< 以赛亚书 20 >
1 亚述王撒珥根打发他珥探到亚实突的那年,他珥探就攻打亚实突,将城攻取。
Mʼchaka chimene mkulu wankhondo wotumidwa ndi mfumu ya ku Asiriya, anabwera ku Asidodi ndi kuwuthira nkhondo ndi kuwulanda,
2 那时,耶和华晓谕亚摩斯的儿子以赛亚说:“你去解掉你腰间的麻布,脱下你脚上的鞋。”以赛亚就这样做,露身赤脚行走。
nthawi imeneyo Yehova anawuza Yesaya mwana wa Amozi kuti, “Pita kavule chiguduli ndi nsapato zako.” Ndipo iye anaterodi, ankangoyenda wamaliseche ndiponso wopanda nsapato.
3 耶和华说:“我仆人以赛亚怎样露身赤脚行走三年,作为关乎埃及和古实的预兆奇迹。
Kenaka Yehova anati, “Monga momwe mtumiki wanga Yesaya wakhala akuyendera wamaliseche ndiponso wopanda nsapato kwa zaka zitatu ngati chizindikiro ndi chenjezo kwa dziko la Igupto ndi Kusi,
4 照样,亚述王也必掳去埃及人,掠去古实人,无论老少,都露身赤脚,现出下体,使埃及蒙羞。
momwemonso mfumu ya ku Asiriya idzatenga ukapolo anthu a ku Igupto ndi a ku Kusi, anyamata ndi okalamba. Iwo adzakhala amaliseche ndi opanda nsapato, matako ali pa mtunda. Zimenezi zidzachititsa manyazi Igupto.
5 以色列人必因所仰望的古实,所夸耀的埃及,惊惶羞愧。
Amene ankadalira Kusi, ndiponso amene ankadzitukumula chifukwa cha Igupto adzakhumudwa ndi kuchita manyazi.
6 “那时,这沿海一带的居民必说:‘看哪,我们素所仰望的,就是我们为脱离亚述王逃往求救的,不过是如此!我们怎能逃脱呢?’”
Tsiku limenelo anthu amene amakhala mʼmbali mwa nyanja adzati, ‘Taonani zomwe zawachitikira amene ife tinkawadalira, amene ife tinkathawirako kuti atithandize ndi kutipulumutsa kwa mfumu ya ku Asiriya! Nanga ife tidzapulumuka bwanji?’”