< 创世记 7 >

1 耶和华对挪亚说:“你和你的全家都要进入方舟;因为在这世代中,我见你在我面前是义人。
Ndipo Yehova anati kwa Nowa, “Lowa mu chombo iwe ndi banja lako lonse, chifukwa ndaona kuti ndiwe wolungama mu mʼbado uwu.
2 凡洁净的畜类,你要带七公七母;不洁净的畜类,你要带一公一母;
Pa mtundu uliwonse wa nyama zoti nʼkudya utengepo zazimuna zisanu ndi ziwiri ndi zazikazi zisanu ndi ziwirinso. Koma pa mtundu wa nyama iliyonse yosati nʼkudya utengepo zazimuna ziwiri ndi zazikazi ziwirinso.
3 空中的飞鸟也要带七公七母,可以留种,活在全地上;
Chimodzimodzinso mbalame, utenge zisanu ndi ziwiri zazimuna ndi zisanu ndi ziwiri zazikazi za mtundu uliwonse kuti mitundu yawo isungike ndi moyo pa dziko lonse lapansi.
4 因为再过七天,我要降雨在地上四十昼夜,把我所造的各种活物都从地上除灭。”
Pakapita masiku asanu ndi awiri ndidzagwetsa mvula pa dziko lapansi kwa masiku makumi anayi usana ndi usiku ndipo ndidzawononga cha moyo chilichonse chimene ndinachipanga pa dziko lapansi.”
5 挪亚就遵着耶和华所吩咐的行了。
Ndipo Nowa anachita zonse zimene Yehova anamulamulira.
6 当洪水泛滥在地上的时候,挪亚整六百岁。
Pamene chigumula chinabwera pa dziko lapansi Nowa anali ndi zaka 600.
7 挪亚就同他的妻和儿子儿妇都进入方舟,躲避洪水。
Ndipo Nowa, ana ake aamuna, mkazi wake, pamodzi ndi ana ake aakazi analowa mu chombo chija kuthawa madzi a chigumula.
8 洁净的畜类和不洁净的畜类,飞鸟并地上一切的昆虫,
Nyama zoti nʼkudya ndi nyama zosadyedwa, mbalame, pamodzi ndi nyama zokwawa zonse zinadza kwa Nowa ziwiriziwiri ndi kulowa mʼchombomo.
9 都是一对一对地,有公有母,到挪亚那里进入方舟,正如 神所吩咐挪亚的。
Ndipo Nowa anatenga ziwiriziwiri, yayimuna ndi yayikazi monga anamulamulira Mulungu.
10 过了那七天,洪水泛滥在地上。
Patapita masiku asanu ndi awiri chigumula chinabwera pa dziko lapansi.
11 当挪亚六百岁,二月十七日那一天,大渊的泉源都裂开了,天上的窗户也敞开了,
Pa tsiku la 17 la mwezi wachiwiri, Nowa ali ndi zaka 600, akasupe onse akuya kwambiri anasefuka ndiponso zitseko za madzi akumwamba zinatsekuka.
12 四十昼夜降大雨在地上。
Ndipo mvula inagwa pa dziko lapansi masiku makumi anayi usana ndi usiku.
13 正当那日,挪亚和他三个儿子闪、含、雅弗,并挪亚的妻子和三个儿妇,都进入方舟。
Linali tsiku lomwelo pamene Nowa ndi ana ake aamuna, Semu, Hamu ndi Yafeti, pamodzi ndi mkazi wake ndi akazi a ana ake atatu aja analowa mu chombo.
14 他们和百兽,各从其类,一切牲畜,各从其类,爬在地上的昆虫,各从其类,一切禽鸟,各从其类,都进入方舟。
Iwowa analowa mʼchombomo pamodzi ndi nyama iliyonse ya kutchire monga mwa mtundu wake, ziweto zonse monga mwa mitundu yawo, nyama yokwawa iliyonse monga mwa mtundu wake ndi mbalame iliyonse monga mwa mtundu wake.
15 凡有血肉、有气息的活物,都一对一对地到挪亚那里,进入方舟。
Nowa analowa mu chombo muja pamodzi ndi zamoyo zonse.
16 凡有血肉进入方舟的,都是有公有母,正如 神所吩咐挪亚的。耶和华就把他关在方舟里头。
Iye analowa nazo zazimuna ndi zazikazi monga mmene Mulungu anamulamulira. Kenaka Yehova anatseka pa khomo.
17 洪水泛滥在地上四十天,水往上长,把方舟从地上漂起。
Chigumula chinagwa pa dziko la pansi kwa masiku makumi anayi. Madzi anayamba kuchuluka ndipo ananyamula chombo chija ndi kuchiyandamitsa pamwamba pa dziko.
18 水势浩大,在地上大大地往上长,方舟在水面上漂来漂去。
Madzi anafika mwamphamvu ndipo anachulukirachulukira pa dziko lapansi moti chombo chinayandama pamwamba pa madziwo.
19 水势在地上极其浩大,天下的高山都淹没了。
Madzi a chigumula anabwerabe molimbika motero kuti mapiri ataliatali onse a pa dziko anamizidwa.
20 水势比山高过十五肘,山岭都淹没了。
Madzi anakwera namiza mapiri kwa mamita pafupifupi asanu ndi awiri.
21 凡在地上有血肉的动物,就是飞鸟、牲畜、走兽,和爬在地上的昆虫,以及所有的人,都死了。
Chamoyo chilichonse choyenda pa dziko lapansi chinafa: mbalame, ziweto, nyama zakuthengo, miyandamiyanda ya zonse zolengedwa za pa dziko lapansi pamodzi ndi anthu.
22 凡在旱地上、鼻孔有气息的生灵都死了。
Chilichonse chamoyo, chokhala pa mtunda chinafa.
23 凡地上各类的活物,连人带牲畜、昆虫,以及空中的飞鸟,都从地上除灭了,只留下挪亚和那些与他同在方舟里的。
Chamoyo chilichonse pa dziko lapansi chinawonongedwa, kuyambira munthu, nyama, zokwawa ndi mbalame. Nowa yekha ndiye anatsala pamodzi ndi onse amene anali naye.
24 水势浩大,在地上共一百五十天。
Madziwo anadzaza dziko lonse lapansi kwa masiku 150.

< 创世记 7 >

The Great Flood
The Great Flood