< 以赛亚书 1 >

1 当乌西雅、约坦、亚哈斯、希西家作犹大王的时候,亚摩斯的儿子以赛亚得默示,论到犹大和耶路撒冷。
Masomphenya wonena za Yuda ndi Yerusalemu, amene Yesaya mwana wa Amozi, anaona pa nthawi ya ulamuliro wa Uziya, Yotamu, Ahazi ndi Hezekiya, mafumu a Yuda.
2 天哪,要听!地啊,侧耳而听! 因为耶和华说: 我养育儿女,将他们养大, 他们竟悖逆我。
Tamverani, miyamba inu! Tchera khutu, iwe dziko lapansi! Pakuti Yehova wanena kuti, “Ndinabala ana ndi kuwalera, koma anawo andiwukira Ine.
3 牛认识主人, 驴认识主人的槽, 以色列却不认识; 我的民却不留意。
Ngʼombe imadziwa mwini wake, bulu amadziwa kumene kuli gome la mbuye wake, koma Israeli sadziwa, anthu anga samvetsa konse.”
4 嗐!犯罪的国民, 担着罪孽的百姓; 行恶的种类, 败坏的儿女! 他们离弃耶和华, 藐视以色列的圣者, 与他生疏,往后退步。
Haa, mtundu wochimwa, anthu olemedwa ndi machimo, obadwa kwa anthu ochita zoyipa, ana odzipereka ku zoyipa! Iwo asiya Yehova; anyoza Woyerayo wa Israeli ndipo afulatira Iyeyo.
5 你们为什么屡次悖逆, 还要受责打吗? 你们已经满头疼痛, 全心发昏。
Chifukwa chiyani mukufuna kuti muzingolangidwabe? Chifukwa chiyani mukupitirira kukhala mʼmoyo wowukira? Mutu wanu wonse uli ndi mabala, mtima wanu wonse wafowokeratu.
6 从脚掌到头顶, 没有一处完全的, 尽是伤口、青肿,与新打的伤痕, 都没有收口,没有缠裹, 也没有用膏滋润。
Kuchokera ku phazi mpaka ku mutu palibe pabwino, paliponse pali mikwingwirima ndi zilonda, mabala ali magazi chuchuchu, mabala ake ngosatsuka, ngosamanga ndiponso ngosapaka mafuta ofewetsa.
7 你们的地土已经荒凉; 你们的城邑被火焚毁。 你们的田地在你们眼前为外邦人所侵吞, 既被外邦人倾覆就成为荒凉。
Dziko lanu lasanduka bwinja, mizinda yanu yatenthedwa ndi moto; minda yanu ikukololedwa ndi alendo inu muli pomwepo, dziko lanu lasanduka bwinja monga ngati lagonjetsedwa ndi alendo.
8 仅存锡安城, 好像葡萄园的草棚, 瓜田的茅屋, 被围困的城邑。
Mwana wamkazi wa Ziyoni watsala yekha ngati nsanja mʼmunda wampesa, ngati chisimba mʼmunda wa minkhaka, ngati mzinda wozingidwa ndi nkhondo.
9 若不是万军之耶和华给我们稍留余种, 我们早已像所多玛、蛾摩拉的样子了。
Yehova Wamphamvuzonse akanapanda kutisiyira opulumuka, tikanawonongeka ngati Sodomu, tikanakhala ngati anthu a ku Gomora.
10 你们这所多玛的官长啊, 要听耶和华的话! 你们这蛾摩拉的百姓啊, 要侧耳听我们 神的训诲!
Imvani mawu a Yehova, inu olamulira Sodomu; mverani lamulo la Mulungu wathu, inu anthu a ku Gomora!
11 耶和华说: 你们所献的许多祭物与我何益呢? 公绵羊的燔祭和肥畜的脂油, 我已经够了; 公牛的血,羊羔的血,公山羊的血, 我都不喜悦。
Yehova akuti, “Kodi ndili nazo chiyani nsembe zanu zochuluka?” “Zandikola nsembe zanu zopsereza za nkhosa zazimuna ndiponso mafuta a nyama zonenepa; sindikusangalatsidwanso ndi magazi angʼombe zamphongo ndi a ana ankhosa ndi ambuzi zazimuna.
12 你们来朝见我, 谁向你们讨这些, 使你们践踏我的院宇呢?
Ndani anakulamulirani kuti mubwere nazo pamaso panga? Ndani anakuwuzani kuti muzipondaponda mʼmabwalo a nyumba yanga?
13 你们不要再献虚浮的供物。 香品是我所憎恶的; 月朔和安息日,并宣召的大会, 也是我所憎恶的; 作罪孽,又守严肃会, 我也不能容忍。
Siyani kubweretsa nsembe zachabechabezo! Nsembe zanu zofukiza zimandinyansa Ine. Sindingapirire misonkhano yanu yoyipa, kapenanso zikondwerero za Mwezi Watsopano ndi Masabata.
14 你们的月朔和节期,我心里恨恶, 我都以为麻烦; 我担当,便不耐烦。
Zikondwerero zanu za Mwezi Watsopano ndi masiku anu opatulika ndimadana nazo. Zasanduka katundu wondilemera; ndatopa kuzinyamula.
15 你们举手祷告,我必遮眼不看; 就是你们多多地祈祷,我也不听。 你们的手都满了杀人的血。
Mukamatambasula manja anu popemphera, Ine sindidzakuyangʼanani; ngakhale muchulukitse mapemphero anu, sindidzakumverani. Manja anu ndi odzaza ndi magazi;
16 你们要洗濯、自洁, 从我眼前除掉你们的恶行, 要止住作恶,
sambani, dziyeretseni. Chotsani pamaso panu ntchito zanu zoyipa! Lekani kuchita zoyipa,
17 学习行善, 寻求公平, 解救受欺压的; 给孤儿伸冤, 为寡妇辨屈。
phunzirani kuchita zabwino! Funafunani chilungamo, thandizani oponderezedwa. Tetezani ana amasiye, muwayimirire akazi amasiye pa milandu yawo.”
18 耶和华说: 你们来,我们彼此辩论。 你们的罪虽像朱红,必变成雪白; 虽红如丹颜,必白如羊毛。
Yehova akuti, “Tiyeni tsono tikambe mlandu wanu. Ngakhale machimo anu ali ofiira, adzayera ngati thonje. Ngakhale ali ofiira ngati kapezi, adzayera ngati ubweya wankhosa.
19 你们若甘心听从, 必吃地上的美物,
Ngati muli okonzeka kundimvera mudzadya zinthu zabwino za mʼdziko;
20 若不听从,反倒悖逆, 必被刀剑吞灭。 这是耶和华亲口说的。
koma mukakana ndi kuwukira mudzaphedwa ndi lupanga.” Pakuti Yehova wayankhula.
21 可叹,忠信的城变为妓女! 从前充满了公平, 公义居在其中, 现今却有凶手居住。
Taonani momwe mzinda wokhulupirika wasandukira wadama! Mzinda umene kale unali wodzaza ndi chiweruzo cholungama; mu mzindamo munali chilungamo, koma tsopano muli anthu opha anzawo!
22 你的银子变为渣滓; 你的酒用水搀对。
Siliva wako wasanduka wachabechabe, vinyo wako wabwino wasungunulidwa ndi madzi.
23 你的官长居心悖逆, 与盗贼作伴, 各都喜爱贿赂, 追求赃私。 他们不为孤儿伸冤; 寡妇的案件也不得呈到他们面前。
Atsogoleri ako ndi owukira, anthu ogwirizana ndi mbala; onse amakonda ziphuphu ndipo amathamangira mphatso. Iwo sateteza ana amasiye; ndipo samvera madandawulo a akazi amasiye.
24 因此,主—万军之耶和华、 以色列的大能者说: 哎!我要向我的对头雪恨, 向我的敌人报仇。
Nʼchifukwa chake Ambuye Yehova Wamphamvu, Wamphamvuyo wa Israeli, akunena kuti, “Haa, odana nane ndidzawatha, ndipo ndidzawabwezera ndekha adani anga.
25 我必反手加在你身上, 炼尽你的渣滓, 除净你的杂质。
Ndidzatambasula dzanja langa kuti ndilimbane nawe; ndidzasungunula machimo ako nʼkuwachotsa, monga mmene amachotsera dzimbiri ndi mankhwala.
26 我也必复还你的审判官,像起初一样, 复还你的谋士,像起先一般。 然后,你必称为公义之城, 忠信之邑。
Ndidzabwezeretsa oweruza ako ngati masiku amakedzana, aphungu ako ndidzawabwezeretsa ngati poyamba paja. Kenaka iweyo udzatchedwa mzinda wolungama, mzinda wokhulupirika.”
27 锡安必因公平得蒙救赎; 其中归正的人必因公义得蒙救赎。
Ziyoni adzawomboledwa mwa chiweruzo cholungama, anthu ake olapadi adzapulumutsidwa mwachilungamo.
28 但悖逆的和犯罪的必一同败亡; 离弃耶和华的必致消灭。
Koma owukira ndi ochimwa adzawawonongera pamodzi, ndipo amene asiya Yehova adzatheratu.
29 那等人必因你们所喜爱的橡树抱愧; 你们必因所选择的园子蒙羞。
“Mudzachita nayo manyazi mitengo ya thundu imene inkakusangalatsani; mudzagwetsa nkhope chifukwa cha minda imene munayipatula.
30 因为,你们必如叶子枯干的橡树, 好像无水浇灌的园子。
Mudzakhala ngati mtengo wa thundu umene masamba ake akufota, mudzakhala ngati munda wopanda madzi.
31 有权势的必如麻瓤; 他的工作好像火星, 都要一同焚毁,无人扑灭。
Munthu wamphamvu adzasanduka ngati udzu wowuma, ndipo ntchito zake zidzakhala ngati mbaliwali; motero zonse zidzayakira limodzi, popanda woti azimitse motowo.”

< 以赛亚书 1 >