< 撒母耳记下 1 >

1 扫罗死后,大卫击杀亚玛力人回来,在洗革拉住了两天。
Atamwalira Sauli, Davide anabwerako kumene anakagonjetsa Aamaleki ndipo anakakhala ku Zikilagi masiku awiri.
2 第三天,有一人从扫罗的营里出来,衣服撕裂,头蒙灰尘,到大卫面前伏地叩拜。
Pa tsiku lachitatu munthu wina wochokera ku msasa wa Sauli anafika, zovala zake zitangʼambika ndiponso anali atathira dothi pamutu pake. Atafika kwa Davide, anadzigwetsa pansi, kupereka ulemu kwa Davideyo.
3 大卫问他说:“你从哪里来?”他说:“我从以色列的营里逃来。”
Davide anamufunsa iye kuti, “Kodi iwe wachokera kuti?” Iye anayankha kuti, “Ine ndathawa ku misasa ya Aisraeli.”
4 大卫又问他说:“事情怎样?请你告诉我。”他回答说:“百姓从阵上逃跑,也有许多人仆倒死亡;扫罗和他儿子约拿单也死了。”
Davide anafunsa, “Tandiwuza, chachitika ndi chiyani?” Iye anati, “Anthu athawa ku nkhondo ndipo ambiri aphedwa. Sauli ndi mwana wake Yonatani aphedwa.”
5 大卫问报信的少年人说:“你怎么知道扫罗和他儿子约拿单死了呢?”
Ndipo Davide anati kwa mnyamata amene anabweretsa nkhaniyi, “Ukudziwa bwanji kuti Sauli ndi mwana wake Yonatani afa?”
6 报信的少年人说:“我偶然到基利波山,看见扫罗伏在自己枪上,有战车、马兵紧紧地追他。
Mnyamatayo anati, “Zinangochitika kuti ndinali pa phiri la Gilibowa, ndipo Sauli anali komweko ataweramira pa mkondo wake, pamodzi ndi magaleta ndi okwera ake atamuyandikira.
7 他回头看见我,就呼叫我。我说:‘我在这里。’
Pamene anatembenuka ndi kundiona ine, iye anandiyitana, ndipo ndinati, ‘Kodi ndichite chiyani?’”
8 他问我说:‘你是什么人?’我说:‘我是亚玛力人。’
Iye anandifunsa, “Iwe ndiwe yani?” Ine ndinayankha kuti, “Ndine Mwamaleki.”
9 他说:‘请你来,将我杀死;因为痛苦抓住我,我的生命尚存。’
“Kenaka iye anati kwa ine, ‘Bwera pafupi ndipo undiphe! Ndikumva ululu kwambiri, koma ndikanali ndi moyo!’
10 我准知他仆倒必不能活,就去将他杀死,把他头上的冠冕、臂上的镯子拿到我主这里。”
“Kotero ndinabwera pafupi ndi kumupha, chifukwa ndinadziwa kuti mmene anagweramo sakanakhalanso ndi moyo. Ndipo ndatenga chipewa chaufumu chimene chinali pamutu pake ndi khoza la pa dzanja lake ndipo ndazibweretsa kwa inu mbuye wanga.”
11 大卫就撕裂衣服,跟随他的人也是如此,
Apo Davide ndi anthu onse amene anali nawo anangʼamba zovala zawo.
12 而且悲哀哭号,禁食到晚上,是因扫罗和他儿子约拿单,并耶和华的民以色列家的人,倒在刀下。
Iwo analira maliro ndi kusala zakudya mpaka madzulo chifukwa cha Sauli ndi mwana wake Yonatani, komanso chifukwa cha gulu la ankhondo la Yehova ndi nyumba ya Israeli, chifukwa anaphedwa ndi lupanga.
13 大卫问报信的少年人说:“你是哪里的人?”他说:“我是亚玛力客人的儿子。”
Davide anati kwa mnyamata amene anabweretsa uthengawo, “Iwe umachokera kuti?” Iye anayankha kuti, “Ine ndine mwana wa mlendo Mwamaleki.”
14 大卫说:“你伸手杀害耶和华的受膏者,怎么不畏惧呢?”
Davide anamufunsanso kuti, “Nʼchifukwa chiyani sunaope kukweza dzanja lako ndi kupha wodzozedwa wa Yehova?”
15 大卫叫了一个少年人来,说:“你去杀他吧!”
Kenaka Davide anayitana mmodzi mwa anyamata ake ndipo anati, “Pita ukamukanthe!” Kotero iye anapita kukamukantha, ndipo mnyamata uja anafa.
16 大卫对他说:“你流人血的罪归到自己的头上,因为你亲口作见证说:‘我杀了耶和华的受膏者。’”少年人就把他杀了。
Pakuti Davide anali atanena kwa iye kuti, “Iwe wadzipha wekha. Pakamwa pako pakunena zokutsutsa wekha, pamene unanena kuti, ‘Ine ndapha wodzozedwa wa Yehova.’”
17 大卫作哀歌,吊扫罗和他儿子约拿单,
Davide anayimba nyimbo iyi ya maliro, kulira Sauli ndi mwana wake Yonatani.
18 且吩咐将这歌教导犹大人。这歌名叫“弓歌”,写在雅煞珥书上。
Ndipo analamula kuti anthu a ku Yuda aphunzitsidwe nyimbo ya maliroyi imene yalembedwa mʼbuku la Yasari:
19 歌中说:以色列啊, 你尊荣者在山上被杀! 大英雄何竟死亡!
“Ulemerero wako iwe Israeli, wagona utaphedwa ku zitunda. Taonani amphamvu agwa kumeneko!
20 不要在迦特报告; 不要在亚实基伦街上传扬; 免得非利士的女子欢乐; 免得未受割礼之人的女子矜夸。
“Musakanene zimenezi ku Gati, musazilengeze ku misewu ya ku Asikeloni, kuti ana aakazi a Afilisti angasangalale, ana aakazi a osachita mdulidwe angakondwere.
21 基利波山哪,愿你那里没有雨露! 愿你田地无土产可作供物! 因为英雄的盾牌在那里被污丢弃; 扫罗的盾牌仿佛未曾抹油。
“Inu mapiri a ku Gilibowa, musakhalenso ndi mame kapena mvula, kapena minda yobereka zopereka za ufa. Pakuti kumeneko chishango cha munthu wamphamvu chinadetsedwa, chishango cha Sauli sanachipakenso mafuta.
22 约拿单的弓箭非流敌人的血不退缩; 扫罗的刀剑非剖勇士的油不收回。
“Pa magazi a ophedwa, pa mnofu wa amphamvu, uta wa Yonatani sunabwerere, lupanga la Sauli silinabwere chabe.
23 扫罗和约拿单— 活时相悦相爱,死时也不分离 —他们比鹰更快,比狮子还强。
“Sauli ndi Yonatani, pa moyo wawo anali okondedwa ndi okoma mtima, ndipo pa imfa yawo sanasiyanitsidwe. Iwo anali ndi liwiro loposa ziwombankhanga, anali ndi mphamvu zoposa mkango.
24 以色列的女子啊,当为扫罗哭号! 他曾使你们穿朱红色的美衣, 使你们衣服有黄金的妆饰。
“Inu ana aakazi a Israeli, mulireni Sauli, amene anakuvekani zovala zofiira ndi zofewa, amene anakometsera zovala zanu ndi zokometsera zagolide.
25 英雄何竟在阵上仆倒! 约拿单何竟在山上被杀!
“Taonani amphamvu agwa ku nkhondo! Yonatani wagona ataphedwa ku zitunda.
26 我兄约拿单哪,我为你悲伤! 我甚喜悦你! 你向我发的爱情奇妙非常, 过于妇女的爱情。
Ine ndikuvutika mumtima chifukwa cha iwe mʼbale wanga Yonatani, unali wokondedwa kwambiri kwa ine. Chikondi chako pa ine chinali chopambana, chopambana kuposa chikondi cha akazi.
27 英雄何竟仆倒! 战具何竟灭没!
“Taonani amphamvu agwa! Zida zankhondo zawonongeka!”

< 撒母耳记下 1 >