< 希伯来书 1 >
Kale lija Mulungu ankayankhula ndi makolo athu pa nthawi zosiyanasiyana ndiponso mwa njira zosiyanasiyana kudzera mwa aneneri.
2 就在这末世借着他儿子晓谕我们;又早已立他为承受万有的,也曾借着他创造诸世界。 (aiōn )
Koma masiku otsiriza ano, Mulungu wayankhula nafe kudzera mwa Mwana wake. Mwanayu anamusankha kuti akhale mwini wa zinthu zonse, ndiponso Mulungu analenga dziko lonse kudzera mwa Iye. (aiōn )
3 他是 神荣耀所发的光辉,是 神本体的真像,常用他权能的命令托住万有。他洗净了人的罪,就坐在高天至大者的右边。
Mwanayo ndiye kuwala kwa ulemerero wa Mulungu, chithunzithunzi chenicheni cha khalidwe lake. Iyeyu amachirikiza zinthu zonse ndi mphamvu ya mawu ake. Iye atayeretsa anthu kuchoka ku machimo awo, anakhala pansi kumwamba kudzanja lamanja la Mulungu waulemerero.
4 他所承受的名,既比天使的名更尊贵,就远超过天使。
Mwanayu ndi wamkulu koposa angelo, monga momwe dzina limene analandira limaposa dzina la angelo.
5 所有的天使, 神从来对哪一个说: 你是我的儿子, 我今日生你? 又指着哪一个说: 我要作他的父, 他要作我的子?
Kodi ndi kwa mngelo uti, kumene Mulungu anati, “Iwe ndiwe mwana wanga; Ine lero ndakhala Atate ako.” Kapena kunenanso kuti, “Ine ndidzakhala abambo ake; iye adzakhala mwana wanga.”
6 再者, 神使长子到世上来的时候,就说: 神的使者都要拜他。
Pamene Mulungu amatuma Mwana wake woyamba kubadwa ku dziko lapansi anati, “Angelo onse a Mulungu amupembedze Iye.”
7 论到使者,又说: 神以风为使者, 以火焰为仆役;
Iye ponena za angelo akuti, “Mulungu amasandutsa angelo ake mphepo, amasandutsa atumiki ake malawi amoto.”
8 论到子却说: 神啊,你的宝座是永永远远的; 你的国权是正直的。 (aiōn )
Koma za Mwana wake akuti, “Inu Mulungu, mpando wanu waufumu udzakhala mpaka muyaya, ndipo mudzaweruza molungama mu ufumu wanu. (aiōn )
9 你喜爱公义,恨恶罪恶; 所以 神,就是你的 神,用喜乐油膏你, 胜过膏你的同伴;
Mwakonda chilungamo ndi kudana ndi zoyipa; Nʼchifukwa chake, Mulungu wanu wakukwezani kuposa anzanu pokudzozani mafuta osonyeza chimwemwe.”
10 又说:主啊,你起初立了地的根基; 天也是你手所造的。
Mulungu akutinso, “Ambuye, pachiyambi Inu munayika maziko a dziko lapansi; ndipo zakumwambako ndi ntchito za manja anu.
11 天地都要灭没,你却要长存。 天地都要像衣服渐渐旧了;
Zimenezi zidzatha, koma Inu ndinu wachikhalire. Izo zidzatha ngati zovala.
12 你要将天地卷起来,像一件外衣, 天地就都改变了。 惟有你永不改变; 你的年数没有穷尽。
Mudzazipindapinda ngati chofunda; ndipo zidzasinthidwa ngati chovala. Koma Inu simudzasintha, ndipo zaka zanu sizidzatha.”
13 所有的天使, 神从来对哪一个说: 你坐在我的右边, 等我使你仇敌作你的脚凳?
Kodi ndi kwa Mngelo uti kumene Mulungu ananenapo kuti, “Khala kudzanja langa lamanja mpaka nditapanga adani ako kukhale chopondapo mapazi ako.”
14 天使岂不都是服役的灵、奉差遣为那将要承受救恩的人效力吗?
Kodi angelo onse si mizimu yotumikira odzalandira chipulumutso?