mʼmbali ya nyanja, kuchokera ku chipululu, dziko lochititsa mantha.
2 令人凄惨的异象已默示于我。 诡诈的行诡诈,毁灭的行毁灭。 以拦哪,你要上去! 米底亚啊,你要围困! 主说:我使一切叹息止住。
Ine ndaona zinthu zoopsa mʼmasomphenya: Wonyenga akunyenga, wofunkha akufunkha komanso owononga akuwononga. Elamu, yambani nkhondo! Mediya, zingani mzinda! Ine ndidzathetsa mavuto onse amene anayambitsa Ababuloni.
3 所以,我满腰疼痛; 痛苦将我抓住, 好像产难的妇人一样。 我疼痛甚至不能听; 我惊惶甚至不能看。
Chifukwa cha zimenezi thupi langa likunjenjemera ndi mantha, ndikumva ululu ngati wa mayi amene akubereka; ndikuvutika kwambiri ndi zimene ndikumva, ndathedwa nzeru ndi zimene ndikuziona.
4 我心慌张,惊恐威吓我。 我所羡慕的黄昏,变为我的战兢。
Mtima wanga ukugunda, ndipo ndikunjenjemera ndi mantha; chisisira chimene ndakhala ndikuchifuna chasanduka chinthu choopsa kwa ine.
5 他们摆设筵席, 派人守望,又吃又喝。 首领啊,你们起来, 用油抹盾牌。
Ankhondo a ku Elamu ndi Mediya akukonza matebulo, akuyala mphasa, akudya komanso kumwa! Mwadzidzidzi anamva mawu akuti, “Dzukani inu ankhondo, pakani mafuta zishango zanu!”
6 主对我如此说: 你去设立守望的, 使他将所看见的述说。
Zimene Ambuye akunena kwa ine ndi izi; “Pita, kayike mlonda kuti azinena zimene akuziona.
7 他看见军队, 就是骑马的一对一对地来, 又看见驴队,骆驼队, 就要侧耳细听。
Taonani, anthu akubwera ali pa akavalo ndipo akuyenda awiriawiri, okwera pa bulu kapena okwera pa ngamira, mlondayo akhale tcheru kwambiri.”
8 他像狮子吼叫,说: 主啊,我白日常站在望楼上, 整夜立在我守望所。
Ndipo mlondayo anafuwula kuti, “Ambuye anga, tsiku ndi tsiku ndimakhala pa nsanja yolondera; Usiku uliwonse ndimakhala pa malo anga olondera.
9 看哪,有一队军兵骑着马, 一对一对地来。 他就说:巴比伦倾倒了!倾倒了! 他一切雕刻的神像都打碎于地。
Taonani, uyo munthu akubwera atakwera pa galeta ali ndi gulu la akavalo. Mmodzi wa iwo akuti, ‘Babuloni wagwa, wagwa! Mafano onse a milungu yake agwa pansi ndipo aphwanyika!’”
10 我被打的禾稼,我场上的谷啊, 我从万军之耶和华— 以色列的 神那里所听见的,都告诉你们了。
Inu anthu anga opunthidwa ndi kupetedwa ngati tirigu, ine ndikukuwuzani zimene ndamva ndikukuwuzani Uthenga wochokera kwa Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli.
11 论度玛的默示: 有人声从西珥呼问我说: 守望的啊,夜里如何? 守望的啊,夜里如何?
Uthenga wonena za Duma: Munthu wina akundiyitana kuchokera ku Seiri kuti, “Iwe mlonda, usikuwu utha liti? Iwe mlonda, utha liti kodi usikuwu?”
12 守望的说: 早晨将到,黑夜也来。 你们若要问就可以问, 可以回头再来。
Mlonda akuyankha kuti, “Kukucha, koma kudanso. Ngati ukufuna kufunsa, funsa tsopano; ndipo ubwerenso udzafunse.”
13 论阿拉伯的默示: 底但结伴的客旅啊, 你们必在阿拉伯的树林中住宿。
Uthenga wonena za Arabiya: Inu anthu amalonda a ku Dedani, amene usiku mumagona mʼzithukuluzi za ku Arabiya,
14 提玛地的居民拿水来,送给口渴的, 拿饼来迎接逃避的。
perekani madzi kwa anthu aludzu. Inu anthu a ku Tema perekani chakudya kwa anthu othawa nkhondo.
15 因为他们逃避刀剑和出了鞘的刀, 并上了弦的弓与刀兵的重灾。
Iwo akuthawa malupanga, lupanga losololedwa, akuthawa uta wokokakoka ndiponso nkhondo yoopsa.
16 主对我这样说:“一年之内,照雇工的年数,基达的一切荣耀必归于无有。
Zimene Ambuye akunena kwa ine ndi izi: “Chaka chimodzi chisanathe, potsata mmene amawerengera munthu waganyu, ulemerero wonse wa Kedara udzatheratu.
17 弓箭手所余剩的,就是基达人的勇士,必然稀少,因为这是耶和华—以色列的 神说的。”
Mwa anthu okoka uta, ankhondo a ku Kedara opulumuka adzakhala owerengeka.” Wayankhula ndi Yehova Mulungu wa Israeli.

< 以赛亚书 21 >