< 以西结书 39 >

1 “人子啊,你要向歌革发预言攻击他,说主耶和华如此说:罗施、米设、土巴的王歌革啊,我与你为敌。
“Iwe mwana wa munthu, nenera modzudzula Gogi ndi kumuwuza kuti Ine Ambuye Yehova ndikuti: ‘Ine ndikudana nawe, iwe Gogi, kalonga wamkulu wa Mesaki ndi Tubala.
2 我必调转你,领你前往,使你从北方的极处上来,带你到以色列的山上。
Ine ndidzakuzunguza ndi kukupirikitsira kutsogolo. Ndidzakutenga kuchokera kutali kumpoto ndi kukutumiza kuti ukalimbane ndi anthu a ku mapiri a Israeli.
3 我必从你左手打落你的弓,从你右手打掉你的箭。
Kenaka Ine ndidzathyola uta wa mʼdzanja lako lamanzere ndipo ndidzagwetsa mivi ya mʼdzanja lako lamanja.
4 你和你的军队,并同着你的列国人,都必倒在以色列的山上。我必将你给各类的鸷鸟和田野的走兽作食物。
Udzagwa ku mapiri a ku Israeli, iwe ndi magulu ako onse ankhondo ndiponso mitundu ya anthu imene ili nawe. Ndidzakusandutsa chakudya cha mitundu yonse ya mbalame zodya nyama, ndiponso cha zirombo zakuthengo.
5 你必倒在田野,因为我曾说过。这是主耶和华说的。
Udzafera pa mtetete kuthengo, pakuti Ine ndayankhula. Ndikutero Ine Ambuye Yehova.
6 我要降火在玛各和海岛安然居住的人身上,他们就知道我是耶和华。
Ndidzatumiza moto pa Magogi ndi pa onse amene amakhala mwamtendere mʼmbali mwa nyanja. Choncho adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.’
7 “我要在我民以色列中显出我的圣名,也不容我的圣名再被亵渎,列国人就知道我是耶和华—以色列中的圣者。
“Ndidzachititsa kuti dzina langa loyera lidziwike pakati pa anthu anga Israeli. Sindidzalola kuti dzina langa liyipitsidwenso, ndipo mitundu ya anthu idzadziwa kuti Ine Yehova ndine Woyera mu Israeli.
8 主耶和华说:这日事情临近,也必成就,乃是我所说的日子。
Zikubwera! Ndipo zidzachitikadi, ndikutero Ine Ambuye Yehova. Ndiye tsiku limene ndinanena lija.
9 “住以色列城邑的人必出去和捡器械,就是大小盾牌、弓箭、梃杖、枪矛,都当柴烧火,直烧七年,
“Pamenepo okhala mʼmizinda ya Israeli adzatuluka ndipo adzasonkhanitsa zida zankhondo kuti zikhale nkhuni ndipo adzazitentha; zishango ndi lihawo, mauta ndi mivi, zibonga za nkhondo ndi mikondo. Adzazisonkhera moto kwa zaka zisanu ndi ziwiri.
10 甚至他们不必从田野捡柴,也不必从树林伐木;因为他们要用器械烧火,并且抢夺那抢夺他们的人,掳掠那掳掠他们的人。这是主耶和华说的。”
Iwo sadzatolera nkhuni kuthengo kapena kukadula ku nkhalango, chifukwa adzasonkhera moto zidazo. Ndipo iwo adzafunkha amene anawafunkhawo, ndi kulanda chuma cha amene anawalanda, ndikutero Ine Ambuye Yehova.
11 “当那日,我必将以色列地的谷,就是海东人所经过的谷,赐给歌革为坟地,使经过的人到此停步。在那里人必葬埋歌革和他的群众,就称那地为哈们·歌革谷。
“Pa tsiku limenelo ndidzamupatsa Gogi manda mu Israeli, mʼchigwa cha apaulendo, kummawa kwa Nyanja Yakufa. Mandawo adzatseka njira ya apaulendo, chifukwa Gogi ndi gulu lake lankhondo adzayikidwa kumeneko. Ndipo chigwacho chidzatchedwa chigwa cha gulu lankhondo la Gogi.
12 以色列家的人必用七个月葬埋他们,为要洁净全地。
“Nyumba ya Israeli idzakhala ikukwirira mitembo kwa miyezi isanu ndi iwiri ndi cholinga choyeretsa dziko.
13 全地的居民都必葬埋他们。当我得荣耀的日子,这事必叫他们得名声。这是主耶和华说的。
Anthu onse a mʼdzikomo adzakwirira nawo mitembo. Ntchito imeneyo adzatchuka nayo pa tsiku limene ndidzaonetsa ulemerero wanga. Ndikutero Ine Ambuye Yehova.
14 他们必分派人时常巡查遍地,与过路的人一同葬埋那剩在地面上的尸首,好洁净全地。过了七个月,他们还要巡查。
“Patapita miyezi isanu ndi iwiri adzalemba ntchito anthu ena odzayenda mʼdziko lonse kufunafuna mitembo imene inatsalira nʼkumayikwirira. Choncho adzayeretseratu dzikolo.
15 巡查遍地的人要经过全地,见有人的骸骨,就在旁边立一标记,等葬埋的人来将骸骨葬在哈们·歌革谷。
Poyenda mʼdzikomo azidzati akaona fupa la munthu azidzayikapo chizindikiro pambali pake mpaka okumba manda atakalikwirira fupalo ku chigwa cha gulu lankhondo la Gogi.
16 他们必这样洁净那地,并有一城名叫哈摩那。
(Komwekonso kudzakhala mzinda wotchedwa Gulu la nkhondo). Ndipo potero adzayeretsa dziko.
17 “人子啊,主耶和华如此说:你要对各类的飞鸟和田野的走兽说:你们聚集来吧,要从四方聚到我为你们献祭之地,就是在以色列山上献大祭之地,好叫你们吃肉、喝血。
“Tsono iwe mwana wa munthu, Ine Ambuye Yehova ndikuti: Itana mbalame za mitundu yonse ndi zirombo zonse zakuthengo ndipo uziwuze kuti, ‘Sonkhanani ndipo bwerani kuchokera ku mbali zonse ku nsembe imene ndikukonzerani inu, nsembe yayikulu pa mapiri a Israeli. Kumeneko inu mudzadya mnofu ndi kumwa magazi.
18 你们必吃勇士的肉,喝地上首领的血,就如吃公绵羊、羊羔、公山羊、公牛,都是巴珊的肥畜。
Mudzadya mnofu wa anthu ankhondo amphamvu ndi kumwa magazi a akalonga a dziko lapansi. Onsewo anaphedwa ngati nkhosa zazimuna, ana ankhosa onenepa, mbuzi ndiponso ngati ngʼombe zazimuna zonenepa za ku Basani.
19 你们吃我为你们所献的祭,必吃饱了脂油,喝醉了血。
Ku phwando lansembe limene ndikukonzera inulo, mudzadya zonona mpaka kukhuta ndi kumwa magazi mpaka kuledzera.
20 你们必在我席上饱吃马匹和坐车的人,并勇士和一切的战士。这是主耶和华说的。”
Pa tebulo langa mudzakhuta pakudya akavalo ndi okwerapo ake, anthu amphamvu ndi asilikali amitundumitundu,’ ndikutero Ine Ambuye Yehova.
21 “我必显我的荣耀在列国中;万民就必看见我所行的审判与我在他们身上所加的手。
“Ine ndidzaonetsa ulemerero wanga pakati pa anthu a mitundu ina, ndipo adzaona mmene ndidzawalangire ndikadzayika dzanja langa pa iwo.
22 这样,从那日以后,以色列家必知道我是耶和华—他们的 神。
Kuyambira tsiku limenelo mpaka mʼtsogolo Aisraeli adzadziwa kuti Ine ndine Yehova Mulungu wawo.
23 列国人也必知道以色列家被掳掠是因他们的罪孽。他们得罪我,我就掩面不顾,将他们交在敌人手中,他们便都倒在刀下。
Ndipo anthu a mitundu ina adzadziwa kuti anthu a Israeli anatengedwa ukapolo chifukwa cha tchimo lawo, chifukwa anali osakhulupirika kwa Ine. Choncho Ine ndinawabisira nkhope yanga ndi kuwapereka kwa adani awo. Motero anaphedwa pa nkhondo.
24 我是照他们的污秽和罪过待他们,并且我掩面不顾他们。”
Ndinawachita zimenezi chifukwa cha kunyansa kwawo ndi zolakwa zawo, ndipo ndinawabisira nkhope yanga.
25 主耶和华如此说:“我要使雅各被掳的人归回,要怜悯以色列全家,又为我的圣名发热心。
“Nʼchifukwa chake Ine Ambuye Yehova ndikuti: Tsopano ndidzakhazikanso pa bwino banja la Yakobo. Ndidzachitira chifundo Aisraeli onse, ndipo ndidzateteza dzina langa loyera.
26 他们在本地安然居住,无人惊吓,是我将他们从万民中领回,从仇敌之地召来。我在许多国的民眼前,在他们身上显为圣的时候,他们要担当自己的羞辱和干犯我的一切罪。
Anthuwo akadzakhala mwamtendere mʼdziko lawo popanda wina wowaopseza, pamenepo adzayiwala zamanyazi zawo zimene zinawachitikira chifukwa chosandikhulupirira Ine.
Ndidzawabwezeranso kwawo kuchokera pakati pa anthu a mitundu ina ndipo ndidzawasonkhanitsa kuchokera ku mayiko a adani awo. Poteropo ndidzaonetsa pamaso pa anthu a mitundu yambiri kuti ndine Woyera.
28 因我使他们被掳到外邦人中,后又聚集他们归回本地,他们就知道我是耶和华—他们的 神;我必不再留他们一人在外邦。
Pamenepo iwo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova Mulungu wawo, ngakhale kuti ndinawapereka ku ukapolo pakati pa anthu a mitundu ina. Ine ndidzawasonkhanitsanso ku dziko lawo osasiyako wina mʼmbuyo.
29 我也不再掩面不顾他们,因我已将我的灵浇灌以色列家。这是主耶和华说的。”
Ine sindidzawabisiranso nkhope yanga, pakuti ndidzathira Mzimu wanga pa Aisraeli. Ndikutero Ine Ambuye Yehova.”

< 以西结书 39 >