< 何西阿书 10 >
1 以色列是茂盛的葡萄树,结果繁多。 果子越多,就越增添祭坛; 地土越肥美,就越造美丽的柱像。
Israeli anali mpesa wotambalala; anabereka zipatso zambiri. Pamene zipatso zawo zinanka zichuluka, anawonjezera kumanga maguwa ansembe. Pamene dziko lake linkatukuka, anakongoletsa miyala yake yopatulika.
2 他们心怀二意, 现今要定为有罪。 耶和华必拆毁他们的祭坛, 毁坏他们的柱像。
Mtima wawo ndi wonyenga ndipo tsopano ayenera kulangidwa chifukwa cha kulakwa kwawo. Yehova adzagumula maguwa awo ansembe ndi kuwononga miyala yawo yopatulika.
3 他们必说:我们没有王, 因为我们不敬畏耶和华。 王能为我们做什么呢?
Pamenepo anthuwo adzanena kuti, “Ife tilibe mfumu chifukwa sitinaope Yehova. Koma ngakhale tikanakhala ndi mfumu, kodi mfumuyo ikanatichitira chiyani?”
4 他们为立约说谎言,起假誓; 因此,灾罚如苦菜滋生在田间的犁沟中。
Mafumu amalonjeza zambiri, amalumbira zabodza pochita mapangano. Kotero maweruzo amaphuka ngati zitsamba zakupha mʼmunda umene walimidwa.
5 撒马利亚的居民必因伯·亚文的牛犊惊恐; 崇拜牛犊的民和喜爱牛犊的祭司 都必因荣耀离开它,为它悲哀。
Anthu amene amakhala mu Samariya akuchita mantha chifukwa cha fano la mwana wangʼombe ku Beti-Aveni. Anthu ake adzalirira fanolo, chimodzimodzinso ansembe ake adamawo, amene anakondwera ndi kukongola kwake, chifukwa lachotsedwa pakati pawo ndi kupita ku ukapolo.
6 人必将牛犊带到亚述当作礼物, 献给耶雷布王。 以法莲必蒙羞; 以色列必因自己的计谋惭愧。
Fanolo lidzatengedwa kupita ku Asiriya ngati mphatso kwa mfumu yayikulu. Efereimu adzachititsidwa manyazi chifukwa cha mafano ake amitengo.
7 至于撒马利亚,她的王必灭没, 如水面的沫子一样。
Samariya ndi mfumu yake adzatengedwa kupita kutali ngati kanthambi koyenda pa madzi.
8 伯·亚文的邱坛— 就是以色列取罪的地方必被毁灭; 荆棘和蒺藜必长在他们的祭坛上。 他们必对大山说:遮盖我们! 对小山说:倒在我们身上!
Malo opembedzerako mafano a ku Aveni adzawonongedwa. Ili ndiye tchimo la Israeli. Minga ndi mitungwi zidzamera ndi kuphimba maguwa awo ansembe. Kenaka anthu adzawuza mapiri kuti, “Tiphimbeni!” ndipo adzawuza zitunda kuti, “Tigwereni!”
9 以色列啊, 你从基比亚的日子以来时常犯罪。 你们的先人曾站在那里, 现今住基比亚的人 以为攻击罪孽之辈的战事临不到自己。
“Iwe Israeli, wachimwa kuyambira mʼmasiku a Gibeya, ndipo wakhala uli pomwepo. Kodi nkhondo sinagonjetse anthu ochita zoyipa ku Gibeya?
10 我必随意惩罚他们。 他们为两样的罪所缠; 列邦的民必聚集攻击他们。
Pamene ndifunire, ndidzalanga anthuwo; mitundu ya anthu idzasonkhanitsidwa kudzalimbana nawo, kuwayika mʼndende chifukwa cha uchimo wawo waukulu.
11 以法莲是驯良的母牛犊,喜爱踹谷, 我却将轭加在它肥美的颈项上, 我要使以法莲拉套。 犹大必耕田; 雅各必耙地。
Efereimu ndi mwana wangʼombe wamkazi wophunzitsidwa amene amakonda kupuntha tirigu, choncho Ine ndidzayika goli mʼkhosi lake lokongolalo. Ndidzasenzetsa Efereimu goli, Yuda ayenera kulima, ndipo Yakobo ayenera kutipula.
12 你们要为自己栽种公义, 就能收割慈爱。 现今正是寻求耶和华的时候; 你们要开垦荒地,等他临到, 使公义如雨降在你们身上。
Mufese nokha chilungamo ndipo mudzakolola chipatso cha chikondi changa chosasinthika. Ndipo tipulani munda wanu wosalimidwawo; pakuti ino ndi nthawi yofunafuna Yehova, mpaka Iye atabwera kudzakugwetserani mivumbi ya chilungamo.
13 你们耕种的是奸恶, 收割的是罪孽, 吃的是谎话的果子。 因你倚靠自己的行为, 仰赖勇士众多,
Koma inu munadzala zolakwa, mwakolola zoyipa; mwadya chipatso cha chinyengo. Chifukwa mumadalira mphamvu zanu ndiponso ankhondo anu ochulukawo,
14 所以在这民中必有哄嚷之声, 你一切的保障必被拆毁, 就如沙勒幔在争战的日子拆毁伯·亚比勒, 将其中的母子一同摔死。
phokoso lankhondo lidzamveka pakati pa anthu anga kotero kuti malinga anu onse adzawonongeka, monga momwe Salimani anawonongera Beti-Aribeli pa nthawi ya nkhondo; pamene anapha amayi pamodzi ndi ana awo omwe.
15 因他们的大恶, 伯特利必使你们遭遇如此。 到了黎明,以色列的王必全然灭绝。
Momwemonso zidzakuchitikira, iwe Beteli chifukwa kuyipa kwako ndi kwakukulu. Tsiku limeneli likadzafika, mfumu ya Israeli idzawonongedwa kwathunthu.