< 撒母耳记下 22 >

1 当耶和华救大卫脱离一切仇敌和扫罗之手的日子,他向耶和华念这诗,
Davide anayimbira Yehova nyimbo iyi pamene Yehovayo anamupulumutsa mʼdzanja la adani ake onse ndiponso mʼdzanja la Sauli.
2 说: 耶和华是我的岩石, 我的山寨,我的救主,
Iye anati, “Yehova ndiye thanthwe langa, chitetezo changa ndi mpulumutsi wanga.
3 我的 神,我的磐石,我所投靠的。 他是我的盾牌,是拯救我的角, 是我的高台,是我的避难所。 我的救主啊,你是救我脱离强暴的。
Mulungu wanga ndiye thanthwe langa, mʼmene ndimathawiramo, chishango changa ndi ndodo yachipulumutso changa. Iye ndi linga langa, pothawirapo panga ndi mpulumutsi wanga. Munandipulumutsa mʼmanja mwa anthu ankhanza.
4 我要求告当赞美的耶和华, 这样,我必从仇敌手中被救出来。
“Ndimayitana Yehova amene ndi woyenera matamando, ndipo ndapulumutsidwa kwa adani anga.
5 曾有死亡的波浪环绕我, 匪类的急流使我惊惧,
“Mafunde a imfa anandizinga; mitsinje yothamanga yachiwonongeko inandiopsa kwambiri.
6 阴间的绳索缠绕我, 死亡的网罗临到我。 (Sheol h7585)
Anandimanga ndi zingwe za ku manda; misampha ya imfa inalimbana nane. (Sheol h7585)
7 我在急难中求告耶和华, 向我的 神呼求。 他从殿中听了我的声音; 我的呼求入了他的耳中。
“Mʼmasautso anga ndinapemphera kwa Yehova; ndinapemphera kwa Mulungu wanga. Iye ali mʼnyumba yake, anamva mawu anga; kulira kwanga kunafika mʼmakutu ake.
8 那时因他发怒,地就摇撼战抖; 天的根基也震动摇撼。
“Dziko lapansi linanjenjemera ndi kuchita chivomerezi, maziko a miyamba anagwedezeka; ananjenjemera chifukwa Iye anakwiya.
9 从他鼻孔冒烟上腾; 从他口中发火焚烧,连炭也着了。
Mʼmphuno mwake munatuluka utsi; moto wonyeketsa unatuluka mʼkamwa mwake, makala amoto anali lawilawi mʼkamwa mwake.
10 他又使天下垂,亲自降临; 有黑云在他脚下。
Iye anangʼamba thambo natsika pansi; pansi pa mapazi ake panali mitambo yakuda.
11 他坐着基路伯飞行, 在风的翅膀上显现。
Iye anakwera pa Kerubi ndi kuwuluka; nawuluka ndi mphepo mwaliwiro.
12 他以黑暗和聚集的水、 天空的厚云为他四围的行宫。
Iye anapanga mdima kukhala chofunda chake, mitambo yakuda ya mlengalenga.
13 因他面前的光辉炭都着了。
Mʼkuwala kumene kunali pamaso pake munkachokera makala amoto alawilawi.
14 耶和华从天上打雷; 至高者发出声音。
Yehova anabangula kumwamba ngati bingu, mawu a Wammwambamwamba anamveka ponseponse.
15 他射出箭来,使仇敌四散, 发出闪电,使他们扰乱。
Iye anaponya mivi yake, nabalalitsa adani ake, ndi zingʼaningʼani zake anawagonjetsa.
16 耶和华的斥责一发,鼻孔的气一出, 海底就出现,大地的根基也显露。
Zigwa za mʼnyanja zinaonekera poyera, ndipo maziko a dziko lapansi anakhala poyera, Yehova atabangula mwaukali, pamene mpweya wamphamvu unatuluka mʼmphuno mwake.
17 他从高天伸手抓住我, 把我从大水中拉上来。
“Ali kumwamba, Iye anatambalitsa dzanja lake ndipo anandigwira; anandivuwula mʼmadzi ozama.
18 他救我脱离我的劲敌和那些恨我的人, 因为他们比我强盛。
Anandipulumutsa kwa mdani wanga wamphamvu, adani anga amene anali amphamvu kuposa ine.
19 我遭遇灾难的日子,他们来攻击我; 但耶和华是我的倚靠。
Adaniwo analimbana nane pamene ndinali pa mavuto, koma Yehova anali thandizo langa.
20 他又领我到宽阔之处; 他救拔我,因他喜悦我。
Iye anandipititsa kumalo otakasuka; anandipulumutsa chifukwa amakondwera nane.
21 耶和华按着我的公义报答我, 按着我手中的清洁赏赐我。
“Yehova wandithandiza molingana ndi chilungamo changa; molingana ndi makhalidwe anga abwino, Iye wandipulumutsa.
22 因为我遵守了耶和华的道, 未曾作恶离开我的 神。
Pakuti ine ndinatsata njira za Yehova; ndilibe mlandu wochoka pamaso pa Mulungu wanga.
23 他的一切典章常在我面前; 他的律例,我也未曾离弃。
Malamulo ake onse ali pamaso panga, sindinasiye malangizo ake.
24 我在他面前作了完全人; 我也保守自己远离我的罪孽。
Ndakhala moyo wosalakwa pamaso pake ndipo ndakhala ndi kupewa tchimo.
25 所以耶和华按我的公义, 按我在他眼前的清洁赏赐我。
Yehova wandipatsa mphotho molingana ndi chilungamo changa, molingana ndi makhalidwe anga abwino pamaso pake.
26 慈爱的人,你以慈爱待他; 完全的人,你以完全待他;
“Kwa wokhulupirika, Inu mumaonetsa kukhulupirika kwanu, kwa anthu amakhalidwe abwino, Inu mumaonetsanso makhalidwe abwino,
27 清洁的人,你以清洁待他; 乖僻的人,你以弯曲待他。
Kwa woyera mtima, Inu mumaonetsa kuyera mtima kwanu, koma kwa anthu achinyengo mumaonetsanso kunyansidwa nawo.
28 困苦的百姓,你必拯救; 但你的眼目察看高傲的人,使他降卑。
Inu mumapulumutsa anthu odzichepetsa, koma maso anu amatsutsana ndi odzikuza ndipo mumawatsitsa.
29 耶和华啊,你是我的灯; 耶和华必照明我的黑暗。
Inu Yehova, ndinu nyale yanga; Yehova wasandutsa mdima wanga kukhala kuwunika.
30 我借着你冲入敌军, 借着我的 神跳过墙垣。
Ndi thandizo lanu nditha kulimbana ndi gulu la ankhondo, ndi Mulungu wanga nditha kuchita zosatheka ndi munthu.
31 至于 神,他的道是完全的; 耶和华的话是炼净的。 凡投靠他的,他便作他们的盾牌。
“Kunena za Mulungu, zochita zake ndi zangwiro; mawu a Yehova alibe cholakwika. Iye ndi chishango kwa onse amene amathawira kwa iye.
32 除了耶和华,谁是 神呢? 除了我们的 神,谁是磐石呢?
Mulungu wina ndi uti wofanana nanu Yehova? Ndipo ndani amene ndi Thanthwe kupatula Mulungu wathu?
33 神是我坚固的保障; 他引导完全人行他的路。
Ndi Mulungu amene anandipatsa mphamvu ndi kulungamitsa njira yanga.
34 他使我的脚快如母鹿的蹄, 又使我在高处安稳。
Iye amasandutsa mapazi anga kukhala ngati ambawala yayikazi; Iye amandithandiza kuyimirira pamwamba pa mapiri.
35 他教导我的手能以争战, 甚至我的膀臂能开铜弓。
Iye amaphunzitsa manja anga kuchita nkhondo; manja anga amatha kuthyola uta wachitsulo.
36 你把你的救恩给我作盾牌; 你的温和使我为大。
Inu mundipatsa ine chishango chanu cha chigonjetso; mumawerama kuti mundikweze.
37 你使我脚下的地步宽阔; 我的脚未曾滑跌。
Inu mwalimbitsa njira yanga kuti ndiyende bwino, kuti mapazi anga asaterereke.
38 我追赶我的仇敌,灭绝了他们, 未灭以先,我没有归回。
“Ine ndinathamangitsa adani anga ndi kuwakantha; sindinabwerere mpaka iwo atawonongedwa.
39 我灭绝了他们, 打伤了他们,使他们不能起来; 他们都倒在我的脚下。
Ndinawakantha kotheratu, ndipo sanathe kudzukanso; Iwo anagwera pansi pa mapazi anga.
40 因为你曾以力量束我的腰,使我能争战; 你也使那起来攻击我的都服在我以下。
Inu munandipatsa ine mphamvu yochitira nkhondo; munagwaditsa adani anga pa mapazi anga.
41 你又使我的仇敌在我面前转背逃跑, 叫我能以剪除那恨我的人。
Inu muchititsa kuti adani anga atembenuke ndi kuthawa; ndipo ndinawononga adani anga.
42 他们仰望,却无人拯救; 就是呼求耶和华,他也不应允。
Iwo anafuwula kupempha thandizo, koma panalibe ndi mmodzi yemwe owapulumutsa. Analirira kwa Yehova, koma sanawayankhe.
43 我捣碎他们,如同地上的灰尘, 践踏他们,四散在地,如同街上的泥土。
Ine ndinawaperesa ngati fumbi la pa dziko lapansi; ndinawasinja ndipo ndinawapondaponda ngati matope a mʼmisewu.
44 你救我脱离我百姓的争竞, 保护我作列国的元首; 我素不认识的民必事奉我。
“Inu mwandipulumutsa mʼmanja mwa mitundu ya anthu; Inu mwandisunga kuti ndikhale mtsogoleri wa anthu a mitundu ina. Anthu amene sindikuwadziwa ali pansi pa ulamuliro wanga.
45 外邦人要投降我, 一听见我的名声就必顺从我。
Alendo amadzipereka okha pamaso panga; akangomva za ine, amandigonjera.
46 外邦人要衰残, 战战兢兢地出他们的营寨。
Iwo onse anataya mtima; anatuluka mʼmalinga awo akunjenjemera.
47 耶和华是活神,愿我的磐石被人称颂! 愿 神—那拯救我的磐石被人尊崇!
“Yehova ndi wamoyo! Litamandidwe Thanthwe langa. Akuzike Mulungu, Thanthwe, Mpulumutsi wanga!
48 这位 神就是那为我伸冤、 使众民服在我以下的。
Iye ndi Mulungu amene amabwezera chilango, amene amayika anthu a mitundu yonse pansi pa ulamuliro wanga,
49 你救我脱离仇敌, 又把我举起,高过那些起来攻击我的; 你救我脱离强暴的人。
amene amandimasula mʼmanja mwa adani anga. Inu munandikuza kuposa adani anga; munandilanditsa mʼmanja mwa anthu ankhanza.
50 耶和华啊,因此我要在外邦中称谢你, 歌颂你的名。
Choncho ine ndidzakutamandani Inu Yehova, pakati pa anthu a mitundu ina; ndidzayimba nyimbo zotamanda dzina lanu.
51 耶和华赐极大的救恩给他所立的王, 施慈爱给他的受膏者, 就是给大卫和他的后裔, 直到永远!
“Iye amapereka chipambano chachikulu kwa mfumu yake, amaonetsa kukoma mtima kwa wodzozedwa wake, kwa Davide ndi zidzukulu zake kwamuyaya.”

< 撒母耳记下 22 >