< 但以理书 9 >
1 米底亚族亚哈随鲁的儿子大流士立为迦勒底国的王元年,
Mʼchaka choyamba cha Dariyo mwana wa Ahasiwero (wochokera kwa Amedi), amene anakhala mfumu ya ku Babuloni,
2 就是他在位第一年,我—但以理从书上得知耶和华的话临到先知耶利米,论耶路撒冷荒凉的年数,七十年为满。
ine Danieli ndinazindikira powerenga mawu a Yehova opatsidwa kwa mneneri Yeremiya, kuti Yerusalemu adzakhala bwinja kwa zaka 70.
Choncho ndinatembenukira kwa Ambuye Mulungu ndipo ndinamudandaulira ndi kupempha posala kudya, ndi kuvala chiguduli ndi kudzola phulusa.
4 我向耶和华—我的 神祈祷、认罪,说:“主啊,大而可畏的 神,向爱主、守主诫命的人守约施慈爱。
Ndinapemphera kwa Yehova Mulungu wanga ndi kuvomereza kuti tinachimwa: Ndinati, “Inu Ambuye, Mulungu wamkulu ndi woopsa, amene mumasunga pangano lanu la chikondi kwa onse amene amakukondani ndi kumvera malamulo anu,
tachimwa ndipo tachita zolakwa ndi zoyipa. Takuwukirani posiya malangizo ndi malamulo anu.
6 没有听从你仆人众先知奉你名向我们君王、首领、列祖,和国中一切百姓所说的话。
Sitinamvere aneneri atumiki anu, amene anayankhula mʼdzina lanu kwa mafumu athu, kwa akalonga athu, makolo athu, ndi kwa anthu onse a mʼdziko.
7 主啊,你是公义的,我们是脸上蒙羞的;因我们犹大人和耶路撒冷的居民,并以色列众人,或在近处,或在远处,被你赶到各国的人,都得罪了你,正如今日一样。
“Ambuye ndinu olungama, koma lero tili ndi manyazi, ife anthu a ku Yuda, a ku Yerusalemu ndi Israeli yense, apafupi ndi akutali omwe, ku mayiko onse kumene munatipirikitsira chifukwa cha kusakhulupirika kwathu.
8 主啊,我们和我们的君王、首领、列祖因得罪了你,就都脸上蒙羞。
Inu Yehova, ife ndi mafumu athu, akalonga athu ndi makolo athu tili ndi manyazi chifukwa takuchimwirani.
9 主—我们的 神是怜悯饶恕人的,我们却违背了他,
Ambuye Mulungu wathu ndi wachifundo ndi wokhululuka, ngakhale kuti tamuwukira:
10 也没有听从耶和华—我们 神的话,没有遵行他借仆人众先知向我们所陈明的律法。
Ife sitinamvere Yehova Mulungu wathu kapena kusunga malamulo ake amene anatipatsa kudzera mwa aneneri atumiki ake.
11 以色列众人都犯了你的律法,偏行,不听从你的话;因此,在你仆人摩西律法上所写的咒诅和誓言都倾在我们身上,因我们得罪了 神。
Aisraeli onse anachimwira lamulo lanu motero anapatuka, nakana kukumverani. “Choncho matemberero ndi olumbira amene alembedwa mʼmalamulo a Mose, mtumiki wa Mulungu, atigwera chifukwa takuchimwirani.
12 他使大灾祸临到我们,成就了警戒我们和审判我们官长的话;原来在普天之下未曾行过像在耶路撒冷所行的。
Inu mwakwaniritsa mawu amene munayankhula otitsutsa ife ndi otsutsa otilamulira potibweretsera tsoka lalikulu. Pa dziko lapansi sipanachitikenso zinthu ngati zimene zaonekera Yerusalemu.
13 这一切灾祸临到我们身上是照摩西律法上所写的,我们却没有求耶和华—我们 神的恩典,使我们回头离开罪孽,明白你的真理。
Monga kunalembedwa mʼMalamulo a Mose, tsoka lililonse latifikira chikhalirecho sitinapemphe Yehova Mulungu wathu kuti atikomere mtima. Sitinasiye machimo athu, ndipo sitinasamale choonadi chanu.
14 所以耶和华留意使这灾祸临到我们身上,因为耶和华—我们的 神在他所行的事上都是公义;我们并没有听从他的话。
Choncho Yehova anakonza kuti atigwetsere tsoka limeneli, ndipo wachitadi popeza Yehova Mulungu wathu ndi wolungama mu chilichonse amachita; chikhalirecho ife sitinamumvere.
15 主—我们的 神啊,你曾用大能的手领你的子民出埃及地,使自己得了名,正如今日一样。我们犯了罪,作了恶。
“Inu Ambuye Mulungu wathu, munatulutsa anthu anu ku Igupto ndi dzanja lanu lamphamvu ndipo dzina lanu ndi lotchuka mpaka lero. Ife tachimwa, tachita zolakwa.
16 主啊,求你按你的大仁大义,使你的怒气和忿怒转离你的城耶路撒冷,就是你的圣山。耶路撒冷和你的子民,因我们的罪恶和我们列祖的罪孽被四围的人羞辱。
Inu Ambuye, molingana ndi zochita zanu zolungama, tikukupemphani kuti muchotse mkwiyo ndi ukali wanu pa Yerusalemu mzinda wanu, phiri lanu loyera. Machimo athu ndi mphulupulu za makolo athu zachititsa kuti onse otizungulira atonze Yerusalemu ndi anthu anu.
17 我们的 神啊,现在求你垂听仆人的祈祷恳求,为自己使脸光照你荒凉的圣所。
“Tsopano Mulungu wathu, imvani mapemphero ndi zopempha za mtumiki wanu. Kuti anthu onse akudziweni kuti ndinu Ambuye, komerani mtima malo anu opatulika amene asanduka bwinja.
18 我的 神啊,求你侧耳而听,睁眼而看,眷顾我们荒凉之地和称为你名下的城。我们在你面前恳求,原不是因自己的义,乃因你的大怜悯。
Tcherani khutu, Inu Mulungu, ndipo imvani; tsekulani maso anu ndipo onani mabwinja athu ndi mzinda umene umadziwika ndi dzina lanu. Sitikupempha chifukwa chakuti ndife olungama, koma chifukwa cha kukula kwa chifundo chanu.
19 求主垂听,求主赦免,求主应允而行,为你自己不要迟延。我的 神啊,因这城和这民都是称为你名下的。”
Inu Ambuye imvani mawu athu! Ambuye khululukani! Ambuye timvereni, ndipo muchitepo kanthu! Kuti anthu adziwe kuti Inu ndinu Mulungu wanga musachedwe chifukwa mzinda wanu ndi anthu anu amadziwika ndi dzina lanu.”
20 我说话,祷告,承认我的罪和本国之民以色列的罪,为我 神的圣山,在耶和华—我 神面前恳求。
Ndikuyankhula ndi kupemphera, kuvomereza machimo anga ndi machimo a anthu anga Aisraeli ndi kupempherera phiri lake loyera kwa Yehova Mulungu wanga,
21 我正祷告的时候,先前在异象中所见的那位加百列,奉命迅速飞来,约在献晚祭的时候,按手在我身上。
Gabrieli, munthu uja amene ndinamuona mʼmasomphenya poyambirira, anabwera kwa ine mowuluka. Iyi inali nthawi ya nsembe ya madzulo.
22 他指教我说:“但以理啊,现在我出来要使你有智慧,有聪明。
Anandilangiza kuti, “Danieli ndabwera tsopano kuti ndikupatse nzeru kuti uzitha kumvetsa zinthu.
23 你初恳求的时候,就发出命令,我来告诉你,因你大蒙眷爱;所以你要思想明白这以下的事和异象。
Utangoyamba kupemphera, Mulungu anayankha. Tsono ine ndabwera kudzakuwuza yankholo, popeza ndiwe wokondedwa kwambiri. Choncho mvetsetsa pamene ndikufotokoza za zinthu zimene unaziona mʼmasomphenya.
24 “为你本国之民和你圣城,已经定了七十个七。要止住罪过,除净罪恶,赎尽罪孽,引进永义,封住异象和预言,并膏至圣者。
“Zaka 490 zinayikidwa kuti anthu a mtundu wako ndi mzinda wanu woyera aleke zoyipa, asiye tchimo. Iwo adzapereka dipo kupepesera zolakwa zawo. Zikadzatero anthu adzaonetsa moyo wachilungamo nthawi zonse. Izi zidzatsimikiza zimene unaziona mʼmasomphenya zija ndi zimene ananenera aneneri. Malo opatulika adzakhazikitsidwa.
25 你当知道,当明白,从出令重新建造耶路撒冷,直到有受膏君的时候,必有七个七和六十二个七。正在艰难的时候,耶路撒冷城连街带濠都必重新建造。
“Tsono udziwe ndipo uzindikire izi kuti kuyambira pamene lamulo linaperekedwa kuti Yerusalemu akonzedwenso mpaka pamene mfumu Yodzozedwa idzafike padzapita zaka 49. Pa zaka 434 mzinda wa Yerusalemu udzamangidwanso, ndipo mabwalo ndi ngalande zake zidzatetezedwa. Koma nthawiyi idzakhala ya masautso.
26 过了六十二个七,那受膏者必被剪除,一无所有;必有一王的民来毁灭这城和圣所,至终必如洪水冲没。必有争战,一直到底,荒凉的事已经定了。
Patatha zaka 434, Wodzozedwayo adzaphedwa ndipo sadzakhala ndi aliyense. Anthu a wolamulira amene adzabwere adzawononga mzinda ndi Nyumba ya Mulungu. Kutha kwake kudzafika ngati chigumula. Komabe nkhondo idzapitirira mpaka chiwonongeko chimene Mulungu ananeneratu chitachitika.
27 一七之内,他必与许多人坚定盟约;一七之半,他必使祭祀与供献止息。那行毁坏可憎的如飞而来,并且有忿怒倾在那行毁坏的身上,直到所定的结局。”
Adzachita pangano lolimba ndi anthu ambiri kwa zaka zisanu ndi ziwiri. Koma pakatinʼpakati pa sabata limodzilo iye adzaletsa kupereka nsembe ndi chopereka. Chonyansa chosakaza chija adzachiyika mʼNyumba ya Mulungu, ndipo chidzakhalapobe mpaka wochita zimenezi atalangidwa ndi chiwonongeko chimene Mulungu ananeneratu.”