< 使徒行传 4 >

1 使徒对百姓说话的时候,祭司们和守殿官,并撒都该人忽然来了。
Pamene Petro ndi Yohane amayankhula ndi anthu, kunabwera ansembe, mkulu woyangʼanira Nyumba ya Mulungu ndiponso Asaduki.
2 因他们教训百姓,本着耶稣,传说死人复活,就很烦恼,
Iwo anakhumudwa kwambiri chifukwa atumwiwo amaphunzitsa anthu ndi kumalalikira za kuuka kwa akufa mwa Yesu.
3 于是下手拿住他们;因为天已经晚了,就把他们押到第二天。
Iwo anagwira Petro ndi Yohane, popeza kunali kutada, anawayika mʼndende mpaka mmawa mwake.
4 但听道之人有许多信的,男丁数目约到五千。
Koma anthu ambiri amene anamva uthenga anakhulupirira, ndipo chiwerengero cha anthu chinakwana 5,000.
5 第二天,官府、长老,和文士在耶路撒冷聚会,
Mmawa mwake olamulira, akulu ndi aphunzitsi a malamulo anasonkhana mu Yerusalemu.
6 又有大祭司亚那和该亚法、约翰、亚历山大,并大祭司的亲族都在那里,
Panali Anasi, Mkulu wa ansembe, Kayafa, Yohane ndi Alekisandro ndi ana a banja la mkulu wa ansembe.
7 叫使徒站在当中,就问他们说:“你们用什么能力,奉谁的名做这事呢?”
Iwo anayimiritsa Petro ndi Yohane patsogolo pawo nayamba kuwafunsa kuti, “Kodi munachita zimenezi ndi mphamvu yanji kapena mʼdzina la yani?”
8 那时彼得被圣灵充满,对他们说:
Petro wodzazidwa ndi Mzimu Woyera, anawawuza kuti, “Inu olamulira ndi akulu!
9 “治民的官府和长老啊,倘若今日因为在残疾人身上所行的善事查问我们他是怎么得了痊愈,
Ngati ife tikufunsidwa lero chifukwa cha ntchito yabwino imene yachitika pa munthu wolumala miyendo ndi mmene iye anachiritsidwira,
10 你们众人和以色列百姓都当知道,站在你们面前的这人得痊愈是因你们所钉十字架、 神叫他从死里复活的拿撒勒人耶稣基督的名。
tsono dziwani izi inu ndi aliyense mu Israeli: munthuyu akuyima pamaso panu, wochiritsidwa kwathunthu, ndi chifukwa cha dzina la Yesu Khristu wa ku Nazareti amene munamupachika koma Mulungu anamuukitsa kwa akufa.
11 他是 你们匠人所弃的石头, 已成了房角的头块石头。
Iye ndi “‘Mwala umene amisiri omanga nyumba anawukana, umenewo wasanduka mwala wa pa ngodya!’
12 除他以外,别无拯救;因为在天下人间,没有赐下别的名,我们可以靠着得救。”
Chipulumutso sichipezeka mwa wina aliyense; pakuti palibe dzina lina pansi pa thambo limene lapatsidwa kwa anthu limene tiyenera kupulumutsidwa nalo.”
13 他们见彼得、约翰的胆量,又看出他们原是没有学问的小民,就希奇,认明他们是跟过耶稣的;
Ataona kulimba mtima kwa Petro ndi Yohane ndi kuzindikira kuti anali osaphunzira, anthu wamba, anadabwa kwambiri ndipo anazindikira kuti anthuwa anakhala pamodzi ndi Yesu.
14 又看见那治好了的人和他们一同站着,就无话可驳。
Koma popeza iwo amamuona munthu amene anachiritsidwa atayima pamodzi ndi iwo, palibe chimene akananena.
15 于是吩咐他们从公会出去,就彼此商议说:
Chifukwa chake anawalamula kuti atuluke mʼbwalo la milandu ndipo akulu abwalowo anayamba kukambirana.
16 “我们当怎样办这两个人呢?因为他们诚然行了一件明显的神迹,凡住耶路撒冷的人都知道,我们也不能说没有。
Iwo anafunsana kuti, “Kodi anthuwa tichite nawo chiyani? Pakuti aliyense okhala mu Yerusalemu akudziwa kuti achita chodabwitsachi, ndipo ife sitingathe kukana.
17 惟恐这事越发传扬在民间,我们必须恐吓他们,叫他们不再奉这名对人讲论。”
Koma kuti mbiriyi isapitirire kuwanda pakati pa anthu, ife tiwachenjeze anthu amenewa kuti asayankhulenso kwa wina aliyense mʼdzina la Yesu.”
18 于是叫了他们来,禁止他们总不可奉耶稣的名讲论教训人。
Pamenepo anawayitananso ndipo anawalamula kuti asayankhule kapena kuphunzitsa konse mʼdzina la Yesu.
19 彼得、约翰说:“听从你们,不听从 神,这在 神面前合理不合理,你们自己酌量吧!
Koma Petro ndi Yohane anayankha kuti, “Weruzani nokha ngati nʼkwabwino pamaso pa Mulungu kumvera inu koposa Mulungu.
20 我们所看见所听见的,不能不说。”
Ife sitingaleke kuyankhula za zimene tinaziona ndi kuzimva.”
21 官长为百姓的缘故,想不出法子刑罚他们,又恐吓一番,把他们释放了。这是因众人为所行的奇事都归荣耀与 神。
Atawonjeza kuwaopseza anawamasula. Sanathe kugwirizana njira yowalangira, chifukwa anthu onse amayamika Mulungu chifukwa cha zimene zinachitika.
22 原来借着神迹医好的那人有四十多岁了。
Ndipo munthu amene anachiritsidwayo anali ndi zaka makumi anayi.
23 二人既被释放,就到会友那里去,把祭司长和长老所说的话都告诉他们。
Atamasulidwa Petro ndi Yohane anapita kwa anzawo ndipo anawafotokozera zonse zimene akulu a ansembe ndi akulu anawawuza.
24 他们听见了,就同心合意地高声向 神说:“主啊!你是造天、地、海,和其中万物的,
Anthu atamva zimenezi anafuwula ndi mtima umodzi napemphera kwa Mulungu. Iwo anati, “Ambuye wolamulira zonse, Inu munalenga kumwamba ndi dziko lapansi ndi nyanja ndiponso zonse zili mʼmenemo.
25 你曾借着圣灵,托你仆人—我们祖宗大卫的口,说: 外邦为什么争闹? 万民为什么谋算虚妄的事?
Inu munayankhula mwa Mzimu Woyera kudzera pakamwa pa Davide kholo lathu, mtumiki wanu kuti, “‘Nʼchifukwa chiyani anthu a mitundu ina akufuna kuchita chiwembu, ndipo akonzekera kuchita zopandapake?
26 世上的君王一齐起来, 臣宰也聚集, 要敌挡主, 并主的受膏者。
Mafumu a dziko lapansi akugwirizana nazo; ndipo olamulira asonkhana pamodzi kulimbana ndi Ambuye ndi wodzozedwa wakeyo.’
27 希律和本丢·彼拉多,外邦人和以色列民,果然在这城里聚集,要攻打你所膏的圣仆耶稣,
Zoonadi, Herode ndi Pontiyo Pilato anasonkhana pamodzi ndi amitundu ndiponso Aisraeli, mu mzinda muno, kupanga zolimbana ndi mtumiki wanu woyera Yesu, amene Inu munamudzoza.
28 成就你手和你意旨所预定必有的事。
Iwo anachita zimene munakonzeratu mwachifuniro chanu ndi mphamvu yanu kuti zichitike.
29 他们恐吓我们,现在求主鉴察,一面叫你仆人大放胆量讲你的道,一面伸出你的手来医治疾病,并且使神迹奇事因着你圣仆耶稣的名行出来。”
Tsopano, Ambuye taonani kuti atiopseza, tithandizeni ife atumiki anu, kuti tiyankhule mawu anu molimba mtima.
Tambasulani dzanja lanu kuchiritsa anthu ndipo kuti, zizindikiro zodabwitsa zichitike mʼdzina la mtumiki wanu woyera Yesu.”
31 祷告完了,聚会的地方震动,他们就都被圣灵充满,放胆讲论 神的道。
Iwo atatha kupemphera, malo amene anasonkhanapo anagwedezeka. Ndipo iwo onse anadzazidwa ndi Mzimu Woyera ndipo anayankhula Mawu a Mulungu molimba mtima.
32 那许多信的人都是一心一意的,没有一人说他的东西有一样是自己的,都是大家公用。
Okhulupirira onse anali a mtima umodzi, ndi maganizo amodzi. Palibe munthu amene amati zomwe anali nazo zinali zake zokha, koma amagawana chilichonse chimene anali nacho.
33 使徒大有能力,见证主耶稣复活;众人也都蒙大恩。
Atumwi anapitirira kuchitira umboni mwa mphamvu zakuuka kwa Ambuye Yesu, ndipo pa iwo panali chisomo chochuluka.
34 内中也没有一个缺乏的;因为人人将田产房屋都卖了,把所卖的价银拿来,
Panalibe anthu osowa kanthu pakati pawo. Pakuti amene anali ndi malo, kapena nyumba amagulitsa ndi kubweretsa ndalamazo
35 放在使徒脚前,照各人所需用的,分给各人。
ndi kuzipereka kwa atumwi, ndipo zimagawidwa kwa aliyense amene anali ndi chosowa.
36 有一个利未人,生在塞浦路斯,名叫约瑟,使徒称他为巴拿巴(巴拿巴翻出来就是劝慰子)。
Yosefe, wa fuko la Levi, wochokera ku Kupro amene atumwi anamutcha Barnaba, kutanthauza kuti mwana wachilimbikitso,
37 他有田地,也卖了,把价银拿来,放在使徒脚前。
anagulitsa munda wake ndipo anadzapereka ndalamazo kwa atumwi.

< 使徒行传 4 >