< 列王纪下 9 >

1 先知以利沙叫了一个先知门徒来,吩咐他说:“你束上腰,手拿这瓶膏油往基列的拉末去。
Mneneri Elisa anayitanitsa mmodzi mwa ana a aneneri, namuwuza kuti, “Manga lamba mʼchiwuno mwako, tenga botolo la mafuta mʼdzanja lako ndipo upite ku Ramoti Giliyadi.
2 到了那里,要寻找宁示的孙子、约沙法的儿子耶户,使他从同僚中起来,带他进严密的屋子,
Ukakafika kumeneko, ukafunefune Yehu mwana wa Yehosafati, mwana wa Nimisi. Ukapite kwa iye, ukamuchotse pakati pa anzake ndi kukamulowetsa mʼchipinda chamʼkati.
3 将瓶里的膏油倒在他头上,说:‘耶和华如此说:我膏你作以色列王。’说完了,就开门逃跑,不要迟延。”
Ndipo ukatenge botololi ndi kuthira mafuta pa mutu wake ndipo ukanene kuti, ‘Yehova akuti, Ine ndikudzoza iwe kukhala mfumu ya Israeli.’ Kenaka ukatsekule chitseko ndi kuthawa ndipo usakachedwe!”
4 于是那少年先知往基列的拉末去了。
Choncho mneneri wachinyamatayo anapita ku Ramoti Giliyadi.
5 到了那里,看见众军长都坐着,就说:“将军哪,我有话对你说。”耶户说:“我们众人里,你要对哪一个说呢?”回答说:“将军哪,我要对你说。”
Atafika ku Giliyadiko anapeza atsogoleri a ankhondo ali pa msonkhano. Iye anati, “Mtsogoleri, ine ndili ndi uthenga wanu.” Ndipo Yehu anafunsa kuti, “Uthengawo ndi wa yani pakati pathu?” Mneneriyo anayankha kuti, “Ndi wa inuyo, mtsogoleri.”
6 耶户就起来,进了屋子,少年人将膏油倒在他头上,对他说:“耶和华—以色列的 神如此说:‘我膏你作耶和华民以色列的王。
Yehu anayimirira nakalowa mʼnyumba. Pamenepo mneneriyo anakhuthulira mafuta pamutu pa Yehu ndipo ananena kuti, “Yehova Mulungu wa Israeli akuti, ‘Ine ndikukudzoza kukhala mfumu ya Israeli, anthu a Yehova.
7 你要击杀你主人亚哈的全家,我好在耶洗别身上伸我仆人众先知和耶和华一切仆人流血的冤。
Uyenera kuwononga nyumba ya mbuye wako Ahabu ndipo ndidzabwezera imfa ya atumiki anga, aneneri ndiponso imfa ya atumiki ena onse a Yehova amene anaphedwa ndi Yezebeli.
8 亚哈全家必都灭亡,凡属亚哈的男丁,无论是困住的、自由的,我必从以色列中剪除,
Banja lonse la Ahabu lidzatheratu. Ndidzachotsa munthu aliyense wamwamuna wa banja la Ahabu kaya ndi kapolo kapena mfulu.
9 使亚哈的家像尼八儿子耶罗波安的家,又像亚希雅儿子巴沙的家。
Ndidzachititsa kuti banja la Ahabu lifanane ndi banja la Yeroboamu mwana wa Nebati ndiponso ngati banja la Baasa mwana wa Ahiya.
10 耶洗别必在耶斯列田里被狗所吃,无人葬埋。’”说完了,少年人就开门逃跑了。
Kunena za Yezebeli, agalu adzamudya ku dera la Yezireeli ndipo palibe amene adzamuyike mʼmanda.’” Kenaka mneneriyo anatsekula chitseko nʼkuthawa.
11 耶户出来,回到他主人的臣仆那里,有一人问他说:“平安吗?这狂妄的人来见你有什么事呢?”回答说:“你们认得那人,也知道他说什么。”
Yehu atatuluka kupita kumene kunali atsogoleri anzake, mmodzi mwa iwo anamufunsa kuti, “Kodi zonse zili bwino? Kodi munthu wamisala uja anabwera kudzatani kwa iwe?” Yehu anayankha kuti, “Iwe ukumudziwa munthu uja ndiponso ukudziwa zomwe amayankhula.”
12 他们说:“这是假话,你据实地告诉我们。”回答说:“他如此如此对我说。他说:‘耶和华如此说:我膏你作以色列王。’”
Atsogoleri aja anati, “Ukunama! Tiwuze.” Yehu anati, “Zimene wandiwuza ndi izi: ‘Yehova akuti: Ine ndakudzoza iwe kukhala mfumu ya Israeli.’”
13 他们就急忙各将自己的衣服铺在上层台阶,使耶户坐在其上;他们吹角,说:“耶户作王了!”
Atsogoleri aja mofulumira anatenga zofunda zawo naziyala pansi pa makwerero kuti Yehu akhalepo. Kenaka analiza lipenga, nafuwula kuti, “Yehu ndiye mfumu!”
14 这样,宁示的孙子、约沙法的儿子耶户背叛约兰。先是约兰和以色列众人因为亚兰王哈薛的缘故,把守基列的拉末;
Choncho Yehu mwana wa Yehosafati, mwana wa Nimisi, anachitira chiwembu Yoramu. (Nthawi imeneyi nʼkuti Yoramu ndi Aisraeli onse akuteteza Ramoti Giliyadi kwa Hazaeli mfumu ya ku Aramu,
15 但约兰王回到耶斯列,医治与亚兰王哈薛打仗所受的伤。耶户说:“若合你们的意思,就不容人逃出城往耶斯列报信去。”
koma nʼkuti Yoramu atabwerera ku Yezireeli kuti akachire mabala amene Aaramu anamuvulaza pa nkhondo ndi Hazaeli mfumu ya ku Aramu.) Yehu anati, “Ngati mukugwirizana nazo zimenezi, wina aliyense asatuluke mu mzinda muno kupita kukafotokoza nkhaniyi ku Yezireeli.”
16 于是耶户坐车往耶斯列去,因为约兰病卧在那里。犹大王亚哈谢已经下去看望他。
Pamenepo Yehu anakwera galeta lake, napita ku Yezireeli, chifukwa Yoramu anali akupumula kumeneko ndipo Ahaziya, mfumu ya ku Yuda, nʼkuti ali komweko kudzamuona.
17 有一个守望的人站在耶斯列的楼上,看见耶户带着一群人来,就说:“我看见一群人。”约兰说:“打发一个骑马的去迎接他们,问说:平安不平安?”
Mlonda amene ankayimirira pa nsanja yolondera mzinda wa Yezireeli ataona gulu lankhondo la Yehu likuyandikira, anafuwula kuti, “Ndikuona gulu lankhondo likubwera.” Yoramu analamula kuti, “Peza munthu wokwera kavalo, mutume kuti akakumane nawo ndi kuwafunsa kuti, ‘Kodi mukubwera mwamtendere?’”
18 骑马的就去迎接耶户,说:“王问说,平安不平安?”耶户说:“平安不平安与你何干?你转在我后头吧!”守望的人又说:“使者到了他们那里,却不回来。”
Choncho munthu wokwera kavalo anapita kukakumana ndi Yehu ndipo anati, “Mfumu ikufunsa kuti, ‘Kodi mukubwera mwamtendere?’” Yehu anayankha kuti, “Kodi iwe nkhani ya mtendere yakukhudza bwanji? Tiye, zinditsata pambuyo panga.” Mlonda uja anakafotokoza kwa mfumu kuti, “Wamthenga uja wakafika kwa anthuwo koma sakubwerera.”
19 王又打发一个骑马的去。这人到了他们那里,说:“王问说,平安不平安?”耶户说:“平安不平安与你何干?你转在我后头吧!”
Choncho mfumu inatumanso munthu wina wachiwiri wokwera kavalo. Atafika kwa anthuwo iye anati, “Mfumu ikufunsa kuti, ‘Kodi mukubwera mwamtendere?’” Yehu anayankha kuti, “Kodi iwe nkhani ya mtendere yakukhudza bwanji? Tiye, zinditsata pambuyo panga.”
20 守望的人又说:“他到了他们那里,也不回来;车赶得甚猛,像宁示的孙子耶户的赶法。”
Mlonda uja anakanenanso kuti, “Wamthenga uja wakafika kwa anthuwo koma sakubwereranso. Kuyendako kukukhala ngati kwa Yehu mwana wa Nimisi, iye amayenda ngati munthu wamisala.”
21 约兰吩咐说:“套车!”人就给他套车。以色列王约兰和犹大王亚哈谢各坐自己的车出去迎接耶户,在耶斯列人拿伯的田那里遇见他。
Yoramu analamula kuti, “Konzani galeta langa.” Ndipo atakonza galeta lake, Yoramu mfumu ya Israeli ndi Ahaziya mfumu ya ku Yuda anakwera nʼkutuluka mu mzindamo, aliyense atakwera galeta lake, kukakumana ndi Yehu. Iwo anakumana ndi Yehu pa munda umene unali wa Naboti, wa ku Yezireeli.
22 约兰见耶户就说:“耶户啊,平安吗?”耶户说:“你母亲耶洗别的淫行邪术这样多,焉能平安呢?”
Yoramu ataona Yehu anafunsa kuti, “Yehu, kodi wabwera mwamtendere?” Yehu anayankha kuti, “Pangakhale bwanji mtendere pamene zopembedza mafano zonse zilipo ndiponso ufiti wa amayi ako Yezebeli uli ponseponse?”
23 约兰就转车逃跑,对亚哈谢说:“亚哈谢啊,反了!”
Yoramu anatembenuka, nathawa akufuwula kwa Ahaziya kuti, “Ahaziya, anthuwa atiwukira!”
24 耶户开满了弓,射中约兰的脊背,箭从心窝穿出,约兰就仆倒在车上。
Pamenepo Yehu anakoka uta wake ndipo analasa Yoramu kumsana pakati pa mapewa. Muviwo unakalasa mtima wake ndipo anagwa pansi mʼgaleta lakelo.
25 耶户对他的军长毕甲说:“你把他抛在耶斯列人拿伯的田间。你当追想,你我一同坐车跟随他父亚哈的时候,耶和华对亚哈所说的预言,
Yehu anawuza Bidikara, mtsogoleri wa galeta lake kuti, “Munyamule ndipo ukamuponye mʼmunda umene unali wa Naboti wa ku Yezireeli, chifukwa kumbukira mmene iwe ndi ine tinkayenda pambuyo pa Ahabu abambo ake, kuti Yehova ananeneratu za iye kuti,
26 说:‘我昨日看见拿伯的血和他众子的血,我必在这块田上报应你。’这是耶和华说的,现在你要照着耶和华的话,把他抛在这田间。”
‘Zoonadi dzulo ndinaona magazi a Naboti ndi magazi a ana ake, akutero Yehova, ndipo Ine ndidzakubwezera ndithu choyipa chimenechi pa munda womwe uno, akutero Yehova.’ Tsono munyamule ndipo ukamuponye mʼmundamo, potsatira zimene Yehova ananena.”
27 犹大王亚哈谢见这光景,就从园亭之路逃跑。耶户追赶他,说:“把这人也杀在车上。”到了靠近以伯莲姑珥的坡上击伤了他。他逃到米吉多,就死在那里。
Ahaziya mfumu ya ku Yuda ataona zimene zinachitika, anathawira ku Beti Hagani. Yehu anamuthamangitsa, uku akufuwula kuti, “Mupheninso!” Iwo anamuvulaza ali mʼgaleta lakelo pa njira yopita ku Guri pafupi ndi Ibuleamu, koma iye anathawira ku Megido ndipo anakafera kumeneko.
28 他的臣仆用车将他的尸首送到耶路撒冷,葬在大卫城他自己的坟墓里,与他列祖同葬。
Antchito ake anamunyamulira mʼgaleta kupita naye ku Yerusalemu ndipo anamuyika mʼmanda pamodzi ndi makolo ake mu mzinda wa Davide.
29 亚哈谢登基作犹大王的时候,是在亚哈的儿子约兰第十一年。
(Mʼchaka cha khumi ndi chimodzi cha ufumu wa Yoramu mwana wa Ahabu, Ahaziya anakhala mfumu ya ku Yuda).
30 耶户到了耶斯列;耶洗别听见就擦粉、梳头,从窗户里往外观看。
Kenaka Yehu anapita ku Yezireeli. Yezebeli atamva zimene zinachitika, anapaka zodzikometsera mʼmaso, naluka tsitsi lake, namasuzumira pa zenera.
31 耶户进门的时候,耶洗别说:“杀主人的心利啊,平安吗?”
Pamene Yehu ankalowa pa chipata iye anafunsa kuti, “Kodi wabwera mwamtendere, iwe Zimuri, munthu wopha mbuye wako?”
32 耶户抬头向窗户观看,说:“谁顺从我?”有两三个太监从窗户往外看他。
Yehu anakweza maso nayangʼana pa zenera, ndipo anafuwula kuti, “Kodi ndani ali mbali yanga? Ndani?” Anthu ofulidwa awiri kapena atatu anayangʼana Yehu pansipo.
33 耶户说:“把她扔下来!”他们就把她扔下来。她的血溅在墙上和马上;于是把她践踏了。
Yehu anawawuza kuti, “Muponyeni pansi!” Motero anamuponya pansi ndipo magazi ake ena anafalikira pa khoma ndi pa akavalo pamene ankamupondaponda.
34 耶户进去,吃了喝了,吩咐说:“你们把这被咒诅的妇人葬埋了,因为她是王的女儿。”
Yehu analowa mʼnyumba yaufumu ndipo anadya ndi kumwa. Kenaka iye anati, “Kamutoleni mkazi wotembereredwayo, ndipo kamuyikeni mʼmanda, popeza ndi mwana wa mfumu.”
35 他们就去葬埋她,只寻得她的头骨和脚,并手掌。
Koma atapita kuti akamuyike mʼmanda, sanapeze kanthu kupatula chibade cha mutu wokha, mapazi ake ndi manja ake.
36 他们回去告诉耶户,耶户说:“这正应验耶和华借他仆人提斯比人以利亚所说的话,说:‘在耶斯列田间,狗必吃耶洗别的肉;
Choncho iwo anabwerera kwa Yehu ndi kukamufotokozera kuti, “Mawu amene Yehova anayankhula kudzera mwa mtumiki wake Eliya wa ku Tisibe ndi awa: Pa munda wa ku Yezireeli agalu adzadya mtembo wa Yezebeli.
37 耶洗别的尸首必在耶斯列田间如同粪土,甚至人不能说这是耶洗别。’”
Mtembo wa Yezebeli udzakhala ngati zinyalala pa munda wa ku Yezireeli, kotero kuti palibe amene adzathe kunena kuti, ‘Uyu ndi Yezebeli.’”

< 列王纪下 9 >