< 撒母耳记下 13 >

1 大卫的儿子押沙龙有一个美貌的妹子,名叫她玛。大卫的儿子暗嫩爱她。
Patapita nthawi, Amnoni mwana wa Davide anakonda Tamara, mlongo wa Abisalomu, mwana wa Davide, amene anali wokongola.
2 暗嫩为他妹子她玛忧急成病。她玛还是处女,暗嫩以为难向她行事。
Amnoni sankagona tulo mpaka anadwala chifukwa cha Tamara mlongo wakeyo, pakuti iye anali asanagonepo ndi mwamuna ndipo zimaoneka kuti zinali zosatheka kuti achite chilichonse kwa iye.
3 暗嫩有一个朋友,名叫约拿达,是大卫长兄示米亚的儿子。这约拿达为人极其狡猾;
Koma Amnoni anali ndi mnzake dzina lake Yehonadabu mwana wamwamuna wa Simea, mʼbale wake wa Davide. Yonadabu anali munthu wochenjera kwambiri.
4 他问暗嫩说:“王的儿子啊,为何一天比一天瘦弱呢?请你告诉我。”暗嫩回答说:“我爱我兄弟押沙龙的妹子她玛。”
Iye anafunsa Amnoni, “Nʼchifukwa chiyani iwe mwana wa mfumu, umaoneka wowonda mmawa uliwonse? Bwanji wosandiwuza?” Amnoni anamuyankha kuti, “Ine ndamukonda Tamara, mlongo wa mʼbale wanga Abisalomu.”
5 约拿达说:“你不如躺在床上装病;你父亲来看你,就对他说:‘求父叫我妹子她玛来,在我眼前预备食物,递给我吃,使我看见,好从她手里接过来吃。’”
Yehonadabu anati, “Pita ukagone ndipo unamizire kudwala. Abambo ako akabwera kudzakuona, udzati kwa iwo, Ine ndikufuna mlongo wanga Tamara abwere kuti adzandikonzere chakudya kuti ndidye. Adzandikonzere chakudyacho ine ndikumuona ndi kudya chili mʼmanja mwake.”
6 于是暗嫩躺卧装病。王来看他,他对王说:“求父叫我妹子她玛来,在我眼前为我做两个饼,我好从她手里接过来吃。”
Kotero Amnoni anagona nakhala ngati akudwala. Mfumu itabwera kudzamuona, Amnoni anati kwa iyo, “Ine ndikufuna mlongo wanga Tamara kuti abwere adzandipangire buledi wapamwamba ineyo ndikuona, kuti ndidye ali mʼmanja mwake.”
7 大卫就打发人到宫里,对她玛说:“你往你哥哥暗嫩的屋里去,为他预备食物。”
Davide anatumiza mawu kwa Tamara ku nyumba yaufumu kuti, “Pita ku nyumba ya mlongo wako Amnoni ndipo ukamukonzere chakudya.”
8 她玛就到她哥哥暗嫩的屋里;暗嫩正躺卧。她玛抟面,在他眼前做饼,且烤熟了,
Choncho Tamara anapitadi ku nyumba ya mlongo wake Amnoni kumalo kumene ankagona. Anakanda ufa, nawumba buledi Amunoniyo akuona ndipo anaphika bulediyo.
9 在他面前将饼从锅里倒出来,他却不肯吃,便说:“众人离开我出去吧!”众人就都离开他,出去了。
Kenaka iye anatenga chiwaya ndipo anamupatsa bulediyo, koma iyeyo anakana. Amnoni anati “Uza aliyense atuluke muno.” Ndipo aliyense anatuluka.
10 暗嫩对她玛说:“你把食物拿进卧房,我好从你手里接过来吃。”她玛就把所做的饼拿进卧房,到她哥哥暗嫩那里,
Kenaka Amnoni anati kwa Tamara, “Bweretsa chakudya kuno, ku chipinda changa chogona kuti ndidye chili mʼmanja mwako.” Ndipo Tamara anatenga buledi amene anapanga ndi kubwera naye kwa mlongo wake ku chipinda chake.
11 拿着饼上前给他吃,他便拉住她玛,说:“我妹妹,你来与我同寝。”
Koma atabweretsa kwa iye kuti adye, anamugwira ndipo anati, “Bwera ugone nane, iwe mlongo wanga.”
12 她玛说:“我哥哥,不要玷辱我。以色列人中不当这样行,你不要做这丑事;
Tamara anati kwa iye, “Ayi mlongo wanga! Usandikakamize. Zotere siziyenera kuchitika mu Israeli! Usachite chinthu choyipa chotere.
13 你玷辱了我,我何以掩盖我的羞耻呢?你在以色列中也成了愚妄人。你可以求王,他必不禁止我归你。”
Kodi ukuganiza bwanji za ine? Kodi manyazi anga ndidzawachotsa bwanji? Ndipo nanga iweyo? Udzakhalatu monga mmodzi mwa zitsiru zoyipitsitsa muno mu Israeli. Chonde kapemphe kwa mfumu. Sadzakuletsa kuti undikwatire.”
14 但暗嫩不肯听她的话,因比她力大,就玷辱她,与她同寝。
Koma sanamvere zimene amanena Tamara ndipo popeza anali wamphamvu kuposa Tamarayo, iye anamugwirira.
15 随后,暗嫩极其恨她,那恨她的心比先前爱她的心更甚,对她说:“你起来,去吧!”
Atatero Amnoni anadana naye kwambiri. Iyeyo anamuda kuposa momwe anamukondera. Amnoni anati, “Dzuka ndipo tuluka!”
16 她玛说:“不要这样!你赶出我去的这罪比你才行的更重!”但暗嫩不肯听她的话,
Iye anayankha, “Ayi! Kundithamangitsa kukhala kulakwa kwakukulu kuposa zimene wachita kale kwa ine.” Koma anakana kumumvera.
17 就叫伺候自己的仆人来,说:“将这个女子赶出去!她一出去,你就关门,上闩。”
Amnoni anayitana wantchito wake ndipo anati, “Mutulutse mkazi uyu muno ndipo utseke chitseko akatuluka.”
18 那时她玛穿着彩衣,因为没有出嫁的公主都是这样穿。暗嫩的仆人就把她赶出去,关门上闩。
Choncho wantchito wakeyo anamutulutsa ndipo anatseka chitseko atatuluka. Tamara anali atavala mkanjo wokongoletsedwa kwambiri, pakuti ichi chinali chovala chimene ana aakazi a mfumu amene sanagonepo ndi mwamuna amavala.
19 她玛把灰尘撒在头上,撕裂所穿的彩衣,以手抱头,一面行走,一面哭喊。
Tamara anatsira phulusa pamutu pake ndipo anangʼamba mkanjo wokongoletsedwa umene anavalawo. Iye anagwira manja ake kumutu ndipo anachoka, akulira mokweza pamene amapita.
20 她胞兄押沙龙问她说:“莫非你哥哥暗嫩与你亲近了吗?我妹妹,暂且不要作声,他是你的哥哥,不要将这事放在心上。”她玛就孤孤单单地住在她胞兄押沙龙家里。
Mlongo wake Abisalomu anati, “Kodi Amnoni uja mlongo wako wagona nawe? Khala chete mlongo wanga. Iye uja ndi mlongo wako ndipo usazilabadire.” Choncho Tamara anakhala mʼnyumba ya Abisalomu mlongo wake ngati woferedwa.
21 大卫王听见这事,就甚发怒。
Mfumu Davide itamva zimenezi, inakwiya kwambiri.
22 押沙龙并不和他哥哥暗嫩说好说歹;因为暗嫩玷辱他妹妹她玛,所以押沙龙恨恶他。
Abisalomu sananene mawu aliwonse kwa Amnoni; abwino kapena oyipa. Iye anamuda Amunoniyo chifukwa anachititsa manyazi mlongo wake Tamara.
23 过了二年,在靠近以法莲的巴力·夏琐有人为押沙龙剪羊毛;押沙龙请王的众子与他同去。
Patapita zaka ziwiri, pamene wometa nkhosa za Abisalomu anali ku Baala-Hazori pafupi ndi malire a fuko la Efereimu, iye anayitana ana onse aamuna a mfumu kuti apite kumeneko.
24 押沙龙来见王,说:“现在有人为仆人剪羊毛,请王和王的臣仆与仆人同去。”
Abisalomu anapita kwa mfumu ndipo anati, “Ometa nkhosa za mtumiki wanu anabwera. Chonde mfumu ndi akuluakulu anu mubwere kudzakhala nane?”
25 王对押沙龙说:“我儿,我们不必都去,恐怕使你耗费太多。”押沙龙再三请王,王仍是不肯去,只为他祝福。
Mfumu inayankha kuti, “Ayi mwana wanga, tisapite tonsefe. Tidzakhala cholemetsa kwa iwe.” Ngakhale Abisalomu anayesetsa kuwumiriza mfumuyo, inakana kupita. Mʼmalo mwake inangomudalitsa Abisalomuyo.
26 押沙龙说:“王若不去,求王许我哥哥暗嫩同去。”王说:“何必要他去呢?”
Kenaka Abisalomu anati, “Ngati sizitero, chonde mulole mʼbale wanga Amnoni apite nane.” Mfumu inamufunsa kuti, “Apite nawe chifukwa chiyani?”
27 押沙龙再三求王,王就许暗嫩和王的众子与他同去。
Koma Abisalomu anamuwumiriza, kotero analola kuti Amnoni pamodzi ndi ana onse a mfumu apite naye.
28 押沙龙吩咐仆人说:“你们注意,看暗嫩饮酒畅快的时候,我对你们说杀暗嫩,你们便杀他,不要惧怕。这不是我吩咐你们的吗?你们只管壮胆奋勇!”
Abisalomu analamula antchito ake kuti, “Tamverani! Amnoni akakaledzera ndi vinyo ndipo ine ndikakanena kuti, ‘Mukantheni Amnoni,’ pamenepo mukamuphe. Musakachite mantha. Kodi ine sindinakulamuleni? Mukhale amphamvu ndipo mulimbe mtima.”
29 押沙龙的仆人就照押沙龙所吩咐的,向暗嫩行了。王的众子都起来,各人骑上骡子,逃跑了。
Kotero antchito a Abisalomu anachita kwa Amnoni zimene Abisalomu anawalamula. Kenaka ana onse a mfumu anayimirira ndipo anakwera pa abulu awo nathawa.
30 他们还在路上,有风声传到大卫那里,说:“押沙龙将王的众子都杀了,没有留下一个。”
Ali mʼnjira, Davide anamva mphekesera yakuti, “Abisalomu wakantha ana onse a mfumu ndipo palibe ndi mmodzi yemwe amene watsala.”
31 王就起来,撕裂衣服,躺在地上。王的臣仆也都撕裂衣服,站在旁边。
Mfumu inayimirira, ningʼamba zovala zake ndi kugona pa dothi. Antchito ake onse anayimirira pomwepo atangʼamba zovala zawo.
32 大卫的长兄,示米亚的儿子约拿达说:“我主,不要以为王的众子—少年人都杀了,只有暗嫩一个人死了。自从暗嫩玷辱押沙龙妹子她玛的那日,押沙龙就定意杀暗嫩了。
Koma Yehonadabu mwana wa Simea, mʼbale wake wa Davide anati, “Mbuye wanga mfumu musaganize kuti wapha ana onse a mfumu; wafa ndi Amnoni yekha. Awa ndiwo akhala maganizo a Abisalomu kuyambira tsiku limene Amnoni anagwirira mlongo wake Tamara.
33 现在,我主我王,不要把这事放在心上,以为王的众子都死了,只有暗嫩一个人死了。”
Mbuye wanga mfumu musavutike ndi maganizo ndi nkhani yoti ana onse a mfumu afa. Wafa ndi Amnoni yekha.”
34 押沙龙逃跑了。 守望的少年人举目观看,见有许多人从山坡的路上来。
Nthawi imeneyi nʼkuti Abisalomu atathawa. Tsono munthu amene amalondera anayangʼana ndipo anaona anthu ambiri pa msewu wa kumadzulo kwake, akubwera kutsetsereka phiri. Mlondayo anapita kukawuza mfumu kuti, “Ndikuona anthu pa njira ya Horonaimu, mʼmbali mwa phiri.”
35 约拿达对王说:“看哪,王的众子都来了,果然与你仆人所说的相合。”
Yehonadabu anati kwa mfumu, “Taonani ana a mfumu afika. Zachitika monga momwe mtumiki wanu ananenera.”
36 话才说完,王的众子都到了,放声大哭;王和臣仆也都哭得甚恸。
Pamene amatsiriza kuyankhula, ana a mfumu analowa, akulira mofuwula. Mfumunso ndi antchito ake onse analira mokhudzidwa.
37 押沙龙逃到基述王亚米忽的儿子达买那里去了。大卫天天为他儿子悲哀。
Abisalomu anathawa, napita kwa Talimai mwana wa Amihudi, mfumu ya ku Gesuri. Koma mfumu Davide inalira mwana wake tsiku ndi tsiku.
38 押沙龙逃到基述,在那里住了三年。
Abisalomu atathawa ndi kupita ku Gesuri, anakhala kumeneko zaka zitatu.
39 暗嫩死了以后,大卫王得了安慰,心里切切想念押沙龙。
Ndipo Davide anagwidwa ndi chifundo chofuna kumulondola Abisalomu pakuti anali atatonthozedwa pa imfa ya Amnoni.

< 撒母耳记下 13 >