< 出埃及记 26 >
1 “你要用十幅幔子做帐幕。这些幔子要用捻的细麻和蓝色、紫色、朱红色线制造,并用巧匠的手工绣上基路伯。
“Panga chihema pogwiritsa ntchito nsalu khumi zofewa, zosalala ndi zolukidwa bwino, zobiriwira, zapepo ndi zofiira. Ndipo anthu aluso apete pa nsaluzo Akerubi.
2 每幅幔子要长二十八肘,宽四肘,幔子都要一样的尺寸。
Nsalu zonse zikhale zofanana. Mulitali mwake zikhale mamita khumi ndi atatu, mulifupi mamita awiri.
3 这五幅幔子要幅幅相连;那五幅幔子也要幅幅相连。
Ulumikize nsalu zisanu kuti ikhale nsalu imodzi. Uchite chimodzimodzi ndi nsalu zisanu zinazo.
4 在这相连的幔子末幅边上要做蓝色的钮扣;在那相连的幔子末幅边上也要照样做。
Panga zokolowekamo za nsalu yobiriwira mʼmphepete mwa nsalu imodzi yotsiriza ya mbali ina. Uchitenso chimodzimodzi ndi nsalu yotsiriza ya mbali inayo.
5 要在这相连的幔子上做五十个钮扣;在那相连的幔子上也做五十个钮扣,都要两两相对。
Upange zokolowekamo 50 pa nsalu yoyamba ndi zokolowekamo makumi asanu zinanso pa nsalu inayo. Upange motero kuti zokolowekamozo ziziyangʼanana.
6 又要做五十个金钩,用钩使幔子相连,这才成了一个帐幕。
Kenaka upange ngowe zagolide makumi asanu zolumikizira nsalu ziwirizo kuti zipange chihema chimodzi.
7 “你要用山羊毛织十一幅幔子,作为帐幕以上的罩棚。
“Upange nsalu za ubweya wambuzi zophimba pamwamba pa chihemacho. Nsalu zonse pamodzi zikhale khumi ndi imodzi.
8 每幅幔子要长三十肘,宽四肘;十一幅幔子都要一样的尺寸。
Nsalu zonse khumi ndi imodzi zikhale zofanana. Mulitali mwake mukhale mamita khumi ndi anayi ndipo mulifupi mwake mukhale mamita awiri.
9 要把五幅幔子连成一幅,又把六幅幔子连成一幅,这第六幅幔子要在罩棚的前面折上去。
Ulumikize nsalu zisanu kuti ikhale nsalu imodzi ndipo zina zisanu ndi imodzi uzilumikizenso kuti ikhale nsalu imodzinso. Nsalu yachisanu ndi chimodzi imene ili kutsogolo kwa tenti uyipinde pawiri.
10 在这相连的幔子末幅边上要做五十个钮扣;在那相连的幔子末幅边上也做五十个钮扣。
Upange zokolowekamo 50 mʼmphepete mwa nsalu imodzi yotsirizira ya nsalu yoyamba yolumikiza ija. Upangenso zokolowekamo zina 50 mʼmphepete mwa nsalu yotsirizira ya nsalu inanso yolumikiza ija.
11 又要做五十个铜钩,钩在钮扣中,使罩棚连成一个。
Kenaka upange ngowe 50 zamkuwa ndipo uzilowetse mu zokolowekazo. Ndiye uphatikize nsalu ziwirizo kuti tentiyo ikhale imodzi.
12 罩棚的幔子所余那垂下来的半幅幔子,要垂在帐幕的后头。
Theka lotsalira la nsaluyo lidzalendewera kumbuyo kwa chihemacho.
13 罩棚的幔子所余长的,这边一肘,那边一肘,要垂在帐幕的两旁,遮盖帐幕。
Nsalu yotsalira ya masentimita 46 mulitali mwake mʼmbali zonse ziwiri idzalendewere kuphimba mbali ziwirizo.
14 又要用染红的公羊皮做罩棚的盖;再用海狗皮做一层罩棚上的顶盖。
Upange chikopa cha nkhosa zazimuna cha utoto wofiira chophimbira tentiyo ndipo pamwamba pake upangireponso chophimbira china cha zikopa za akatumbu.
“Upange maferemu amatabwa amtengo wa mkesha oyimikira chihemacho.
Feremu iliyonse ikhale yotalika mamita anayi ndipo mulifupi mwake mukhale masentimita 69.
Thabwa lililonse likhale ndi zolumikizira ziwiri. Upange maferemu onse a chihemacho ndi matabwa otere.
Upange maferemu makumi awiri a mbali yakummwera kwa chihemacho.
19 在这二十块板底下要做四十个带卯的银座,两卯接这块板上的两榫,两卯接那块板上的两榫。
Ndipo upange matsinde 40 asiliva ndipo uwayike pansi pa maferemuwo. Pansi pa feremu iliyonse pakhale matsinde awiri ogwiriziza zolumikizira ziwiri zija.
Ndipo mbali yakumpoto ya chihemacho upangenso maferemu makumi awiri.
21 和带卯的银座四十个;这板底下有两卯,那板底下也有两卯。
Upangenso matsinde 40 asiliva, awiri pansi pa feremu iliyonse.
Upange maferemu asanu ndi imodzi a kumbuyo kwa tenti, kumbali yakumadzulo.
Ndipo upangenso maferemu awiri a pa ngodya yakumbuyo kwenikweni kwa tenti.
24 板的下半截要双的,上半截要整的,直顶到第一个环子;两块都要这样做两个拐角。
Pa ngodya ziwirizi pakhale maferemu awiri, kuyambira pansi mpaka pamwamba ndipo alumikizidwe pa ngowe imodzi. Maferemu onse akhale ofanana.
25 必有八块板和十六个带卯的银座;这板底下有两卯,那板底下也有两卯。
Choncho pakhale maferemu asanu ndi atatu ndiponso matsinde 16 asiliva, awiri akhale pansi pa feremu iliyonse.
“Upange mitanda ya matabwa amtengo wa mkesha: mitanda isanu ikhale ya maferemu a mbali imodzi ya chihema,
27 为帐幕那面的板做五闩,又为帐幕后面的板做五闩。
mitanda isanu inanso ikhale ya maferemu a mbali inayo. Pakhalenso mitanda ina isanu ya mbali yakumadzulo, kumapeto kwenikweni kwa chihema.
Mtanda wapakati pa maferemuwo uchokere pa maferemu a mbali ina mpaka mbali inanso.
29 板要用金子包裹,又要做板上的金环套闩;闩也要用金子包裹。
Maferemuwo uwakute ndi golide ndiponso upange mphete zagolide zogwiriziza mitandayo. Ndipo mitandayonso uyikute ndi golide.
“Upange chihema mofanana ndi momwe ndinakuonetsera pa phiri paja.
31 “你要用蓝色、紫色、朱红色线,和捻的细麻织幔子,以巧匠的手工绣上基路伯。
“Upange nsalu yokhala ndi mtundu wamtambo, wapepo ndi ofiira ndipo nsaluyo ikhale yolukidwa bwino, yofewa ndi yosalala. Ndipo anthu aluso apetepo zithunzi za Akerubi.
32 要把幔子挂在四根包金的皂荚木柱子上,柱子上当有金钩,柱子安在四个带卯的银座上。
Nsaluyo uyikoloweke pa nsanamira zinayi zamtengo wa mkesha zokutidwa ndi golide zomwe zili ndi ngowe zagolide, zomwe zayima pa matsinde asiliva anayi.
33 要使幔子垂在钩子下,把法柜抬进幔子内;这幔子要将圣所和至圣所隔开。
Ukoloweke kataniyo ku ngowe ndipo uyike Bokosi la Chipangano mʼkatimo. Kataniyo idzalekanitse malo wopatulika ndi malo wopatulika kwambiri.
Uyike chivundikiro pa bokosi laumboni ku malo wopatulika kwambiri.
35 把桌子安在幔子外帐幕的北面;把灯台安在帐幕的南面,彼此相对。
Uyike tebulo kunja kwa katani yotchinga cha kumpoto kwa chihema ndipo uyike choyikapo nyale chija kummwera moyangʼanana ndi tebulolo.
36 “你要拿蓝色、紫色、朱红色线,和捻的细麻,用绣花的手工织帐幕的门帘。
“Pa chipata cholowera mu chihema, uyikepo nsalu yamtundu wamtambo, wapepo ndi ofiira, yomwe ndi yofewa ndi yosalala, yopetedwa bwino ndi amisiri aluso.
37 要用皂荚木为帘子做五根柱子,用金子包裹。柱子上当有金钩;又要为柱子用铜铸造五个带卯的座。”
Upange ngowe zagolide za nsaluyo ndi nsanamira zisanu zamtengo wa mkesha ndipo uzikute ndi golide. Upangenso matsinde asanu amkuwa a nsanamirazo.”