< 传道书 1 >

1 在耶路撒冷作王、大卫的儿子、传道者的言语。
Mawu a Mlaliki, mwana wa Davide, mfumu ya ku Yerusalemu:
2 传道者说:虚空的虚空, 虚空的虚空,凡事都是虚空。
“Zopandapake! Zopandapake!” atero Mlaliki. “Zopandapake kotheratu! Zopandapake.”
3 人一切的劳碌, 就是他在日光之下的劳碌,有什么益处呢?
Kodi munthu amapindulanji pa ntchito zake zonse zimene amasautsidwa nazo pansi pano?
4 一代过去,一代又来, 地却永远长存。
Mibado imabwera ndipo mibado imapita, koma dziko lapansi limakhalapobe nthawi zonse.
5 日头出来,日头落下, 急归所出之地。
Dzuwa limatuluka ndipo dzuwa limalowa ndipo limapita mwamsanga kumene limatulukira.
6 风往南刮,又向北转, 不住地旋转,而且返回转行原道。
Mphepo imawombera cha kummwera ndi kukhotera cha kumpoto; imawomba mozungulirazungulira, kumangobwererabwerera komwe yachokera.
7 江河都往海里流,海却不满; 江河从何处流,仍归还何处。
Mitsinje yonse imakathira ku nyanja, koma nyanjayo sidzaza; kumene madziwo amachokera, amabwereranso komweko.
8 万事令人厌烦, 人不能说尽。 眼看,看不饱; 耳听,听不足。
Zinthu zonse ndi zotopetsa, kutopetsa kwake ndi kosaneneka. Maso satopa ndi kuona kapena khutu kukwaniritsidwa ndi kumva.
9 已有的事后必再有; 已行的事后必再行。 日光之下并无新事。
Zomwe zinalipo kale zidzakhalaponso, zomwe zinachitika kale zidzachitikanso. Ndiye kuti chatsopano palibiretu pansi pano.
10 岂有一件事人能指着说这是新的? 哪知,在我们以前的世代早已有了。
Kodi chilipo chinthu chimene wina anganene kuti, “Taona! Ichi ndiye chatsopano?” Chinalipo kale, kalekale; chinalipo ife kulibe.
11 已过的世代,无人记念; 将来的世代,后来的人也不记念。
Anthu akale sakumbukiridwa, ngakhale amene adzabwera mʼtsogolomu sadzakumbukiridwa ndi iwo amene adzabwere pambuyo pawo.
12 我传道者在耶路撒冷作过以色列的王。
Ine, Mlalikine, ndinali mfumu ya Israeli mu Yerusalemu.
13 我专心用智慧寻求、查究天下所做的一切事,乃知 神叫世人所经练的是极重的劳苦。
Ndinayika mtima wanga pophunzira ndi kufunafuna mwa nzeru zinthu zonse zimene zimachitika pansi pa thambo. Ndi ntchito yolemetsa ndithu imene Mulungu anayipereka kwa anthu!
14 我见日光之下所做的一切事,都是虚空,都是捕风。
Ine ndaona zinthu zonse zochitika pansi pano; zinthu zonsezo ndi zopandapake, nʼkungodzivuta chabe.
15 弯曲的,不能变直; 缺少的,不能足数。
Chinthu chokhota sichingathe kuwongoledwa; chimene palibe sichingathe kuwerengedwa.
16 我心里议论说:我得了大智慧,胜过我以前在耶路撒冷的众人,而且我心中多经历智慧和知识的事。
Ine ndinaganiza mu mtima mwanga, “Taona, ine ndakula ndi kukhala wa nzeru zochuluka kupambana aliyense amene analamulirapo Yerusalemu ndisanabadwe; ndaphunzira nzeru zochuluka ndi luntha.”
17 我又专心察明智慧、狂妄,和愚昧,乃知这也是捕风。
Ndipo ndinadzipereka kuti ndithe kumvetsa kuti nzeru nʼchiyani, misala nʼchiyani, uchitsiru nʼchiyani, koma ndinazindikira ichi, kuti kuteronso nʼkungodzivuta chabe.
18 因为多有智慧,就多有愁烦; 加增知识的,就加增忧伤。
Pakuti nzeru zochuluka zimabweretsa chisoni chochulukanso: chidziwitso chochuluka, zowawa zochulukanso.

< 传道书 1 >