< 以西结书 20 >

1 第七年五月初十日,有以色列的几个长老来求问耶和华,坐在我面前。
Tsiku lakhumi la mwezi wachisanu, chaka chachisanu ndi chiwiri, ena mwa akuluakulu a Israeli anabwera kudzapempha nzeru kwa Yehova, ndipo anakhala pansi pamaso panga.
2 耶和华的话临到我说:
Tsono Yehova anandiyankhula nati:
3 “人子啊,你要告诉以色列的长老说,主耶和华如此说:你们来是求问我吗?主耶和华说:我指着我的永生起誓,我必不被你们求问。
“Iwe mwana wa munthu, ayankhule akuluakulu a Israeli ndi kuwawuza kuti, ‘Ambuye Yehova akuti: Kodi mwabwera kudzapempha nzeru kwa Ine? Ndithu pali Ine wamoyo, Ine sindidzakulolani kupempha nzeru kwa Ine, akutero Ambuye Yehova.’
4 人子啊,你要审问审问他们吗?你当使他们知道他们列祖那些可憎的事,
“Kodi uwaweruza? Iwe mwana wa munthu, kodi ugamula mlandu wawo? Uwadziwitse tsono zonyansa zimene anachita makolo awo, uwawuze kuti,
5 对他们说,主耶和华如此说:当日我拣选以色列,向雅各家的后裔起誓,在埃及地将自己向他们显现,说:我是耶和华—你们的 神。
‘Ambuye Yehova akuti: Pa tsiku limene ndinasankha Israeli, ndinalumbira kwa zidzukulu za nyumba ya Yakobo ndipo ndinadziwulula kwa iwo ku Igupto. Ndinalumbira ndi kuwawuza kuti: Ine ndine Yehova Mulungu wanu.
6 那日我向他们起誓,必领他们出埃及地,到我为他们察看的流奶与蜜之地;那地在万国中是有荣耀的。
Pa tsiku limenelo ndinalumbira kwa iwo kuti ndidzawatulutsa mʼdziko la Igupto ndi kupita nawo ku dziko limene ndinawapezera, dziko la mwana alirenji, dziko lokongola kwambiri kupambana mayiko ena.
7 我对他们说,你们各人要抛弃眼所喜爱那可憎之物,不可因埃及的偶像玷污自己。我是耶和华—你们的 神。
Ndipo ndinawawuza kuti, ‘Aliyense ataye zinthu zonse zonyansa zimene ankasangalala nazo, ndipo musadziyipitse ndi mafano a Igupto, Ine ndine Yehova Mulungu wanu.’
8 他们却悖逆我,不肯听从我,不抛弃他们眼所喜爱那可憎之物,不离弃埃及的偶像。 “我就说,我要将我的忿怒倾在他们身上,在埃及地向他们成就我怒中所定的。
“‘Koma iwo anandiwukira ndipo sanafune kundimvera. Palibe amene anataya zonyansa zonse zimene ankasangalala nazo. Panalibenso amene anasiya mafano a ku Igupto. Tsono ndinaganiza zowakhuthulira ukali wanga ndi kuwaonetsa mkwiyo wanga mʼdziko la Igupto momwemo.
9 我却为我名的缘故没有这样行,免得我名在他们所住的列国人眼前被亵渎;我领他们出埃及地,在这列国人的眼前将自己向他们显现。
Koma sindinachite zimenezi chifukwa cha dzina langa, kuti lisayipitsidwe pakati pa anthu a mitundu ina amene ankakhala pakati pawo. Paja ndinali nditaonetsa mphamvu zanga pamaso pa mitunduyo potulutsa Aisraeli mʼdziko la Igupto.
10 这样,我就使他们出埃及地,领他们到旷野,
Choncho ndinawatulutsa mʼdziko la Igupto ndi kubwera nawo mʼchipululu.
11 将我的律例赐给他们,将我的典章指示他们;人若遵行就必因此活着。
Ndinawapatsa malangizo anga ndi kuwadziwitsa malamulo anga amene munthu aliyense akawamvera adzakhala ndi moyo.
12 又将我的安息日赐给他们,好在我与他们中间为证据,使他们知道我—耶和华是叫他们成为圣的。
Ndinawapatsanso Masabata ngati chizindikiro pakati pathu, kuti adziwe kuti Ine Yehova ndinawapatula.
13 以色列家却在旷野悖逆我,不顺从我的律例,厌弃我的典章(人若遵行就必因此活着),大大干犯我的安息日。 “我就说,要在旷野将我的忿怒倾在他们身上,灭绝他们。
“‘Komabe anthu a Israeli anandiwukira mʼchipululu. Iwo sanatsatire malangizo anga koma anakana malamulo anga amene munthu aliyense akawamvera adzakhala ndi moyo. Ndipo anayipitsa kotheratu Masabata anga. Choncho, ndinaganiza zowakhuthulira ukali wanga ndi kuwawononga mʼchipululu.
14 我却为我名的缘故,没有这样行,免得我的名在我领他们出埃及的列国人眼前被亵渎。
Koma sindinachite zimenezi chifukwa cha dzina langa, kuti lisayipitsidwe pakati pa anthu a mitundu ina amene anandiona ndikutulutsa Aisraeliwo mu Igupto.
15 并且我在旷野向他们起誓,必不领他们进入我所赐给他们流奶与蜜之地(那地在万国中是有荣耀的);
Ndinalumbiranso kwa iwo mʼchipululu muja, nditakweza dzanja, kuti sindidzawalowetsanso mʼdziko limene ndinawapatsa, dziko la mwana alirenji, lokoma kwambiri kuposa mayiko ena onse.
16 因为他们厌弃我的典章,不顺从我的律例,干犯我的安息日,他们的心随从自己的偶像。
Paja anakana malamulo anga, sanatsatire malangizo anga ndipo anayipitsa masabata anga. Mitima yawo inakonda mafano.
17 虽然如此,我眼仍顾惜他们,不毁灭他们,不在旷野将他们灭绝净尽。
Komabe ndinawamvera chisoni ndipo sindinawawononge kapena kuwatheratu mʼchipululu.
18 “我在旷野对他们的儿女说:不要遵行你们父亲的律例,不要谨守他们的恶规,也不要因他们的偶像玷污自己。
Tsono kwa ana awo mʼchipululu ndinati, ‘Musatsatire malangizo a makolo anu kapena kusunga malamulo awo kapena kudziyipitsa ndi mafano awo.
19 我是耶和华—你们的 神,你们要顺从我的律例,谨守遵行我的典章,
Ine ndine Yehova Mulungu wanu; tsatirani malangizo anga ndipo sungani malamulo anga.
20 且以我的安息日为圣。这日在我与你们中间为证据,使你们知道我是耶和华—你们的 神。
Masabata anga muziwasunga ngati opatulika kuti akhale chizindikiro pakati pa Ine ndi inu. Mukatero mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova Mulungu wanu.’
21 只是他们的儿女悖逆我,不顺从我的律例,也不谨守遵行我的典章(人若遵行就必因此活着),干犯我的安息日。 “我就说,要将我的忿怒倾在他们身上,在旷野向他们成就我怒中所定的。
“‘Koma ana awo anandiwukira. Iwo sanatsatire malangizo anga, sanamvere malamulo anga, ngakhale kuti amapereka moyo kwa munthu amene amawamvera. Ndiponso anayipitsa Masabata anga. Choncho ndinaganiza zowakhuthulira ukali wanga ndi kuwawonongeratu mʼchipululu momwemo.
22 虽然如此,我却为我名的缘故缩手没有这样行,免得我的名在我领他们出埃及的列国人眼前被亵渎。
Koma sindinatero chifukwa cha dzina langa kuti lisayipitsidwe pakati pa anthu a mitundu ina amene anandiona ndikutulutsa Aisraeliwo mu Iguptomo.
23 并且我在旷野向他们起誓,必将他们分散在列国,四散在列邦;
Choncho ndinalumbira mʼchipululu, nditakweza dzanja langa, kuti ndidzawabalalitsa pakati pa anthu a mitundu ina ndi kuwamwazira ku mayiko akutali,
24 因为他们不遵行我的典章,竟厌弃我的律例,干犯我的安息日,眼目仰望他们父亲的偶像。
chifukwa sanamvere malamulo anga, anakana malangizo anga, nayipitsa masabata anga, ndi kupembedza mafano a makolo awo.
25 我也任他们遵行不美的律例,谨守不能使人活着的恶规。
Ine ndinawapatsanso malangizo amene sanali abwino ndi malamulo amene sakanatha kupeza nawo moyo.
26 因他们将一切头生的经火,我就任凭他们在这供献的事上玷污自己,好叫他们凄凉,使他们知道我是耶和华。
Ndinawalekerera kuti adziyipitse ndi mphatso zawo zomwe, makamaka popereka ana awo oyamba kubadwa ngati nsembe zopsereza. Ndinatero kuti ndiwadetse nkhawa ndi kuti adziwe kuti Ine ndine Yehova.’
27 “人子啊,你要告诉以色列家说,主耶和华如此说:你们的列祖在得罪我的事上亵渎我;
“Tsono iwe mwana wa munthu, yankhula nawo Aisraeli ndipo uwawuze kuti, ‘Ambuye Yehova akuti makolo anu anandinyozanso posaonetsa moyo wokhulupirika.
28 因为我领他们到了我起誓应许赐给他们的地,他们看见各高山、各茂密树,就在那里献祭,奉上惹我发怒的供物,也在那里焚烧馨香的祭牲,并浇上奠祭。
Nditawalowetsa mʼdziko limene ndinachita kulumbirira kuti ndidzawapatsa, iwo tsono ankapita kulikonse kumene anaona chitunda chachitali ndi mtengo wa masamba ambiri kukapereka kumeneko nsembe ndi zopereka zawo zimene zinkandikwiyitsa. Kumeneko ankapereka nsembe za fungo lokoma ndiponso nsembe za zakumwa.
29 我就对他们说:你们所上的那高处叫什么呢?(那高处的名字叫巴麻直到今日。)
Tsono ndinawafunsa kuti: Kodi chitunda chimene mukupitako nʼchotani? Chitundachi chakhala chikutchedwa mpaka lero kuti ‘Chitunda cha Chipembedzo.’
30 所以你要对以色列家说,主耶和华如此说:你们仍照你们列祖所行的玷污自己吗?仍照他们可憎的事行邪淫吗?
“Tsono uwawuze Aisraeli kuti, ‘Ine Ambuye Yehova ndikuti: Kodi mudzadziyipitsa nokha monga anachitira makolo anu ndi kuchita chigololo ndi milungu yawo yonyansa?
31 你们奉上供物使你们儿子经火的时候,仍将一切偶像玷污自己,直到今日吗?以色列家啊,我岂被你们求问吗?主耶和华说:我指着我的永生起誓,我必不被你们求问。
Pamene mubwera kudzapereka mphatso zanu ndi kudzapereka ana kuti akhale ngati nsembe zopsereza mumadziyipitsa ndi mafano anu mpaka lero. Kodi Aisraeli, ndingathe kukulolani bwanji kuti mulandire malangizo kwa Ine? Ndithu pali Ine wamoyo, akutero Ambuye Yehova, sindidzalola kuti mupemphe nzeru kwa Ine.
32 “你们说:我们要像外邦人和列国的宗族一样,去事奉木头与石头。你们所起的这心意万不能成就。”
“‘Inu munanena kuti, ‘Tikufuna tikhale ngati anthu a mitundu ina, ngati anthu adziko lapansi, amene amapembedza mtengo ndi mwala.’ Koma zimene mukuganizazo sizidzachitika.
33 主耶和华说:“我指着我的永生起誓,我总要作王,用大能的手和伸出来的膀臂,并倾出来的忿怒,治理你们。
Ndithu pali Ine wamoyo, akutero Ambuye Yehova, ndi dzanja langa lamphamvu, nditasamula mkono wanga mokwiya kwambiri, Ine ndidzakhala wokulamulani.
34 我必用大能的手和伸出来的膀臂,并倾出来的忿怒,将你们从万民中领出来,从分散的列国内聚集你们。
Ndidzakuchotsani pakati pa anthu a mitundu ina ndikukusonkhanitsani kuchokera ku mayiko kumene munamwazikirako, ndi dzanja langa lamphamvu ndi lotambasuka ndili wokwiya kwambiri.
35 我必带你们到外邦人的旷野,在那里当面刑罚你们。
Ndidzakulowetsani mʼchipululu cha anthu a mitundu ina ndipo kumeneko, moonana maso ndi maso, ndidzakuzengani mlandu.
36 我怎样在埃及地的旷野刑罚你们的列祖,也必照样刑罚你们。这是主耶和华说的。
Monga ndinawalangira makolo anu mʼchipululu cha dziko la Igupto, motero ndidzakulangani, akutero Ambuye Yehova.
37 我必使你们从杖下经过,使你们被约拘束。
Ndidzakuwerengani ndi ndodo ya mʼbusa, kukulowetsani mʼchimango cha pangano langa.
38 我必从你们中间除净叛逆和得罪我的人,将他们从所寄居的地方领出来,他们却不得入以色列地。你们就知道我是耶和华。
Ndidzakuchotserani anthu amene anandigalukira ndi kundiwukira. Ngakhale ndidzawatulutsa mʼdziko limene akukhalamo, koma sadzalowamo mʼdziko la Israeli. Pamenepo mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova.
39 “以色列家啊,至于你们,主耶和华如此说:从此以后若不听从我,就任凭你们去事奉偶像,只是不可再因你们的供物和偶像亵渎我的圣名。
“‘Koma inu Aisraeli, zimene ndikunena Ine Ambuye Yehova ndi izi: Pitani katumikireni mafano anu onse, aliyense wa inu! Koma mʼtsogolo mwake mudzandimvera ndithu ndipo simudzayipitsa dzina langa lopatulika popereka mphatso zanu kwa mafano.
40 “主耶和华说:在我的圣山,就是以色列高处的山,所有以色列的全家都要事奉我。我要在那里悦纳你们,向你们要供物和初熟的土产,并一切的圣物。
Pakuti pa phiri langa lopatulika, phiri lalitali la ku Israeli, akutero Ambuye Yehova, Aisraeli onse adzanditumikira, ndipo kumeneko Ine ndidzawalandira. Kumeneko ndidzayembekeza zopereka zanu ndi mphatso zanu zopambana, pamodzi ndi nsembe zanu zonse zopatulika.
41 我从万民中领你们出来,从分散的列国内聚集你们,那时我必悦纳你们好像馨香之祭,要在外邦人眼前在你们身上显为圣。
Ndidzakulandirani ngati nsembe ya fungo lokoma ndikadzakutulutsani pakati pa anthu a mitundu ina ndi kukusokhanitsani kuchokera ku mayiko kumene munabalalitsidwirako. Motero ndidzadzionetsa pakati panu kuti ndine woyera ndipo mitundu ya anthu idzaona.
42 我领你们进入以色列地,就是我起誓应许赐给你们列祖之地,那时你们就知道我是耶和华。
Tsono mudzadziwa kuti ndine Yehova ndikadzabwera nanu ku dziko la Israeli, dziko limene ndinalumbira kuti ndidzapereka kwa makolo anu.
43 你们在那里要追念玷污自己的行动作为,又要因所做的一切恶事厌恶自己。
Kumeneko mudzakumbukira makhalidwe anu ndi machitidwe anu onse amene munadziyipitsa nawo, ndipo mudzanyansidwa nokha chifukwa cha zoyipa zimene munachita.
44 主耶和华说:以色列家啊,我为我名的缘故,不照着你们的恶行和你们的坏事待你们;你们就知道我是耶和华。”
Inu mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova, ndikadzakuchitirani zabwino chifukwa cha dzina langa koma osati molingana ndi njira zanu zoyipa ndi machitidwe anu okhota, inu Aisraeli, akutero Ambuye Yehova.’”
45 耶和华的话临到我说:
Yehova anandiyankhula nati:
46 “人子啊,你要面向南方,向南滴下预言攻击南方田野的树林。
“Iwe mwana wa munthu, tembenuka uyangʼane kummwera; ndipo lalika mawu odzudzula anthu akummwera ndipo unenere zodzudzula dziko la nkhalango ya kummwera.
47 对南方的树林说,要听耶和华的话。主耶和华如此说:我必使火在你中间着起,烧灭你中间的一切青树和枯树,猛烈的火焰必不熄灭。从南到北,人的脸面都被烧焦。
Iwuze nkhalango yakummwera kuti, ‘Imvani mawu a Yehova! Ambuye Yehova akuti: Ndikuyatsa moto ndipo motowo udzapsereza mitengo yako yonse yayiwisi ndi yowuma yomwe. Malawi ake sadzazimitsika ndipo aliyense kuchokera kummwera mpaka kumpoto adzapsa nawo.
48 凡有血气的都必知道是我—耶和华使火着起,这火必不熄灭。”
Aliyense adzadziwa kuti Ine Yehova ndi amene ndayatsa motowo, ndipo sudzazimitsidwa.’”
49 于是我说:“哎!主耶和华啊,人都指着我说:他岂不是说比喻的吗?”
Ndipo ine ndinati, “Aa, Ambuye Yehova! Anthu akungondinena kuti, ‘Kodi suja amangonena nthano chabe ameneyu!’”

< 以西结书 20 >