< 撒母耳记下 15 >

1 此后,押沙龙为自己预备车马,又派五十人在他前头奔走。
Patapita nthawi, Abisalomu anadzipezera galeta ndi akavalo pamodzi ndi amuna makumi asanu amene amathamanga patsogolo pake.
2 押沙龙常常早晨起来,站在城门的道旁,凡有争讼要去求王判断的,押沙龙就叫他过来,问他说:“你是哪一城的人?”回答说:“仆人是以色列某支派的人。”
Iye amadzuka mmamawa ndi kuyima pa njira yopita ku chipata cha mzinda. Munthu wina aliyense akakhala ndi zodandaula zopita nazo kwa mfumu kuti akaweruze, Abisalomu amamuyitana iye ndi kumufunsa kuti, “Kodi ukuchokera ku limodzi mwa mafuko a Israeli?”
3 押沙龙对他说:“你的事有情有理,无奈王没有委人听你伸诉。”
Kenaka Abisalomu amanena kwa iye kuti, “Taona, madandawulo ako ndi abwino ndi oyenera, koma palibe woyimira mfumu woti akumvere.”
4 押沙龙又说:“恨不得我作国中的士师!凡有争讼求审判的到我这里来,我必秉公判断。”
Ndipo Abisalomu amawonjezera kunena kuti, “Ine ndikanangosankhidwa kukhala woweruza mʼdziko muno bwenzi munthu aliyense amene ali ndi madandawulo kapena milandu akubwera kwa ine ndipo ndikanaonetsetsa kuti chilungamo chachitika.”
5 若有人近前来要拜押沙龙,押沙龙就伸手拉住他,与他亲嘴。
Ndipo nthawi zonse amati munthu akasendera pafupi ndi kumugwandira, Abisalomu amatambalitsa dzanja lake, kumuyimiritsa munthuyo ndi kupsompsona.
6 以色列人中,凡去见王求判断的,押沙龙都是如此待他们。这样,押沙龙暗中得了以色列人的心。
Abisalomu amachitira izi Aisraeli onse amene amabwera kwa mfumu kuti adzaweruzidwe ndipo Abisalomuyo anagwira mtima anthu a mu Israeli.
7 满了四十年,押沙龙对王说:“求你准我往希伯 去,还我向耶和华所许的愿。
Patapita zaka zinayi Abisalomu anati kwa mfumu, “Loleni ndipite ku Hebroni kuti ndikakwaniritse lonjezo limene ndinachita kwa Yehova.
8 因为仆人住在亚兰的基述,曾许愿说:‘耶和华若使我再回耶路撒冷,我必事奉他。’”
Pamene mtumiki wanu amakhala ku Gesuri ku Aramu, anachita lonjezo ili: ‘Ngati Yehova adzandibweretsadi ku Yerusalemu, ndidzapembedza Yehovayo mu Hebroni.’”
9 王说:“你平平安安地去吧!”押沙龙就起身,往希伯 去了。
Mfumu inati kwa iye, “Pita mu mtendere” Kotero iye anapita ku Hebroni.
10 押沙龙打发探子走遍以色列各支派,说:“你们一听见角声就说:‘押沙龙在希伯 作王了!’”
Ndipo Abisalomu anatuma amithenga ake mwamseri kwa mafuko onse a Israeli kukanena kuti, “Mukangomva kulira kwa malipenga pamenepo munene kuti, ‘Abisalomu ndiye mfumu mu Hebroni.’”
11 押沙龙在耶路撒冷请了二百人与他同去,都是诚诚实实去的,并不知道其中的真情。
Anthu 200 ochokera mu Yerusalemu anapita naye Abisalomu. Iwo anayitanidwa monga alendo ndipo anapita osadziwa chilichonse pa nkhaniyi.
12 押沙龙献祭的时候,打发人去将大卫的谋士、基罗人亚希多弗从他本城请了来。于是叛逆的势派甚大;因为随从押沙龙的人民,日渐增多。
Pamene Abisalomu amapereka nsembe, iye anayitanitsanso Ahitofele Mgiloni, mlangizi wa Davide, wa ku Gilo, kotero kuwukiraku kunakula kwambiri, ndipo anthu otsatira Abisalomu anapitirira kuchuluka.
13 有人报告大卫说:“以色列人的心都归向押沙龙了!”
Munthu wina anabweretsa uthenga ndi kudzamuwuza Davide kuti, “Mitima ya Aisraeli onse ili pa Abisalomu.”
14 大卫就对耶路撒冷跟随他的臣仆说:“我们要起来逃走,不然都不能躲避押沙龙了;要速速地去,恐怕他忽然来到,加害于我们,用刀杀尽合城的人。”
Ndipo Davide anati kwa akuluakulu ake amene anali mu Yerusalemu. “Bwerani! Tiyeni tithawe, mwina palibe adzapulumuke kwa Abisalomu. Tiyeni tichoke msanga, mwina iye adzabwera msanga ndi kutipitirira, nʼkuwononga ife ndi mzinda wathu ndi lupanga.”
15 王的臣仆对王说:“我主我王所定的,仆人都愿遵行。”
Akuluakulu a mfumu anamuyankha kuti, “Antchito anu ndi okonzeka kuchita chilichonse chimene mbuye wathu mfumu mukufuna kuchita.”
16 于是王带着全家的人出去了,但留下十个妃嫔看守宫殿。
Mfumu inanyamuka pamodzi ndi banja lake lonse. Koma iye anasiya azikazi khumi kuti azisamalira nyumba yaufumu.
17 王出去,众民都跟随他,到伯·墨哈,就住下了。
Kotero mfumu inanyamuka pamodzi ndi anthu onse oyitsatira, ndipo anayima pamalo pena chapatalipo.
18 王的臣仆都在他面前过去。基利提人、比利提人,就是从迦特跟随王来的六百人,也都在他面前过去。
Ankhondo ake onse anayamba kuyenda pamaso pa Davide, ndipo Akereti ndi Apeleti, pamodzinso ndi Agiti okwanira 600 amene anamutsata kuchokera ku Gati, nawonso anayenda pamaso pake.
19 王对迦特人以太说:“你是外邦逃来的人,为什么与我们同去呢?你可以回去与新王同住,或者回你本地去吧!
Mfumu inati kwa Itai Mgiti, “Nʼchifukwa chiyani iwe ukupita ndi ife? Bwerera ndipo ukakhale ndi mfumu Abisalomu. Iwe ndiwe mlendo munthu wothawa kwawo.
20 你来的日子不多,我今日怎好叫你与我们一同飘流、没有一定的住处呢?你不如带你的弟兄回去吧!愿耶和华用慈爱诚实待你。”
Wangobwera dzulo lomweli, lero ndikutenge kuti uziyendayenda ndi ife, pamene ine sindikudziwa kumene ndikupita? Bwerera, ndipo tenga abale ako. Chifundo ndi kukhulupirika zikhale nawe.”
21 以太对王说:“我指着永生的耶和华起誓,又敢在王面前起誓:无论生死,王在哪里,仆人也必在那里。”
Koma Itai anayankha mfumu kuti, “Pali Yehova wamoyo, kulikonse kumene mbuye wanga mfumu mudzakhala, kaya ndi moyo kapena imfa, mtumiki wanu adzakhala komweko.”
22 大卫对以太说:“你前去过河吧!”于是迦特人以太带着跟随他的人和所有的妇人孩子,就都过去了。
Davide anati kwa Itai, “Tiye pita nafe” Kotero Itai Mgiti anayenda pamodzi ndi anthu ake ndi mabanja amene anali naye.
23 本地的人都放声大哭。众民尽都过去,王也过了汲沦溪;众民往旷野去了。
Anthu onse a madera ozungulira analira mofuwula pamene anthu onsewo amadutsa. Mfumunso inawoloka chigwa cha Kidroni, ndipo anthu onse anayenda kulowera ku chipululu.
24 撒督和抬 神约柜的利未人也一同来了,将 神的约柜放下。亚比亚他上来,等着众民从城里出来过去。
Zadoki anali nawonso, ndipo Alevi onse amene anali naye ananyamula Bokosi la Chipangano la Mulungu. Iwo anayika pansi Bokosi la Mulungulo ndipo Abiatara ankapereka nsembe mpaka pamene anthu onse anamaliza kutuluka mu mzinda.
25 王对撒督说:“你将 神的约柜抬回城去。我若在耶和华眼前蒙恩,他必使我回来,再见约柜和他的居所。
Kenaka mfumu inati kwa Zadoki, “Tenga Bokosi la Mulungu ubwerere nalo mu mzinda. Ngati ndidzapeza chifundo pamaso pa Yehova, adzandibweretsa kuti ndilionenso ndi malo ake okhalamo.
26 倘若他说:‘我不喜悦你’,看哪,我在这里,愿他凭自己的意旨待我!”
Koma iye anati, ‘Akapanda kukondwera nane,’ chabwino, andichite chimene chimukomere.”
27 王又对祭司撒督说:“你不是先见吗?你可以安然回城;你儿子亚希玛斯和亚比亚他的儿子约拿单都可以与你同去。
Mfumu inatinso kwa wansembe Zadoki, “Kodi siwe mlosi? Bwerera mu mzinda mwamtendere pamodzi ndi mwana wako Ahimaazi ndi Yonatani mwana wa Abiatara. Iwe ndi Abiatara tengani ana anu awiri.
28 我在旷野的渡口那里等你们报信给我。”
Ine ndidzadikira powolokera Yorodani ku chipululu mpaka nditalandira mawu ochokera kwa iwe ondiwuza mmene zilili zinthu.”
29 于是撒督和亚比亚他将 神的约柜抬回耶路撒冷,他们就住在那里。
Kotero Zadoki ndi Abiatara ananyamula Bokosi la Mulungu lija nabwerera nalo ku Yerusalemu, ndipo anakakhala kumeneko.
30 大卫蒙头赤脚上橄榄山,一面上一面哭。跟随他的人也都蒙头哭着上去;
Koma Davide anapitirira ndi kukakwera phiri la Olivi akupita nalira. Anafunda kumutu koma sanavale nsapato. Anthu onse amene anali naye anafundanso kumutu, ndipo nawonso amalira pamene amapita.
31 有人告诉大卫说:“亚希多弗也在叛党之中,随从押沙龙。”大卫祷告说:“耶和华啊,求你使亚希多弗的计谋变为愚拙!”
Tsono Davide anamva kuti, “Ahitofele ali pakati pa anthu owukira pamodzi ndi Abisalomu.” Choncho Davide anapemphera, “Inu Yehova, musandutse uphungu wa Ahitofele ukhale uchitsiru.”
32 大卫到了山顶、敬拜 神的地方,见亚基人户筛,衣服撕裂,头蒙灰尘来迎接他。
Davide atafika pamwamba pa phiri pomwe anthu ankapembedzerapo Mulungu, Husai Mwariki anadzakumana naye atangʼamba mkanjo wake ndi kudzithira fumbi kumutu.
33 大卫对他说:“你若与我同去,必累赘我;
Davide anati kwa iye, “Ngati iwe upite ndi ine, udzakhala chondilemetsa.
34 你若回城去,对押沙龙说:‘王啊,我愿作你的仆人;我向来作你父亲的仆人,现在我也照样作你的仆人。’这样,你就可以为我破坏亚希多弗的计谋。
Koma ngati ubwerera ku mzinda ndi kukanena kwa Abisalomu kuti, ‘Inu mfumu ine ndidzakhala wantchito wanu.’ Mʼmbuyomu ndinali wantchito wa abambo anu koma tsopano ndidzakhala wantchito wanu. Ukatero udzandithandiza kulepheretsa malangizo a Ahitofele.
35 祭司撒督和亚比亚他岂不都在那里吗?你在王宫里听见什么,就要告诉祭司撒督和亚比亚他。
Kodi ansembe, Zadoki ndi Abiatara, sakukhala nawe kumeneko? Ukawawuze zonse zimene umamva mʼnyumba yaufumu.
36 撒督的儿子亚希玛斯,亚比亚他的儿子约拿单,也都在那里。凡你们所听见的可以托这二人来报告我。”
Ana awo awiri, Ahimaazi wa Zadoki, ndi Yonatani mwana wa Abiatara ali nawo pamodzi, uzikawatuma kwa ine ndi china chilichonse chimene ukamve.”
37 于是,大卫的朋友户筛进了城;押沙龙也进了耶路撒冷。
Ndipo Husai bwenzi la Davide anafika ku Yerusalemu pamene Abisalomu amalowa mu mzinda.

< 撒母耳记下 15 >