< 列王纪下 5 >
1 亚兰王的元帅乃缦在他主人面前为尊为大,因耶和华曾借他使亚兰人得胜;他又是大能的勇士,只是长了大麻风。
Tsono Naamani anali mtsogoleri wa gulu lankhondo a mfumu ya ku Aramu. Iye anali munthu wodalirika pamaso pa mbuye wake ndipo anali wokondedwa kwambiri, chifukwa kudzera mwa iye Yehova anapambanitsa Aaramu. Anali msilikali wolimba mtima, koma anali ndi khate.
2 先前亚兰人成群地出去,从以色列国掳了一个小女子,这女子就服事乃缦的妻。
Tsono magulu a Aaramu anapita ku nkhondo ndipo anakagwira ukapolo mtsikana wamngʼono wa ku Israeli, ndipo ankatumikira mkazi wa Naamani.
3 她对主母说:“巴不得我主人去见撒马利亚的先知,必能治好他的大麻风。”
Mtsikanayo anawuza mkazi wa Naamani kuti, “Mbuye wanga akanapita kukaonana ndi mneneri amene amakhala ku Samariya, akanachiritsidwa khate lawo.”
4 乃缦进去,告诉他主人说,以色列国的女子如此如此说。
Naamani anapita kwa mbuye wake kukamuwuza zomwe mtsikana wochokera ku Israeli ananena.
5 亚兰王说:“你可以去,我也达信于以色列王。”于是乃缦带银子十他连得,金子六千舍客勒,衣裳十套,就去了;
Mfumu ya ku Aramu inayankha kuti, “Iwe uyenera kupita. Ine ndilembera kalata mfumu ya ku Israeli.” Choncho Naamani ananyamuka kupita ku Samariya, atatenga ndalama za siliva 30,000, ndalama zagolide 6,000 ndiponso zovala khumi za pa chikondwerero.
6 且带信给以色列王,信上说:“我打发臣仆乃缦去见你,你接到这信,就要治好他的大麻风。”
Kalata imene anapita nayo kwa mfumu ya ku Israeli inali ndi mawu awa: “Taonani, ndikutumiza Naamani mtumiki wanga pamodzi ndi kalatayi kwa inu kuti mumuchiritse khate lake.”
7 以色列王看了信就撕裂衣服,说:“我岂是 神,能使人死使人活呢?这人竟打发人来,叫我治好他的大麻风。你们看一看,这人何以寻隙攻击我呢?”
Mfumu ya ku Israeli itangowerenga kalatayo, inangʼamba mkanjo wake ndipo inati, “Kodi ine ndine Mulungu? Kodi ndingathe kupha kapena kupereka moyo? Chifukwa chiyani munthu ameneyu wanditumizira munthu woti ndimuchiritse khate lake? Taonani, iyeyu akungofuna kuti apeze chifukwa choyambanirana nane!”
8 神人以利沙听见以色列王撕裂衣服,就打发人去见王,说:“你为什么撕了衣服呢?可使那人到我这里来,他就知道以色列中有先知了。”
Elisa munthu wa Mulungu atamva kuti mfumu ya ku Israeli yangʼamba mkanjo wake, anatumiza uthenga uwu: “Chifukwa chiyani mwangʼamba mkanjo wanu? Mutumizeni munthuyo kwa ine ndipo iyeyo adzadziwa kuti muli mneneri mu Israeli.”
Choncho Naamani anapita pamodzi ndi akavalo ake ndi magaleta nakayima pa khomo la nyumba ya Elisa.
10 以利沙打发一个使者,对乃缦说:“你去在约旦河中沐浴七回,你的肉就必复原,而得洁净。”
Elisa anatumiza uthenga kwa iye woti, “Pita, kasambe kasanu ndi kawiri mu mtsinje wa Yorodani, thupi lako lidzachira ndi kukhalanso monga kale ndipo udzayeretsedwa.”
11 乃缦却发怒走了,说:“我想他必定出来见我,站着求告耶和华—他 神的名,在患处以上摇手,治好这大麻风。
Koma Naamani anachoka mokwiya ndipo anati, “Ine ndimaganiza kuti munthuyu atuluka ndipo ayimirira nayitana dzina la Yehova Mulungu wake, nayendetsa dzanja lake pamwamba pa nthendayi ndi kundichiritsa khate langa.
12 大马士革的河亚罢拿和法珥法岂不比以色列的一切水更好吗?我在那里沐浴不得洁净吗?”于是气忿忿地转身去了。
Kodi Abana ndi Faripara, mitsinje ya ku Damasiko, siyoposa mitsinje ina yonse ya ku Israeli? Kodi sindikanasamba mʼmitsinje imeneyo ndi kuyeretsedwa?” Kotero anatembenuka nachoka ali wokwiya kwambiri.
13 他的仆人进前来,对他说:“我父啊,先知若吩咐你做一件大事,你岂不做吗?何况说你去沐浴而得洁净呢?”
Antchito ake anamuyandikira namufunsa kuti, “Abambo anga, mneneri akanakulamulani chinthu chachikulu, kodi inu simukanachita? Nanga nʼzovuta motani zomwe mneneri wanena kuti ‘Kasambeni ndipo mudzayeretsedwa!’”
14 于是乃缦下去,照着神人的话,在约旦河里沐浴七回;他的肉复原,好像小孩子的肉,他就洁净了。
Choncho Naamani anapita ku Yorodani nakadzimiza mʼmadzimo kasanu nʼkawiri, monga momwe munthu wa Mulungu anamuwuzira. Thupi lake linakhalanso monga kale ndipo linakhala losalala ngati la kamnyamata.
15 乃缦带着一切跟随他的人,回到神人那里,站在他面前,说:“如今我知道,除了以色列之外,普天下没有 神。现在求你收点仆人的礼物。”
Pamenepo Naamani ndi atumiki ake onse anabwerera kwa munthu wa Mulungu uja. Naamani anayima pamaso pa Elisa ndipo anati, “Tsopano ndikudziwa kuti kulibe Mulungu wina pa dziko lonse lapansi koma mu Israeli mokha. Chonde, tsopano landirani mphatso ya mtumiki wanu.”
16 以利沙说:“我指着所事奉永生的耶和华起誓,我必不受。”乃缦再三地求他,他却不受。
Mneneri anayankha kuti, “Pali Yehova wamoyo, amene ine ndimamutumikira, sindidzalandira zimenezi.” Ndipo ngakhale Naamani anamukakamiza, iye anakanabe.
17 乃缦说:“你若不肯受,请将两骡子驮的土赐给仆人。从今以后,仆人必不再将燔祭或平安祭献与别神,只献给耶和华。
Naamani anati, “Ngati inu simulandira, chonde lolani mtumiki wanu kuti atengeko dothi lokwanira kunyamula abulu awiri, popeza mtumiki wanu sadzaperekanso nsembe yopsereza ndi nsembe zina kwa mulungu wina koma Yehova.
18 惟有一件事,愿耶和华饶恕你仆人:我主人进临门庙叩拜的时候,我用手搀他在临门庙,我也屈身。我在临门庙屈身的这事,愿耶和华饶恕我。”
Koma Yehova andikhululukire ine pa chinthu ichi: Pamene mbuye wanga alowa mʼnyumba ya mapemphero ya Rimoni ine ndimapita naye ndipo ndimakagwada naye limodzi. Pamene ndikugwada mʼnyumba ya mapemphero ya Rimoni, Yehova azikhululukira mtumiki wanu pa chinthu chimenechi.”
19 以利沙对他说:“你可以平平安安地回去!” 乃缦就离开他去了;走了不远,
Elisa anati, “Pita mu mtendere.” Choncho anachoka nayenda pangʼono.
20 神人以利沙的仆人基哈西心里说:“我主人不愿从这亚兰人乃缦手里受他带来的礼物,我指着永生的耶和华起誓,我必跑去追上他,向他要些。”
Koma Gehazi, mtumiki wa Elisa munthu wa Mulungu, anaganiza mu mtima mwake kuti, “Taonani, mbuye wanga wamulekerera Naamani Mwaramuyu, posalandira zomwe anabweretsa. Pali Yehova wamoyo, ine ndimuthamangira ndipo ndikatengako zinthu kwa iye.”
21 于是基哈西追赶乃缦。乃缦看见有人追赶,就急忙下车迎着他,说:“都平安吗?”
Choncho Gehazi anamuthamangira Naamani uja. Naamani ataona Gehazi akumuthamangira, anatsika mʼgaleta lake ndi kukakumana naye. Iye anafunsa Gehazi kuti, “Kodi nʼkwabwino?”
22 说:“都平安。我主人打发我来说:‘刚才有两个少年人,是先知门徒,从以法莲山地来见我,请你赐他们一他连得银子,两套衣裳。’”
Gehazi anayankha kuti, “Inde nʼkwabwino. Mbuye wanga wandituma kuti ndidzakuwuzeni kuti, ‘Anyamata awiri mwa ana a aneneri angondipeza kumene kuchokera ku dziko la mapiri la Efereimu. Chonde apatseniko ndalama za siliva 3,000 ndi zovala ziwiri za pa phwando.’”
23 乃缦说:“请受二他连得”;再三地请受,便将二他连得银子装在两个口袋里,又将两套衣裳交给两个仆人;他们就在基哈西前头抬着走。
Naamani anati, “Kuli bwino utenge ndalama zasiliva 6,000.” Iye anakakamiza Gehazi kuti alandire, ndipo kenaka anamanga matumba awiri a ndalama zasiliva pamodzi ndi zovala zinayi za pa mphwando. Naamani anazipereka kwa antchito ake awiri ndipo anazinyamula nayenda patsogolo pa Gehazi.
24 到了山冈,基哈西从他们手中接过来,放在屋里,打发他们回去。
Gehazi atafika ku phiri, anawalanda antchito aja zinthu zija nazibisa mʼnyumbamo. Iye anawawuza anthu aja kuti abwerere ndipo anapita.
25 基哈西进去,站在他主人面前。以利沙问他说:“基哈西你从哪里来?”回答说:“仆人没有往哪里去。”
Kenaka analowa mʼnyumbamo nakayima pamaso pa mbuye wake Elisa. Elisa anafunsa kuti, “Kodi Gehazi unali kuti?” Iye anayankha kuti, “Mtumiki wanu sanapite kwina kulikonse.”
26 以利沙对他说:“那人下车转回迎你的时候,我的心岂没有去呢?这岂是受银子、衣裳、买橄榄园、葡萄园、牛羊、仆婢的时候呢?
Koma Elisa anati kwa Gehazi, “Kodi mzimu wanga sunali nawe pamene munthu uja anatsika mʼgaleta lake ndi kukumana nawe? Kodi ino ndi nthawi yolandira ndalama, kapena kulandira zovala, mitengo ya olivi, minda ya mpesa, nkhosa, ngʼombe kapena antchito aamuna kapena antchito aakazi?
27 因此,乃缦的大麻风必沾染你和你的后裔,直到永远。”基哈西从以利沙面前退出去,就长了大麻风,像雪那样白。
Khate la Naamani lidzakumatirira iwe ndi zidzukulu zako mpaka muyaya.” Ndipo Gehazi anachoka pamaso pa Elisa ali ndi khate lotuwa ngati phulusa.