< 历代志下 15 >

1 神的灵感动俄德的儿子亚撒利雅。
Mzimu wa Mulungu unabwera pa Azariya mwana wa Odedi.
2 他出来迎接亚撒,对他说:“亚撒和犹大、便雅悯众人哪,要听我说:你们若顺从耶和华,耶和华必与你们同在;你们若寻求他,就必寻见;你们若离弃他,他必离弃你们。
Iye anapita kukakumana ndi Asa ndipo anati kwa iye, “Tandimverani, inu Asa ndi Ayuda onse ndi Benjamini. Yehova ali ndi inu, inunso mukakhala naye. Ngati inu mumufunafuna Iye mudzamupeza, koma ngati mumusiya, Iye adzakusiyani.
3 以色列人不信真神,没有训诲的祭司,也没有律法,已经好久了;
Kwa nthawi yayitali Israeli anali wopanda Mulungu weniweni, wopanda wansembe wophunzitsa ndi wopanda malamulo.
4 但他们在急难的时候归向耶和华—以色列的 神,寻求他,他就被他们寻见。
Koma pamene anali pa mavuto anatembenukira kwa Yehova, Mulungu wa Israeli ndi kufunafuna Iye, ndipo anamupeza.
5 那时,出入的人不得平安,列国的居民都遭大乱;
Masiku amenewo sikunali kwabwino kuyenda ulendo, pakuti anthu onse okhala mʼdziko anali pa mavuto aakulu.
6 这国攻击那国,这城攻击那城,互相破坏,因为 神用各样灾难扰乱他们。
Mtundu umodzi umakanthidwa ndi mtundu wina ndipo mzinda wina umakanthidwa ndi mzinda wina, pakuti Mulungu amawasautsa ndi mazunzo a mtundu uliwonse.
7 现在你们要刚强,不要手软,因你们所行的必得赏赐。”
Koma inu, khalani amphamvu ndipo musataye mtima, pakuti mudzalandira mphotho ya ntchito yanu.”
8 亚撒听见这话和俄德儿子先知亚撒利雅的预言,就壮起胆来,在犹大、便雅悯全地,并以法莲山地所夺的各城,将可憎之物尽都除掉,又在耶和华殿的廊前重新修筑耶和华的坛;
Asa atamva mawu awa ndiponso uneneri wa Azariya mwana wa Odedi, analimba mtima. Iye anachotsa mafano onse onyansa mʼdziko lonse la Yuda ndi Benjamini ndi mʼmizinda yonse imene analanda a ku mapiri a Efereimu. Iye anakonzetsa guwa lansembe la Yehova limene linali kutsogolo kwa khonde la Nyumba ya Mulungu.
9 又招聚犹大、便雅悯的众人,并他们中间寄居的以法莲人、玛拿西人、西缅人。有许多以色列人归降亚撒,因见耶和华—他的 神与他同在。
Kenaka anasonkhanitsa anthu onse a ku Yuda ndi Benjamini ndiponso anthu ochokera ku Efereimu, Manase ndi Simeoni amene ankakhala pakati pawo, pakuti gulu lalikulu linabwera kwa iye kuchokera ku Israeli litaona kuti anali ndi Yehova Mulungu wake.
10 亚撒十五年三月,他们都聚集在耶路撒冷。
Iwo anasonkhana mu Yerusalemu mwezi wachitatu wa chaka cha 15 cha ulamuliro wa Asa.
11 当日他们从所取的掳物中,将牛七百只、羊七千只献给耶和华。
Pa nthawi imeneyi anapereka nsembe kwa Yehova, ngʼombe 700 ndiponso nkhosa ndi mbuzi 7,000 zochokera pa zolanda ku nkhondo zimene anabweretsa.
12 他们就立约,要尽心尽性地寻求耶和华—他们列祖的 神。
Iwo anachita pangano loti azifunafuna Yehova, Mulungu wa makolo awo, ndi mtima ndi moyo wawo wonse.
13 凡不寻求耶和华—以色列 神的,无论大小、男女,必被治死。
Aliyense wosafunafuna Yehova Mulungu wa Israeli aziphedwa, kaya ndi wamngʼono kapena wamkulu, mwamuna kapena mkazi.
14 他们就大声欢呼,吹号吹角,向耶和华起誓。
Iwo analumbira kwa Yehova, mokweza mawu, akuyimba malipenga ndi mbetete.
15 犹大众人为所起的誓欢喜;因他们是尽心起誓,尽意寻求耶和华,耶和华就被他们寻见,且赐他们四境平安。
Anthu onse a ku Yuda anakondwera pa kulumbirako chifukwa analumbira ndi mtima wawo wonse. Iwo anafunafuna Mulungu mwachidwi, ndipo anamupeza Iye. Kotero Yehova anawapatsa mpumulo mbali zonse.
16 亚撒王贬了他祖母玛迦太后的位,因她造了可憎的偶像亚舍拉。亚撒砍下她的偶像,捣得粉碎,烧在汲沦溪边。
Mfumu Asa anachotsanso Maaka agogo ake pa udindo wa amayi a mfumu chifukwa anapanga fano lonyansa la Asera. Asa anagwetsa fanolo, naliswa ndipo kenaka anakaliwotcha ku chigwa cha Kidroni.
17 只是邱坛还没有从以色列中废去,然而亚撒的心一生诚实。
Ngakhale kuti sanachotse malo opembedzerako mafano mu Israeli, mtima wa Asa unali wodzipereka kwathunthu kwa Yehova, masiku onse a moyo wake.
18 亚撒将他父所分别为圣、与自己所分别为圣的金银和器皿都奉到 神的殿里。
Iye anabweretsanso mʼNyumba ya Mulungu zipangizo zasiliva, golide ndi ziwiya zina zimene iyeyo ndi abambo ake anazipatula.
19 从这时直到亚撒三十五年,都没有争战的事。
Panalibenso nkhondo mpaka chaka cha 35 cha ufumu wa Asa.

< 历代志下 15 >